Chiweruzo Chomalizira
“PAMENE umwalira moyo wako udzazunzidwa wokha; ndiko kudzakhala helo wake: koma patsiku lachiweruzo thupi lako lidzagwirizana ndi moyo wako, ndipo pamenepo udzakhala ndi mahelo aŵiri, moyo wako ukukhetsa thukuta lamwazi, ndipo thupi lako likuzunzika ndi kupweteka kwakukulu.”
UMU ndimmene mlaliki C. H. Spurgeon wa m’zaka za zana la 19 anafotokozera lingaliro la atsogoleri achipembedzo la tsiku lachiweruzo ndi kuvutika kwa okanidwa. Mmisiri Wachitaliyana Michelangelo anali ndi chikhulupiriro choopsa chofananacho, monga momwe zikuonekera pa chithunzithunzi chake cha “Chiweruzo Chomalizira” (chigawo chake chimene chasonyezedwa pamwambapa), chimene analemba pa chipupa cha nyumba yolambirira ya Sistine m’Roma. The New Encyclopædia Britannica imanena motere ponena za chithunzithunzi chimenechi: “Kristu wa m’Chiweruzo ali mulungu wodzudzula ndi woopsa mmalo mwa mpulumutsi Wachikristu, woyezamira kwambiri kukana fuko la anthu mmalo mwakulandira odalitsidwa kumwamba.”
Chiphunzitso cha Chikristu Chadziko
M’zaka mazana apita, tsiku lachiweruzo ndi moto wa helo zinali nkhani zotchuka za ulaliki. Pamaguwa awo, alaliki onga C. H. Spurgeon analankhula mwamphamvu ndi malongosoledwe opereka chithunzi ponena za chizunzo choipitsitsa choyembekezera ochimwa. Masiku ano, kulalikira koteroko sikumamvedwa kaŵirikaŵiri. Koma moto wa helo ndi chiweruzo chomalizira zidakali ziphunzitso zalamulo za matchalitchi ambiri.
Zochuluka za zipembedzo za Chikristu Chadziko kwakukulukulu zimavomereza chiphunzitso cha Roma Katolika chakuti ziweruzo za Mulungu zimadza m’njira ziŵiri. Choyamba, pali “chiweruzo chachindunji.” Pamene munthu amwalira, moyo wake wolingaliridwa kukhala wosakhoza kufa umaweruzidwa pomwepo ndi kutumizidwa ku umuyaya kaya mu helo kapena kumwamba.a Ndiyeno pamabwera chiweruzo chomalizira, kapena cha onse, pamapeto a nthaŵi pamene matupi a akufa aukitsidwa ndi kugwirizanitsidwanso ndi miyoyo yawo yosakhoza kufayo.
Patsiku lachiweruzo limeneli, miyoyo imakhalabe kumwamba ndipo imagwirizanitsidwa ndi matupi amene apangidwa kukhala opanda chivundi. Amene azunzika m’helo amakhalanso m’menemo, ndipo miyoyo yawo imagwirizanitsidwanso ndi matupi oukitsidwawo, opanda chivundi. Malinga ndi kunena kwa ena, ichi chimawonjezera kuzunzika kwawo. Awo okhalabe ndi moyo monga anthu padziko lapansi samafa. Iwo amaweruzidwa pamene adakali amoyo ndipo amapita, “thupi ndi moyo” titero kunena kwake, molunjika kumwamba kapena ku helo.
Kuthekera kwakupirira kuzunzika kosaneneka m’moto wa helo kwapangitsa nkhani yonse ya chiweruzo chomalizira chokhala m’manja mwa Yesu Kristu kukhala chinthu chochititsa mantha kuchilingalira. Polingalira za chimenechi, kodi mungadabwe mutadziŵa kuti, kwenikweni, ziweruzo za Mulungu kaŵirikaŵiri zimadzetsa chisangalalo ndikuti Tsiku Lachiweruzo lidzakhala imodzi ya nthaŵi zosangalatsa koposa m’mbiri yonse ya anthu? Kodi zingakhale choncho motani?
[Mawu a M’munsi]
a Aroma Katolika amakhulupiriranso m’chothekera chachitatu: chilango chakanthaŵi m’purigatoriyo usanaloŵe kumwamba.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Random/Sipa Icono