Chikhulupiriro Cholimba cha Abale Athu a ku Rwanda
KUCHIYAMBIYAMBI kwa 1994 dziko lonse linachita kakasi pamene mbiri ya kupululutsa anthu kowopsa inamveka kudziko la mu Afirika la Rwanda. Nkhondo yachiweniweni yankhanza inali itabuka—chotulukapo cha udani wa zaka mazana ambiri.
Poyang’anizana ndi chitaganya chosalemekeza konse lamulo ngakhale kulisunga, Mboni za Yehova zoposa 2,000 ku Rwanda zinakakamizika kuthaŵa kuti zipulumutse miyoyo yawo. Pafupifupi 1,300 zinapeza chitetezo m’misasa ya othaŵa kumaiko oyandikana nawo a Zaire ndi Tanzania, koma zina sizinakhoze kuthaŵa panthaŵi yake. Tili achisoni kunena kuti pafupifupi abale ndi alongo athu 400—achikulire ndi ana omwe, omwedi ali anthu wamba—afa m’chiwawa chankhalwe chimenecho. Akristu padziko lonse akulira maliro a osunga umphumphu olimba mtima ameneŵa ndipo akupeza chitonthozo m’lonjezo la Baibulo la chiukiriro.—Yohane 11:25.
Kodi mkhalidwe wa abale ndi alongo a ku Rwanda otsalawo wakhala wotani? Akulu anatumizidwa kuchokera kumaiko angapo kukafufuza nkhaniyo mwakudzionera okha. Lipoti lina linanena kuti abale a ku Rwandawo ayang’anizana ndi mkhalidwewo “mwaulemu ndi molimba mtima kwambiri.” Mwachitsanzo, limodzi la mapempho oyambirira a abalewo linali la mabuku ofotokoza Baibulo. ‘Iwo akuoneka kukhala ofunitsitsa kwambiri kulandira chakudya chauzimu mmalo mwa thandizo lakuthupi, ngakhale kuti akusoŵa zinthu zambiri,’ lipotilo likumaliza motero. Ndipo ngakhale kuti mikhalidwe m’misasayo ili yoipa, ‘mbali yaudongo koposa ili kumene abale athu akukhala.’
Watch Tower Society yapereka ndalama zogulira chakudya, mabulangete, zovala, nsapato, ndi mankhwala. Abale athu ku France anapereka zopereka mooloŵa manja, ndipo pofika kuchiyambiyambi kwa June, pafupifupi matani aŵiri a katundu anali atatumizidwa kwa abale athu osoŵa ku Rwanda.
Mosadabwitsa, mikhalidwe imeneyi yachititsa umboni wabwino kwambiri kuperekedwa. Openyerera akhudzidwa mtima kwambiri poona kuti abale athu a ku Rwanda analandira thandizo ndi chichirikizo chotero kwa Mboni zinzawo, ndipo kwakhala kotheka kugaŵana thandizo limeneli ndi ena. Ena anena kuti Mboni ndizo zokha zimene zachezeredwa ndi ziŵalo za chipembedzo chawo m’misasayo!
Mkhalidwe wovuta wa abale athu a ku Rwanda umatikumbutsa kuti mu “masiku otsiriza,” ano anthu adzakhala “aukali” ndi “achiwawa.” (2 Timoteo 3:1-5; Today’s English Version) Ndipo pamene kuli kwakuti Yehova samalonjeza kuti adzatetezera anthu ake mozizwitsa ku ngozi zakuthupi, iye amalonjezadi kutetezera mkhalidwe wawo wauzimu ndi unansi wawo ndi iye ndipo, mu ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu, kuukitsa awo amene akufa tsopano. (Salmo 91:1-10) Mapemphero athu akuti Yehova achirikize ndi kuthandiza abale otsalawo a ku Rwanda m’nthaŵi imeneyi yovuta apitirizetu kuperekedwa kaamba ka iwo.—Salmo 46:1.