Kumamatira ku Nthaŵi za Msonkhano
1 Kusonkhana pamodzi mokhazikika pa misonkhano ya mpingo kuli kakonzedwe kachikondi kochokera kwa Yehova. Ulinso mwaŵi umene tiyenera kukondwera nawo nthaŵi zonse. Komabe, tauzidwa kuti, m’mipingo ina, misonkhano imasinthidwa ndipo nthaŵi zina imachotsedwa kuti papezeke mpata wochita zosangulutsa kapena chinthu china. Kodi zimenezi nzoyenera? Kodi zimasonyeza chiyamikiro chakuya kaamba ka kakonzedwe kameneka kochokera kwa Yehova Mulungu?
2 Misonkhano ya mpingo imapanga mbali yofunika ya kulambira koona. Tikulamulidwa ndi Yehova kusonkhana pamodzi pa maziko okhazikika. (Aheb. 10:24, 25) Pamene nthaŵi za msonkhano za mpingo zakhazikitsidwa, ziyenera kumamatiridwa. Sitiyenera konse kusintha msonkhano kapena kusauchita chifukwa cha zochitika zosangulutsa zilizonse, ukwati kapena maliro. Zochitika zina ziyenera kulinganizidwa pa nthaŵi zina osati nthaŵi zimene mpingo unalinganiza kaamba ka kulambira kwa mpingo. Ngati, chifukwa cha mikhalidwe ina, palibe akulu okamba nkhani yapoyera kapena kuchititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda, mtumiki wotumikira wokhoza akhoza kugwirizira. Mulimonse mmene zingakhalire, Phunziro la Nsanja ya Olonda liyenera kuchitidwa kaamba ka phindu la ziŵalo zotsala za mpingo ndi okondwerera.—1 Akor. 14:40.
3 Mkati mwa mlungu wa Chikumbutso ndi pamene misonkhano yachigawo ikuchitidwa, kaŵirikaŵiri Bungwe Lolamulira limapereka chitsogozo ponena za misonkhano, kaya iyenera kusinthidwa kapena kusachitidwa. Iwo aperekanso chitsogozo chakuti pamene tsiku la msonkhano wapadera lindandalikidwa kukhala Loŵeruka, misonkhano ya pa Sande iyenera kuchitidwa monga nthaŵi zonse. Ngati ukhala pa Sande, chidule cha Phunziro la Nsanja ya Olonda chidzaperekedwa pa msonkhano wa tsiku limodzi kaamba ka phindu la onse opezekapo. Mipingo iyenera kumamatira thithithi ku chitsogozo chotero chochokera ku Bungwe Lolamulira ponena za misonkhano yochitidwa mkati mwa nyengo zimenezo.
4 Chotero, tiyeni tipitirize kukhala ndi lingaliro losamalitsa la nthaŵi za misonkhano yathu ndi kumamatira zolimba ku izo. Koposa zonse, tiyeni tifike nthaŵi zonse pa misonkhano yathu kuti ‘tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino monga momwe tiona tsiku lilikuyandika.’—Aheb. 10:24, 25.