Misonkhano Yautumiki ya June
Mlungu Woyambira June 6
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu zokhudza malowo. Mwachidule sonyezani mmene magazini atsopano angagaŵidwire kunyumba ndi nyumba kumapeto a mlungu uno. Kumbutsani omvetsera kuwombola makope a buku lakuti Achichepere Akufunsa logwiritsira ntchito mu utumiki kumapeto a mlungu uno.
Mph. 20: “Kodi Mukufesa Mooloŵa Manja?” Mafunso ndi mayankho. Pamene nthaŵi ilola, pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zaumwini zosonyeza mmene achitira kuyesayesa m’mbali ina ya utumiki wawo ndipo adalitsidwa nako.
Mph. 15: “Kuthandiza Achichepere Kupeŵa Zisonkhezero Zoipa.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene malingaliro operekedwa angagwiritsidwire ntchito.
Nyimbo Na. 30 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 13
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Ŵerengani lipoti la maakaunti ndi ziyamikiro za zopereka za ku Sosaite. Phatikizanipo ndemanga zachidule zosonyeza mmene munthu wa mzimu wopatsa amadalitsidwira.—Miy. 11:24a.
Mph. 15: “Malo a Achichepere m’Chitaganya Chachikristu.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Pamene nthaŵi ilola, khalani ndi wofalitsa wokhoza achitire chitsanzo umodzi wa maulendo obwereza osonyezedwawo.
Mph. 20: “Phunziro Labuku Lampingo Limachirikiza Zochita Zophunzitsa.” Wochititsa phunziro labuku lampingo akambitsirana ndi omvetsera. Gogomezerani mmene nkhaniyo imalimbikitsira (1) kupezeka paphunziro labuku kowonjezereka, (2) kuyankha kowonjezereka paphunzirolo, ndi (3) kuchirikiza kwabwino misonkhano yokonzekera utumiki.
Nyimbo Na. 65 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 20
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Kambitsiranani mbali yakuti “Chikumbutso pa Kuchitira Lipoti Nthaŵi ya Utumiki Wakumunda Mochedwa ndi Molongosoka.”
Mph. 10: Zosoŵa za pamalopo. Kapena kambani nkhani yakuti “Kodi Ndiyenera Kusankha Ntchito Yophunziridwa Yotani?” yochokera mu Achichepere Akufunsa, masamba 174-9.
Mph. 10: “Kumamatira ku Nthaŵi za Msonkhano.” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 15: “Kodi Mukuchita Chifuniro cha Mulungu?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya March 1, 1994, masamba 28-30.
Nyimbo Na. 223 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 27
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Fotokozani makonzedwe a utumiki wakumunda pamapeto a mlungu wa holide ya kudziko.
Mph. 15: “Misonkhano Yatanthauzo Yokonzekera Utumiki Wakumunda.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho ya woyang’anira utumiki. Pokambitsirana ndime 3, tchulani mawu oyamba amodzi kapena aŵiri a m’buku la Kukambitsirana amene angagwiritsiridwe ntchito kumapeto a mlungu uno. Pandime 5 tchulani vuto lililonse lokhudza mkhalidwe pamene tili mu utumiki wakumunda umene waonedwa pampingopo; perekani mokoma mtima malingaliro a kuwongolera.
Mph. 20: Pendani Chogaŵira cha July. Chogaŵira: Mabrosha akuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century. Mipingo yokhalabe ndi timabuku ta masamba 32 iyenera kutigaŵira m’munda. Mabrosha ameneŵa ali othandiza kuyambitsira maphunziro a Baibulo. Pendani mbali zosangalatsa ndi zithunzithunzi zimene zingagwiritsiridwe ntchito kuyambitsa makambitsirano. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene mungayambire makambitsirano a nkhani ya Baibulo. (Gwiritsirani ntchito malingaliro a m’buku la Kukambitsirana pa “Mtsogolo/ Chisungiko” patsamba 12 ndi “Ufumu” patsamba 13.) Zitsanzo ziyenera kumalizidwa ndi kupangana za kuyamba phunziro la Baibulo.
Nyimbo Na. 118 ndi pemphero lomaliza.