Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 2/1 tsamba 32
  • “Ndinkapsa ndi Mkwiyo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndinkapsa ndi Mkwiyo”
  • Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1991
w91 2/1 tsamba 32

“Ndinkapsa ndi Mkwiyo”

Msungwana wazaka 15 zakubadwa wa ku Knoxville, Tennessee, analemba motere: “Ndinafuna kulongosola chiyamikiro changa kwa inu kaamba ka bukhu lanu latsopano la Questions Young People Ask​—Answers That Work. Ndasangalala kwambiri kuliŵerenga.”

Kenaka iye akulongosola chimene chinapangitsa kuti alembe kalata yake: “Ndinkapsa ndi mkwiyo ndi mchimwene wanga chifukwa anandinenera pamene sindinachite chinachake panyumba chomwe ndinafunikira kuchita. Popeza tsopano mkwiyowo unatha, ndikudzimva waliŵongo ndipo ndabwera m’chipinda mwanga kudzakulemberani ndi kuŵerenga ‘Why Are My Brother and Sister So Hard to Get Along With?’ (Mutu 6) ndikudziŵa kuti udzakhala wothandiza kwambiri kulaka mavuto amtsogolo.”

Achichepere amayang’anizana ndi mafunso ambiri amene amafunikira chiweruzo chanzeru: Kodi ndiri wokonzekera kupalana ubwenzi? Kodi ndingathetse bwanji kukhumbira? Bwanji ponena za kugonana ukwati usanachitike? Kodi ndingadziŵe motani ngati chiri chikondi chenicheni? Kodi ndiyenera kusankha ntchito yophunziridwa yotani? Kodi ndingalake motani chitsenderezo cha ausinkhu wanga? Achichepere amafunikira mayankho ogwira ntchito ku mafunso oterowo ndi ena.

Tikulingalira kuti mudzapindula kwakukulu ndi bukhu la Questions Young People Ask​—Answers That Work, limene liri ndi mutu pa lirilonse la mafunsoŵa. Mungalandire kope la bukhu lokhala ndi zithunzi zokongolali mwakungodzaza ndi kutumiza kapepalaka.

Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 320 la Questions Young People Ask​—Answers That Work. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakumaloko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena