Kuthandiza Banja Lathu la Chikhulupiriro mu Bosnia
MBONI ZA YEHOVA sizimakhala ndi phande m’mikangano ya ndale. (Yohane 17:16) Komabe, potsatira uphungu wa Paulo wakuchitira chokoma “makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro,” zimapereka chithandizo mwamsanga kwa Akristu anzawo okhala m’madera osakazidwa ndi nkhondo. (Agalatiya 6:10) Pamene nyengo yozizira ya 1993-94 inayandikira, Mboni za ku Austria ndi Croatia zinaika miyoyo yawo pachiswe kuti zikathandize banja lawo la chikhulupiriro mu Bosnia. Lotsatirali ndilo lipoti lawo.
Kuyambira March kufikira October 1993, panalibe mpata wotumizira mitokoma ya chithandizo ku Bosnia. Komabe, kuchiyambi kwa October, akuluakulu aboma anasonyeza kuti kungakhale kotheka kupititsa katunduyo. Imeneyi ikakhalabe ntchito yangozi, popeza kuti pakati pa magulu onse a m’Bosnia panali kumenyana kwakukulu.
Komabe, pa Lachiŵiri, October 26, 1993, malole athu ananyamuka ku Vienna atanyamula matani 16 a chakudya ndi nkhuni za Akristu anzathu mu Bosnia. Tinavala mabaji athu a msonkhano wachigawo kuti tidziŵidwe.
Titafika pamalire a Croatia ndi Bosnia, tinaperekezedwa kumsasa wa asilikali kumene malole athu anafufuzidwa kwambiri. Pempho lathu la kudutsa dera la Serbia linakanidwa. Tinaloledwa kudutsa kokha mwa kudzera m’chigawo chapakati cha Bosnia—pakati penipeni pa kumenyanako!
Zoyesayesa Zosaphula Kanthu?
Pamene asilikali olonda anali kutiperekeza kumalo osiyanasiyana ofufuzira, tinali kumva kuwombera kwa akasinja ndi mfuti kogonthetsa m’kutu. Mkati mwa usiku, tinadutsa m’nkhalango molondedwa ndi akasinja aŵiri ndi jipi. Malole athu anali kuyenda pang’onopang’ono kupyola m’dera la nkhondolo! Zinthu zonse zinayenda bwino kufikira mmaŵa pamene mfuti zinawombedwa pamitu yathu ndipo tinakabisala kuseri kwa phiri lina. Pambuyo pa kanthaŵi kuwomberako kunalekeka, ndipo tinapitiriza ulendo wathu.
Pamene tinafika pa msasa wina, ofesala wamkulu wa pamenepo anatifunsa kuti tinali ayani ndi chimene tinali kufuna. “Ntchito yanuyi siitheka,” iye anatero pamene tinamuuza chifuno chathu. “Inu mulibe mpata wa kutuluka m’malo ano, ngakhale kuyenda mamita oŵerengeka okha. M’dzikomu muli njala yaikulu kwakuti anthu adzakuukirani ndi kuba katundu wanuyu.” Anatilimbikitsa kubwerera.
Kodi zoyesayesa zathu ‘zinalephereka’? Kodi kunali kosaphula kanthu kuyembekezera kuti tikapyola m’madera osakazidwa ndi nkhondo ndi okanthidwa ndi njala ndiyeno katundu wathuyo ndi miyoyo yathu m’kupulumuka? Chosankha chachikulu chinafunika kupangidwa. Tinali titamva kale kuwombedwa kwa mfuti ndi kuphulika kwa mabomba kogonthetsa m’kutu. Pamene tinali ndi asilikali usikuwo, tinaona kuti iwo anali okonzekera kumenya nkhondo. Anavala mavesiti owatetezera ku zipolopolo ndipo ananyamula zida zambiri. Ngakhale wophika zakudya wawo anaberekera mfuti yachiwaya kumsana. Koma ife tinangovala mashati, mataye, ndi mabaji! Kodi kunali kwanzeru kwa ife kupitirizabe ulendowo?
