Ana Ndi “Cholowa Chochokera kwa Yehova”
KODI n’chiyani chimene chimabwera m’maganizo mwanu mukamva mawu akuti “cholowa”? Kodi ndi ndalama, malo kapena nyumba kapenanso chinthu chinachake chamtengo wapatali chimene munalandira kuchokera kwa anthu a m’banja lanu? Kaya cholowa chake ndi chotani, chimakhalabe chamtengo wapatali ndipo mumafunitsitsa kuchisamalira.
Baibulo limati ana ndi “cholowa chochokera kwa Yehova.” (Sal. 127:3) Choncho n’zosachita kufunsa kuti makolo a Chikhristu amaona kuti ana awo ndi mphatso zochokera kwa Atate wawo wakumwamba ndipo amayesetsa kuwateteza komanso kuwasamalira. Amafunanso kuwathandiza kuti azisangalala komanso akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.
Koma n’zomvetsa chisoni kuti masiku ano makolo ena saona kuti ana awo ndi cholowa chochokera kwa Mulungu. (Yes. 49:15; 2 Tim. 3:1-3) Ena angamafunitsitse kusamalira ana awo koma zimawavuta kuchita zimenezi chifukwa cha mavuto osiyanasiyana. Kodi ena mwa mavuto amenewa ndi ati? Kodi Yehova amafuna kuti makolo azitani? Nanga kodi makolo angatani kuti alere bwino ana awo?
MAVUTO OMWE AMAKHALAPO
Zimene achibale komanso ena amayembekezera. M’madera ena, anthu amalemekeza kwambiri makolo omwe ali ndi ana ochuluka. Choncho anthu okwatirana angamakakamizidwe ndi achibale kapena maneba kuti akhale ndi ana ambiri, mwinanso kuposa omwe angathe kuwasamalira.
Kudera nkhawa zam’tsogolo. M’mayiko amene ana ambiri amamwalira chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi, matenda komanso kusowa kwa thandizo la zaumoyo, mabanja ena amakhala ndi ana ambiri n’cholinga choti ngati ana ena atamwalira, padzapezeke ena opulumuka. Makolo enanso angasankhe kukhala ndi ana ambiri kuti akadzakalamba anawo adzawasamalire. Zimenezi zimachitika kwambiri m’mayiko amene boma silipereka thandizo kwa achikulire.
Njira za kulera. M’madera ena, sizikhala zophweka kuti mabanja apeze mankhwala othandiza kuti mayi asatenge mimba. Pomwe ena amada nkhawa kuti thupi lawo siligwirizana ndi njira zakulera zosadalirika zomwe zimapezeka m’dera lawo. Ndiye pali enanso amene sangathe kugwiritsa ntchito njira za kulera chifukwa choti ndi zodula.a
KODI YEHOVA AMAFUNA KUTI MAKOLO AZICHITA CHIYANI?
Muzipeza nthawi yochita zinthu ndi mwana aliyense payekha
Muzipezera ana anu zomwe amafunikira. Yehova anapatsa makolo udindo wopezera ana awo aang’ono zimene amafunikira. Iye amayembekezera kuti makolo azigwira ntchito mwakhama kuti apezere mwana aliyense chakudya, zovala komanso malo ogona. Yehova amafunanso kuti makolo azionetsetsa kuti anawo aphunzira zinthu zimene zingadzawathandize. Choncho makolo a Chikhristu samangofulumira kutumiza ana awo kumasukulu ogonera komweko. Koma amaonetsetsa kuti anawo akukhalabe panyumba mpaka atakula n’cholinga choti aphunzire maluso omwe angawathandize pa moyo. Amapezanso nthawi yochita zinthu ndi mwana aliyense, zomwe zimamuthandiza kumva kuti ndi wotetezeka ndiponso amakondedwa. Komabe, Yehova ndi wololera ndipo sayembekezera kuti makolo akhale olemera kuti akwanitse udindowu. Ndipotu iye anasankha makolo amene anali olimbikira ntchito koma osauka kuti alere Mwana wake wokondedwa.—Mat. 13:55, 56; Luka 2:24.
Mfundo ya m’Baibulo: “Ndithudi, ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a mʼbanja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.”—1 Tim. 5:8.
Yehova amamvetsa kuti makolo angamafunike kuthandizidwa pamene akukula. Ndipotu njira ina imene ana angalemekezere makolo awo ndi kuwathandiza pamene akalamba. (Eks. 20:12; 1 Tim. 5:4) Komabe, Yehova amasangalala makolo akamaganizira kwambiri mmene adzasamalire anawo, osati mmene anawo adzasamalire makolowo.—2 Akor. 12:14.
