Kodi Akufa Ali ndi Chiyembekezo Chotani?
Mkazi wina ku Augusta, Georgia, U.S.A., analemba kuti: “Posachedwapa mchemwali wanga wamng’ono anafa m’ngozi yowopsa ya galimoto. Anali ndi zaka 18 zokha, wathanzi labwino ndipo wokonzekera kumaliza maphunziro. Ndinapeza matrakiti angapo pakati pa maluŵa oikidwa pamanda pake. Iwo andithandiza kwambiri, ndipo ndingakonde kuoda bukhu lotsatira limene mumagaŵira.”
Mkaziyo anapempha bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Iye anagamula kuti: “Ndiganiza kuti lidzathandiza ine ndi banja langa kumvetsetsa zinthu ndi kupeza mtendere wamaganizo.”
Mukhoza kulandira kope la chofalitsidwa chimenechi chokhala ndi zithunzithunzi zokongola mwakudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 256 la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)