Kufika ku Travnik
Kunaonekera ngati kuti chiyembekezo chathu chokha chinali cha kukambitsirana ndi gulu lina lachitatu m’nkhondo imeneyi. Mmaŵa tinafunsa msungwana wina ngati anadziŵa kumene tingapeze malikulu a gululo. “Si kutali,” iye anatero. “Mutangopyola mitengoyo, mudzapeza nyumba imene kale inali chipatala.” Tinafunitsitsa kupitako. Asilikaliwo anadabwa kuti tinakhoza kuchoka pamsasa wankhondo opanda zida.
Chipatala chakalecho chinali chogumuka, koma ofesala wina anali pamenepo. Iye anavomera kutithandiza, akumatilangiza kuti tikambitsirane ndi ofesala wake wamkulu choyamba. Iye anatiloŵetsa m’galimoto lake lopuwazika ndi kuliyendetsa mwaliŵiro m’mphepete mwa dera la nkhondolo. Tinaima panyumba ina pamene ofesala wamkuluyo anatilandira m’chipinda chamdima.
“Usiku wapitawo tinafuna kukuwomberani,” iye anatero. “Kodi mukufuna chiyani?”
“Ndife Mboni za Yehova, ndipo tikufuna kupereka katundu wachithandizo kwa abale athu.”
Iye anadabwadi—ndi kuchita chidwi—popeza kuti kwa milungu yambiri palibe malole alionse onyamula chithandizo amene anayesa kuloŵa m’Bosnia. Titafufuzidwa kwambiri, tinapatsidwa chilolezo cholembedwa. Usiku wapitawo tinalingalira kuti sitidzakhala ndi mpata wa kupitiriza ulendo wathu, ndipo tsopano tinakhoza kupitiriza ulendowo popanda kuperekezedwa!
Tinayendetsa malolewo m’nkhalango, tikumadutsa malo ofufuzira ambiri, ndipo nthaŵi zina tinayendetsa malole m’mbali mwa dera la nkhondo. Mosasamala kanthu za ngoziyo, tinafika bwino lomwe ku Travnik. Msilikali wina amene anamva za kufika kwathu anathamangira kunyumba imene abale athu anali kukhala. “Anthu anu afika pano ndi malole!” iye anafuula motero. Tangoganizirani chisangalalo chawo. Tinanyamula chakudyacho kuchiloŵetsa m’nyumba, ndi kukambitsirana nawo pang’ono, komano tinafunikira kupitabe patsogolo. Kunayamba kuda, ndipo ulendo wangozi wa makilomita 32 unali patsogolo pathu.
Kumka ku Zenica
Galimoto lotiperekeza linatitsogolera kupyola nkhalango paliŵiro lalikulu. Ena anati sitidzafika konse ku Zenica, koma tinafika. M’taunimo munangoti zii ngati kuti munalibe anthu. Munalibe magetsi ndipo munalibe galimoto mu msewu. Zenica anazingidwa kumbali zonse, kukumachititsa njala yaikulu ndi kuthedwa nzeru.
Pamene tinali kuyendetsa malole mu msewu, tinaona zodabwitsa—alongo aŵiri Achikristu akumachitira umboni! Tinadzauzidwa kuti, pamsonkhano wawo wa tsiku lapitalo, abale anasankha kuti iwo adzapita ku nkhalango kukafuna chakudya, popeza kuti chakudya chinali kucheperachepera. Tinangofika panthaŵi yake! Tinatsitsa katunduyo pa imodzi ya malole pa 4 koloko mmaŵa, pamene mu msewu munalibe aliyense.
Tsiku lotsatira tinaonana ndi kazembe wankhondo, amene anali wodabwa kwambiri kuti tinafika ku Zenica. Tsopano tinafunsa kuti tidziŵe za mmene tingayendere kumka kumalo athu otsatira, Sarajevo.