Muziwathandiza mwauzimu. Makolo alinso ndi udindo wophunzitsa ana awo kuti azikonda komanso kulambira Yehova. Iye amaona kuti zimenezi ndi zinthu zofunika kwambiri zomwe makolo ayenera kuphunzitsa ana awo.—Deut. 6:6, 7.
Mfundo ya m’Baibulo: “Pitirizani kuwalera [ana anu] powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.”—Aef. 6:4.
YEHOVA NDI WOFUNITSITSA KUKUTHANDIZANI
Muzikambirana kuchuluka kwa ana amene mukufuna kudzakhala nawo
Muziganizira zam’tsogolo. Ngati mukufuna kudzakhala ndi ana, muziganizira mofatsa mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Mwachitsanzo, ngati mutadzakhala ndi ana ambiri, kodi muzidzakwanitsa kuwapezera chakudya, zovala ndiponso kuwapititsa kusukulu? Ngati si choncho, kambiranani ndi mwamuna kapena mkazi wanu n’kuona kuchuluka kwa ana omwe mungadzakhale nawo kuti muzidzakwanitsa kuwasamalira mmene Yehova amafunira. N’zoona kuti Yehova amamvetsa kuti tikhoza kukumana ndi zosayembekezereka pa moyo. (Mlal. 9:11) Komabe iye adzadalitsa zimene mukuyesetsa kuchita kuti mukhale makolo abwino.
Mfundo za m’Baibulo: “Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino, koma onse amene amachita zinthu mopupuluma amasauka.”—Miy. 21:5.
“Ndi ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi nʼkuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?”—Luka 14:28.
Muziika Yehova pamalo oyamba m’banja mwanu. Kulambira Yehova kuzikhala chinthu chofunika kwambiri. Ngati muli ndi ana kale, muziyesetsa kuphunzitsa mwana aliyense payekha kuti azikonda Yehova. Muziwathandiza kuti azimvetsera mwatcheru pamisonkhano ya mpingo. Muzionetsetsa kuti mukuchita Kulambira kwa Pabanja wiki iliyonse. Muziphunzitsa ana anu kulalikira. Musamasiye udindo wolera ana m’manja mwa ana anu akuluakulu kapenanso achibale ena. Kuphunzitsa ana kuti azikonda Yehova kumafuna nthawi komanso khama, koma madalitso amene mumapeza amakhala ambiri.
Mfundo ya m’Baibulo: “Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe mʼchoonadi.”—3 Yoh. 4.b
Muzidalira Yehova. Kaya mukuganizira zokhala ndi ana kapena muli nawo kale, musamakayikire kuti mfundo za Yehova n’zofunika kwambiri kuposa chikhalidwe kapena miyambo ya m’dera lanu.
Kuthandiza ana anu kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kumafuna nthawi komanso khama
Ngati mutasankha kukhala ndi ana ochepa, musamakayikire kuti Yehova azidzakupatsani zonse zofunika mukadzakalamba. Muzipewa maganizo oti ana ndi “podzapulumukira.” Musamaope kuti mudzasowa mtengo wogwira. Yehova akulonjeza kuti adzakusamalirani. Ndipotu nthawi zonse amakwaniritsa zimene walonjeza.—Yos. 23:14.
Mfundo za m’Baibulo: “Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”—Miy. 3:5, 6.
“Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.”—Sal. 37:25.
“Choncho nthawi zonse muziika Ufumu ndi mfundo zolungama za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.”—Mat. 6:33.
Ana ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova wapereka kwa makolo. Iye amasangalala makolo a Chikhristu akamalera ana m’njira imene iyeyo amafuna. Iwo amapezera ana awo zimene amafunikira, kuwathandiza kuti azisangalala komanso kuwathandiza mwauzimu. Amasankhanso kuchuluka kwa ana amene angakhale nawo ndipo amaona kuti zimene Mulungu amafuna n’zofunika kwambiri kuposa chikhalidwe kapena miyambo ya m’dera lawo. Makolo a Chikhristu akamachita zimenezi, amasonyeza kuti ana awo ndi mphatso yamtengo wapatali, kapena kuti “cholowa chochokera kwa Yehova.”
a Mwamuna ndi mkazi wake ndi amene ayenera kusankha kuchuluka kwa ana amene adzakhale nawo, nthawi imene adzakhale ndi anawo komanso njira ya kulera imene adzagwiritse ntchito, bola ikhale yosachotsa mimba. Palibe amene ayenera kuwaweruza pa zimene asankha. (Aroma 14:4, 10-13) Mabanja a Chikhristu amayeneranso kukumbukira malangizo a pa 1 Akorinto 7:3-5.
b Ngakhale kuti ana otchulidwa pavesili ndi Akhristu amene Yohane anawaphunzitsa choonadi, ndi mmenenso makolo amamvera akaganizira za ana awo omwe akutumikira Yehova.