Mfungulo ya Moyo wabanja Wachipambano
“TILI ndi mabanja amene akusweka mwathu muno,” anatero woyembekezera kusankhidwa kukhala prezidenti mu United States chaka chatha. Ndithudi, ukulu wa kusweka kwa mabanja ukuziziritsa m’nkhongono. “Kusintha kwakukulu kofananako m’malipoti a zachuma kapena maindasitale mkati mwa nyengo yofananayo,” anatero magazini a Fortune, “kudzatichititsa kakasi ndi kudabwa.”
Ngakhale mabanja amene akuyesa kutsatira malamulo a mkhalidwe a Baibulo kaŵirikaŵiri amayambukiridwa ndi vutolo. Zaka zingapo kumbuyoku, tate wina wa ana asanu ndi mmodzi osafika zaka khumi ndi zitatu anauzidwa ndi Mkristu mnzake motsimikiza kuti: “Zikhoza kuchitika kuti anayi a ana anu nkupanduka pachowonadi.” Komabe, tate ameneyu sanafune konse kuti zimenezi zikachitike ngakhale kwa mmodzi yekha wa ana ake. Iye anafotokoza chifukwa chake.
“Ana athu sali kwenikweni athu,” iye anatero. “Iwo anaikiziridwa ndi Yehova Mulungu kwa ine ndi mkazi wanga, monga ‘choloŵa,’ kapena mphatso yochokera kwa iye. Ndipo iye anati ngati tiwaphunzitsa mwanjira yoyenera, ‘sadzachokamo.’ Chotero tayesayesa nthaŵi zonse kuwasamalira monga ngati kuti anali a Yehova.”—Salmo 127:3; Miyambo 22:6.
Tateyu anazindikira mfungulo ya moyo wa banja wachipambano—makolo ayenera kusamalira ana awo monga ngati kuti akusamalira chuma cha Mulungu. Ngakhale kuti izi sizikutanthauza kuti ana adzalabadira chitsogozo chanu nthaŵi zonse, inu muli ndi thayo la kusamalira ana amene Mulungu wakuikizirani.
Thayo Lalikulu
Muyenera kupereka chisamaliro chimenechi ndi mantha aulemu ndi nkhaŵa yaikulu, osati mosasamala kapena mwamphwayi. Muyenera kutherapo nthaŵi ndi zoyesayesa mukumazindikira kuti mudzachita chodziyankhira kwa Mulungu kaamba ka choloŵa chake, kapena mphatso imene anakupatsani. Simuyenera kuyesa njira zina zolerera ana. Makolo amangofunikira malangizo a Mulungu operekedwa m’Mawu ake, Baibulo, ndipo ayenera kuwatsatira mosamalitsa.
Nazi zimene Yehova Mulungu akulangiza: “Muziwaphunzitsa [mawu anga] mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu. Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pa maso anu. Ndipo muziwalembera pamphuthu za nyumba zanu, ndi pazipata zanu.” Baibulo limafulumizanso kuti: “Atate inu, . . . muwalere [ana anu] m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].”—Deuteronomo 6:7-9; Aefeso 6:4.
Chotero kusamalira ana kumafuna chisamaliro cha tsiku ndi tsiku; inde, kumatanthauza kuwapatsa mowoloŵa manja nthaŵi yanu ndipo makamaka chikondi chanu ndi chisamaliro chanu chachikulu. Makolo amene amapatsa ana awo zinthu zofunika zimenezi amachita zimene Mulungu amanena kuti nzofunika kupangitsa moyo wa banja kukhala wachipambano.
Kodi mumaganiza kuti kutereku nkufunsira zopambanitsa? Makolo ambiri amasonyeza mwa machitidwe awo kuti nzimene amaganiza. Komabe, mphatso zochokera kwa Mulungu zimenezi—ana anu—zimafunikiradi chisamaliro chapadera chowonjezereka.
Mmene Mungawasamalirire
Mwanzeru, talingalirani za chitsanzo cha awo amene anapeza chipambano m’kulera ana. Magazini ena, m’nkhani yake yosonyezedwa pachikuto ya mutu wakuti “Mabanja Odabwitsa,” inatchula zinthu zinayi zimene zili zofunika m’kulera ana mwachipambano: “[1] Kukambitisirana panthaŵi ya chakudya kumene kumasonkhezera kulingalira kolama, [2] kuŵerenga mabuku abwino, [3] chisonkhezero cha anthu opereka chitsanzo chabwino, [4] kudziŵa kuti pali mwambo wa banja wofunika kuusunga.”—U.S.News & World Report, December 12, 1988.
Ponena za “kukambitsirana panthaŵi ya chakudya,” kumbukirani kuti Mulungu amalangiza makolo kuphunzitsa ana awo pamene akhala pansi m’nyumba mwawo. Kodi banja lanu limadyera pamodzi nthaŵi zonse, mwakutero mukumapereka mpata tsiku ndi tsiku wakucheza pamodzi ndi makambitsirano otsitsimulana? Nthaŵi zoterozo nzofunika kwambiri ndipo zimakhala zosaiŵalika kwa ana, zikumawapatsa lingaliro la bata ndi chisungiko. Mwana wina wa zaka zisanu ndi chimodzi ananena kuti anakonda kwambiri nthaŵi zachakudya “chifukwa chakuti simuyenera kudandaula za aliyense,” popeza kuti onse amakhalapo.
Bwanji ponena za mtundu wa kukambitsirana kwanu panthaŵi ya chakudya? Kodi makambitsirano anu kaŵirikaŵiri amazikidwa pankhani za “mabuku abwino,” kuphatikizapo Baibulo ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo mukumakambitsirana za utumiki wathu kwa Mulungu kapena nkhani zonena za chilengedwe cha Mulungu? Kuwonjezera pakukambitsirana kwa panthaŵi ya chakudya kotero, mwandandanda yokhazikika ya kuphunzira, makolo ayenera kukulitsa mwa ana awo chikondi pa Yehova ndi malamulo ake olungama.
“Kudyera pamodzi nthaŵi zonse sikunali vuto,” anafotokoza motero tate wa ana asanu ndi mmodzi wotchulidwa poyambapo. “Iko kunali chizoloŵezi, ndipo kunatigwirizanitsa pamodzi. Koma kukhala ndindandanda yokhazikika ya phunziro la Baibulo kunali kovuta.” Chifukwa cha kutopa pambuyo pa tsiku la ntchito yotopetsa, nthaŵi zina iye anali kuodzera paphunzirolo. Komabe, sanasiye kuchititsa phunziro la Baibulo lokhazikika ndi ana ake, ndipo nthaŵi zonse anakambitsirana nawo aliyense payekha ndi kumvetsera kwa iwo kwa nthaŵi zotalikirapo.
Kuwonjezera pakutsogolera m’makambitsirano opindulitsa a panthaŵi ya chakudya ndi kuwapezera mabuku abwino, kodi mumatsimikizira kuti ana anu amalandira “chisonkhezero cha anthu opereka chitsanzo chabwino”? Chowonadi nchakuti, kulinganiza kuti ana anu adziyanjana nthaŵi zonse ndi awo amene amalondola chitsanzo cha munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, Yesu Kristu, nkofunika kwambiri kwa iwo ngati ati adzakhale achikulire achipambano.
Chomalizira, bwanji ponena za “kudziŵa kuti pali mwambo wa banja wofunika kuusunga”? Ana anu ayenera kuzindikira kuti pali miyezo ya banja imene ayenera kuisunga—kuti makhalidwe ena, malankhulidwe, mavalidwe, machitidwe, ndi zina zotero, siziloledwa ndipo zimaswa mwambo wa banja. Ayenera kuzindikira kuti kuswa mwambo wa banja ndimlandu waukulu—kuti kungakupwetekeni mtima kwambiri, monga momwe anachitira kholo lakale Yakobo, amene anyamata ake mwamachitidwe ochititsa manyazi anapangitsa khololo kukhala munthu ‘wonunkha kwa anthu okhala m’dzikolo.’—Genesis 34:30.
Tate wa ana asanu ndi mmodziyo amene anaona ana akewo monga chuma cha Mulungu anagogomezera makamaka “mwambo wa banja.” Iye anakambitsirana nthaŵi zonse ndi ana ake mmene miyezo ya banja ponena za mavalidwe, kapesedwe, ndi kulekana ndinjira za dzikoli inaliri yogwirizana ndi mzimu ndi chitsogozo cha Mlengi, Yehova Mulungu. Monga chotulukapo cha nthaŵi yaikulu, chikondi, ndi chisamaliro chachikulu zopatsidwa kwa iwo—akumaphunzitsidwa m’njira zimene ayenera kuyendamo—ana asanu ndi mmodzi onsewo alabadira ‘mwakusachoka panjira yawo.’—Miyambo 22:6.
Kuzungulira dziko lonse, pali zikwi za mabanja olimba oterowo. Nchitamando chotani nanga chimene iwo amapereka kwa Mlengi, ndipo iwo amakhala mphotho yotani nanga kwa makolo achikondi opanda dyera! M’kupita kwa zaka, makolo oterowo amayamikiridwa mowonjezereka ndi ana awo amene amapindula ndi zoyesayesa zawo. Chonde pendani nkhani yotsatira ya mkazi wina amene analeredwa ndi makolo aumulungu, ndipo onani maphunziro opindulitsa amene mungatengepo.