“Palibe aliyense amene wayesa kuloŵa mmenemo ndi lole kwa miyezi yambiri,” kazembe wankhondoyo anatero. Potsirizira pake anatipatsa chilolezo choyendera ulendowo kudutsa mapiri. “Koma kukuuzani zoona, kuyenda kwake nkovuta,” iye anachenjeza motero. “Sindidziŵa ngati malole anu akhoza kukafika kumalowo.”
Kazembeyo sanangokulitsa nkhaniyo ndi pakamwa. Pamene kunatsala makilomita 40 chabe kuti tifike ku Sarajevo, tinapatukira m’nkhalango ndi kuyenda makilomita 140! Sitidzaiŵala konse ulendo umenewu kuchokera ku Zenica kudzera ku Sarajevo kumka ku Jablanica umene unatenga usana utatu ndi usiku uŵiri, pa liŵiro la makilomita asanu pa ola. “Msewu” wake unali njira yowonongeka ndi galimoto zankhondo. Tinayendetsa malolewo m’materezi ndi m’maenje owopsa. Kaŵirikaŵiri tinayendetsa malolewo titazimitsa magetsi, ndipo panthaŵi ziŵiri malole athu anatsala pafupi kutererekera kuphompho. Lole ina ya gulu lankhondo yotsatira galimoto zathu inayatsa magetsi ake kwakanthaŵi chabe ndipo inawomberedwa nthaŵi yomweyo. Nthaŵi zina tinakonza milatho ndi kusintha matayala.
Pamene tinafika m’dera la Sarajevo, tinapempha kuti tilankhulane ndi kazembe wamkulu. Pamene tinali kuyembekezera, tinaona lole ina mu msewu itanyamula mitembo khumi ndi thumba la chiguduli la mitu ya anthu; asilikali ake anali kukambitsirana za kupereka mitemboyo—chinthu chosakondweretsadi, chikumatichititsa kukhumba tsikulo pamene nkhondo zidzatha.—Yesaya 2:4.
Potsirizira pake, pa 10:00 a.m. mmodzi wa ife anapatsidwa mwaŵi wa kulankhula ndi kazembe ndi maofesala ake akuluakulu m’chipinda chamdima, chounikiridwa ndi kandulo yokha.
“Ndinu yani kodi?” kazembeyo anafunsa motero.
“Ndife Mboni za Yehova. Tikufuna kupereka chakudya kwa Mboni zinzathu mu Sarajevo.”
“Kodi mukudziŵa kuti mu Sarajevo muli Mboni za Yehova zambiri?”
“Inde, nchifukwa chake tili kuno.”
Ndiyeno kazembeyo anatchula dzina la Mboni ina. “Kodi mumamdziŵa?”
“Inde, iyeyo ndi bwenzi lathu.”
“Nanenso ndi bwenzi langa,” kazembeyo anatero. “Tinaimbira sukulu pamodzi. Chiyambire pamene wakhala Mboni, ndimamyamikira kwambiridi. Iye wakuchitirani zambiri anthunu. Chonde tatiuzani zambiri ponena za Mboni za Yehova.”
Panali kukambitsirana kwa ola limodzi, ndipo pambuyo pake magazini ndi mabrosha oposa khumi ndi aŵiri anagaŵiridwa. Pambuyo pa kuonana kwachiŵiri, kazembeyo anavomereza kupanga makonzedwe apadera kotero kuti katundu wachithandizoyo aperekedwe kwa abale a mu Sarajevo.
Imeneyi inali ntchito yaikulu. Pafupifupi anthu 30, kuphatikizapo osakhala Mboni, ananyamula maphukusi olemera makilogalamu 27 lililonse. Iwo anagwira ntchito zolimba kuyambira pa 8:00 p.m. kufikira pa 5:00 a.m. pausiku uŵiri wosiyana—chiwonkhetso cha maola 18. Mkulu wina wampingo anasimba kuti anansi ake anachita chidwi kwambiri ndi zoyesayesa za kupereka chithandizocho kwakuti anagwada pansi ndi abale ndi kuthokoza Yehova! Zoonadi, nawonso analandirako chakudya.
