“Korona ndi Bukhu la Umboni”
“ATATERO [Yehoyada wansembe] anatulutsa mwana wa mfumu namuika korona ndi Bukhu la Umboni; namlonga ufumu, namdzoza.” (2 Mafumu 11:12, NW) Umu ndi mmene bukhu la Mafumu likufotokozera kulongedwa ufumu kwa Mfumu Yoasi. Kodi mwawona kuti pambali pa “korona,” kapena nduwira yachifumu, Yehoyada anaikanso “Bukhu la Umboni” pa mfumu yachichepereyo? Kodi nchiyani chomwe chinali Bukhu la Umboni? Ndipo kodi nchifukwa ninji linali mbali ya mwambo wakulongedwa ufumuwu?
Liwu Lachihebri lotembenuzidwa panopo kukhala “Bukhu la Umboni” kaŵirikaŵiri limasonya ku Malamulo Khumi kapena Chilamulo cha Mulungu mwachisawawa. (Eksodo 31:18; Salmo 78:5, Revised Standard Version) Mogwirizana ndi chimenechi, nkhani yolingana nayo yopezeka pa 2 Mbiri 23:11 inalembedwa motere mu The Jerusalem Bible (1966): “Kenaka Yehoyada anabweretsa mwana wa mfumu, namveka chisoti chachifumu, ndipo anampatsa Lamulo.” Komabe, pa 2 Mafumu 11:12, matembenuzidwe ameneŵa amaloŵa mmalo liwu lakuti “Bukhu la Umboni” ndi liwu lakuti “zigwinjiri,” ngakhale kuti liwu Lachihebri limodzimodzilo likupezeka m’mavesi aŵiri onsewo. Kodi nchifukwa ninji?
Bukhu lotchuka Lachijeremani lothirira ndemanga Baibulo lotchedwa, Herders Bibelkommentar, likulongosola kuti otembenuza ena sangalingalire kuti mfumuyo ingavale Chilamulo pamutu pake kapena pamkono. Popeza kuti polongosola za Mfumu Sauli, 2 Samueli 1:10 amatchula za chigwinjiri (kapena khoza) limodzi ndi korona amene anavala, iwo amakhulupirira kuti lemba la pa 2 Mafumu 11:12 poyambirira linalembedwa kuti “korona ndi zigwinjiri.” Komatu kumeneku nkuganiza chabe. Kuloŵa mmalo liwu lakuti “Bukhu la Umboni” ndi “zigwinjiri” kumatanthauza kusintha lemba kwakukulu.
Chotero The New Jerusalem Bible (1985) imabwezeretsa lingaliro la Chilamulo, kapena pangano la lamulo, ikumamasulira mawuwo motere, “nampatsa kope la panganolo.” Koma kodi Yehoyada anampatsa Yoasi “Bukhu la Umboni”? Zowona, liwu Lachihebri lotembenuzidwa ‘kuika’ lingamasuliridwenso kukhala “kupatsa.” Koma ponse paŵiri m’Mafumu ndi Mbiri, likuwoneka kamodzi kokha, kusonya ponse paŵiri ku korona ndi Bukhu la Umboni. Kuwonjezerapo, ilo latsatiridwa mofulumira ndi liwu Lachihebri lakuti “pa.” Chotero, “kuika pa” kuyenera kukhala kutembenuza kolondola. Ponse paŵiri korona ndi Bukhu la Umboni ‘zinaikidwa pa’ Mfumu Yoasi wachichepere, monga momwe New World Translation ikusonyezera.
Chotero kodi nchifukwa ninji—ndipo ndimotani—mmene mkulu wansembe ‘anaikira’ Bukhu la Umboni pa mfumu yachichepereyo? Talingalirani kufotokoza kwa katswiri Wachijeremani wotchedwa Otto Thenius uku: “Chilamulo, ndibukhu limene munalembedwa malamulo a Mose. Ilo linaikidwa mophiphiritsira pamutu pa mfumu, pambuyo pakukometseredwa ndi korona.” (Die Bücher der Könige) Mofananamo, Profesa Ernst Bertheau akuthirira ndemanga motere: “Kuikidwa kwa Chilamulo [pa mfumu] kunalidi kophiphiritsira, kuti mfumuyo inali ndi thayo lakulamulira mogwirizana nalo.”—Die Bücher der Chronik.
Mulungu analamula kuti pamene mfumu iyamba kulamulira pampando wachifumu, inayenera kudzilembera kope la Chilamulo, kuliphunzira ndi kuligwiritsira ntchito m’moyo wake wonse. (Deuteronomo 17:18-20) Kuika “Bukhu la Umboni” pa mfumu yatsopano kukanakhala kuchitira fanizo kwachidule kophiphiritsira kuti ngakhale kuti iye wakhala mfumu tsopano, iye sanali pamwamba pa Chilamulo cha Yehova. Momvetsa chisoni, pambuyo pa imfa ya mkulu wansembe Yehoyada, Yoasi anaiwala phunziro lofunika limeneli ndipo pang’onopang’ono analeka kulambira Yehova, pomalizira pake anaphedwa ndi achiŵembu.—2 Mbiri 24:17-25.