Malo a Achichepere m’Chitaganya Chachikristu
1 Anthu ambiri lerolino ali oyedzamira pa kunyalanyaza kapena kupatula achichepere, akumaŵaona kukhala osafunikira chisamaliro kapena kudera nkhaŵa. Buku la Achichepere Akufunsa limasanthula mwakuya mmene Mlengi wathu, Yehova Mulungu, ndi Mwana wake, Yesu Kristu, amaonera achichepere. Kodi tingathandize motani anthu oona mtima amene asonyeza kufunitsitsa kumvetsera? Mwa kupanga maulendo obwereza. Pamene tibwerera, nthaŵi zonse kumakhala bwino kukhala ndi chinachake chotsimikizirika m’maganizo chokanena chimene chidzathandiza anthu kuona lingaliro la Yehova la achichepere.
2 Ngati munthuyo anasonyeza chikondwerero m’mfundo zimene munakambitsirana naye kuchokera m’buku la “Achichepere Akufunsa,” mayambidwe awa angakhale okhutiritsa kuyambitsira kukambitsirana kwanu:
◼ “Kale, anthu ambiri anali kuŵerenga Baibulo. Koma tikukhala m’nthaŵi imene mikhalidwe ya maganizo ikusintha. Kodi mukuganiza bwanji pa zimenezi? Kodi mumakhulupirira kuti Baibulo lili ndi zambiri zonena kwa anthu achichepere? [Ŵerengani Aefeso 6:1-3 ndi kudikira ndemanga.] Ndipo pamene kuli kwakuti chitaganya cha anthu chasintha kwambiri chiyambire nthaŵi za Baibulo, zilakolako za unyamata zasintha pang’ono. Motero Baibulo lidakali latsopano monga kale. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:16.] Komabe, kupyolera m’buku la Achichepere Akufunsa, tayesayesa kupereka uphungu wa Baibulo m’njira yakuti achichepere samaona ngati kuti akulalikiridwa, koma, mmalo mwake, kukambitsirana nawo.”
3 Mungayambe kukambitsirana kwanu ndi zonga zotsatirazi:
◼ “Pa ulendo wanga wapitawo, panafunsidwa funso lakuti, Kodi mtsogolo mwa munthu ndi dziko lapansi nchiyani? Taonani mmene buku limene ndinakusiyirani likuyankhira funso limenelo.” Tsegulani mutu 38 wa buku la Achichepere Akufunsa ndi kumulimbikitsa kuŵerenga ndime 2 patsamba 307. Ndiyeno, mungafunse kuti: “Kodi ndi kusintha kwakukulu kotani, kumene mukuganiza kuti kudzachitika padziko lapansi?” Ngati nkoyenerera, mfundo imeneyi ingakambitsiridwe panthaŵiyo kapena pa ulendo wanu wotsatira mwa kupitiriza m’ndime zina m’mutu umodzimodziwo wa buku la Achichepere Akufunsa.
4 Ngati mwininyumba anaonekera kukhala wopembedza, mungafunse kuti:
◼ “Kodi mwaona kuti anthu ambiri lerolino, mosasamala kanthu kuti ndi a chipembedzo chiti, ali okondweretsedwa ndi mmene tingalimbanirane bwinopo ndi mavuto a moyo wa banja? Tonsefe timayesayesa kuchita zabwino koposa zomwe tingathe, koma ngati pali chinachake chimene chingatithandize kukhala ndi chipambano chachikulu kwambiri, timakondwera, kodi sichoncho?” Dikirani ndemanga. Ndiyeno ŵerengani Akolose 3:12, 18-21. Pambuyo poŵerenga lembalo, mwininyumba angafotokoze malingaliro ake. Ndiyeno mungasumike chidwi pa mfundo yakutiyakuti kapena ziŵiri za m’mutu 2 wa buku la Achichepere Akufunsa.
5 Njira ina imene mungayambire ulendo wobwereza ndi mwa kunena kuti:
◼ “Kodi munayamba mwadabwa kuti, Kodi Mulungu amasamaliradi za chisalungamo ndi kuvutika kumene anthu akukumana nako? [Dikirani ndemanga.] Mokondweretsa, Baibulo limasonyeza kuti mikhalidwe imeneyi idzatha. [Tsegulani tsamba 307, ndi kuŵerenga Chivumbulutso 11:18.] Awo amene amamzindikira monga Mpangi wawo ndi kuchita chifuniro chake angayembekezere madalitso abwino koposa.”
6 Ofalitsa ozoloŵera afika pa kudziŵa kuti nkwabwino koposa kundandalika nthaŵi zokhazikika za maulendo obwereza. Kukhala ndi makonzedwe otsimikizirika a ntchito imeneyi kudzatithandiza kulondola chikondwerero mwamsanga. Sankhani nthaŵi imene ili yabwino koposa kwa inu ndi anthu okhala m’gawo. Mwa kukhala kwanu ndi phande mokhazikika m’ntchito imeneyi, mudzapeza chimwemwe m’kukwaniritsa ntchito ya “kupanga ophunzira.”—Mat. 28:19, 20, NW.