Tangoganizirani chisangalalo chimene abale athu anakhala nacho pamene analandira makilogalamu pafupifupi 11,000 a katundu wachithandizo! Mkhalidwewo unali wothetsa nzeru. M’malowo, kilogalamu imodzi ya ufa watirigu ili pamtengo wa pakati pa DM450 ndi DM1,000 ($300 ndi $660, za United States). Thumba la nkhuni lili pamtengo wa pafupifupi DM400 ($260, za United States), ndipo lita ya mafuta a dizilo ili pamtengo wa DM30 ($20, za United States).
Kunali monga ngati kuti tsopano tinali kufupidwa kaamba ka ngozi iliyonse imene tinayang’anizana nayo m’njiramo. Tinali okondwa kusinkhasinkha za chisangalalo cha abale athu pamene analandira katundu ameneyu wachithandizo. Chinali chokumana nacho chimene iwo—ndi ife—sitidzaiŵala konse. Koma tsopano tinayamba kuganiza za ntchito yovuta ya kubwerera kwathu.
Kubwerera Kwathu
“Kodi tidzabwerera bwanji?” tinafunsa kazembeyo.
“Mwa njira imodzimodziyo imene mwadzera,” iye anayankha motero.
Tinali otopa, mafuta agalimoto anali ochepa, ndipo tinalibe matayala apadera. Kunayamba kuvumba mvula, ndipo sitikanatha kuyenda m’matope. Tinafunsa kazembeyo ngati tingadzere chakummwera.
“Kumeneko kuli kumenyana kwakukulu,” iye anatero. “Ngakhale mbeŵa singadutse kumeneko.” Komabe, patapita kanthaŵi, iye anasintha maganizo. “Yesani kudzerako,” iye anatero. “Ndi iko komwe, inu mwakhoza kufika kuno.”
Tinasiya lole imodzi kumbuyo ndi kuthira mafuta ake m’malole atatu. Tinanyamuka pakati pa usiku ndipo tinaloŵanso m’nkhalango ndi malolewo.
Ulendo wathu sunali wopanda mavuto. Tinapeza lole yankhondo itapikuka, itapinga pang’ono mlatho umene tinafuna kuwoloka. Tinaona kuti ngati titagulula limodzi la magudumu ake, pakakhala danga lokwanira kudzera.
Tinapempha chilolezo kwa msilikali wina wonyamula mfuti. “Kodi tingagulule gudumu limodzi ndi kulimangiriranso titawoloka pa mlathowu?”
“Mukangogwira gudumulo, mfuti yanga ilira,” msilikaliyo anayankha motero, atanenekera mfuti yakeyo.
Tinalingalira kuti kukakhala bwino kwambiri kupanga khofi ndi kupatsako msilikaliyo. Kwa maola angapo, tinamuuza za misonkhano yamitundu yonse ya 1991, monga umene unachitidwa mu Zagreb. Pambuyo pa zimenezo, mtima wake unafeŵa, ndipo anatilola kugulula gudumulo.
Ku Jablanica, mmodzi wa ife analankhula ndi mkulu wankhondo ponena za njira imene tinafuna kudzera. Iye sanakhulupirire zimene anali kumva. “Mwati mukufuna kudzera ku chigwa cha Neretva?”
Iye anayeneradi kuvutika maganizo. Dera la mapiri la chigwa cha Neretva lili ndi magulu ankhondo osiyanasiyana. Amawomberana mosalekeza. Kwa pafupifupi makilomita 16, msewuwo ndi wangozi. “Ndimo mmene ulili,” kazembeyo anatero, “ndipo inu mukufunabe kudzera kumeneko?”
Atasinkhasinkha nkhaniyo, kazembeyo ananena kuti tingathe kudzerako—koma kokha titatsagana ndi akuluakulu. Komabe, akuluakulu ameneŵa sanafune kutsagana nafe! Potsirizira pake, tinapempha kuti angodziŵitsa a mbali inayo ndi kuwauza za kudutsa kwathu. Tikadutsa popanda otiperekeza mmaŵa wotsatirawo.
Tinalemba malembo aakulu pamalole athu osonyeza kuti ndife onyamula chithandizo cha anthu. Titapemphera, tinayenda ndi malolewo m’chigwa. Tinagwirizana kuti titawomberedwa mfuti, sitidzawonjezera liŵiro ndi kuchititsa ena kutikayikira.
Tinawoloka pa mlatho kumka kumbali ina ya mtsinje ndi kupitirizabe kuyenda kudutsa chigwa chotsatira, tikumapyola nyama zakufa ndi malole ndi akasinja owonongedwa. Mwadzidzidzi tinaona mabomba otcheredwa pamsewu, akumadodometsa kudutsa kwathu. Tinaliza hutala ya lole mpaka asilikali aŵiri obisala kuseri kwa mwala anasuzumira. “Ndinu yani? Mukufunanji?” anafunsa motero.
Titadzidziŵikitsa, tinawapempha ngati angachotse mabombawo mu msewu, ndipo anavomera. Potsirizira pake, tinafika mbali inayo.
Asilikali ake kumeneko anadabwa kutiona. Iwo anatuluka pang’onopang’ono m’malo awo obisalamo, nayandikira lole mfuti zawo zitaneneketsedwa kwa ife. Tinasonyeza zikalata zathu zachilolezo pamodzi ndi manambala athu a galimoto, amene tinachotsa kuwopera kudziŵidwa pamene tinali kuyendetsa malolewo kupyola m’dera lankhondo.
“Palibe aliyense amene amakuyembekezerani,” msilikali wina anatero. “Kodi mwatha bwanji kudzera kumeneku?”
Mosiyana ndi pempho lathu, palibe aliyense wokhala pa madindiro ameneŵa amene anadziŵitsidwa kuti tinalinkudza! Ofesalayo anapitiriza kunena kuti: “Mfuti zathu zinali zachire, ndipo tinali pafupi kuyamba kuwombera.”
Tinafunsa chifukwa chake sanatero.
“Sindikudziŵa,” msilikaliyo anatero. “Ndikhulupirira kuti imeneyi inali imfa yanu. Koma pamene tinakuyang’anani ndi chiŵiya choonera patali, tinaona mawu akuti ‘chithandizo cha anthu,’ ndipo sitinadziŵe zochita nanu. Nchifukwa chake mwafika bwino lomwe.” Pambuyo pake tinapereka pemphero lochokera mu mtima lothokoza Yehova kaamba ka chitetezo chake.
Ngakhale kuti mikhalidwe yawo ili yovuta kwambiri, mzimu wa abale ndi alongo athu a ku Bosnia ngwochititsa chidwi. Amagaŵana zinthu zakuthupi zimene ali nazo ndiponso amakambitsirana mawu ambiri a chikhulupiriro ndi chilimbikitso. Mu Zenica, muli Mboni zokangalika 40, kuphatikizapo apainiya apadera 2, apainiya othandiza 11, ndi obatizidwa chatsopano 14. Mboni 65 ndi apainiya othandiza 4 amene adakali mu mzinda wa Sarajevo akuchititsa maphunziro a Baibulo 134. Mbonizo zimachita avareji ya maola 20 mwezi uliwonse akumalankhula ndi ena za mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.
Zoonadi, Mboni za Yehova zimapanga banja la padziko lonse la chikhulupiriro. Izo zimaika miyoyo yawo pachiswe mofunitsitsa kuchitira zabwino awo amene ali ogwirizana nawo m’chikhulupiriro—ngakhaledi awo amene sanayambe akumanapo nawo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amawakonda. Yesu Kristu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Ndithudi zimenezi zakhala choncho ndi banja lathu la chikhulupiriro mu Bosnia.
[Mapu/Zithunzi patsamba 24]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Adriatic Sea
AUSTRIA
SLOVENIA
HUNGARY
CROATIA
BOSNIA
Travnik
Zenica
Sarajevo
SERBIA
[Zithunzi]
Kupereka chithandizo ku Bosnia ndi Herzegovina
[Chithunzi patsamba 26]
Kudutsa pafupi ndi lole yopikuka