Mkangano wa Imfa ya Yesu
PATSIKU la Paskha wa 33 C.E., pananyongedwa anthu atatu. Amuna atatu oŵeruzidwa anatsogozedwa ku malo akunja kwa malinga a Yerusalemu ndikukaphedwa mwanjira yosautsa koposa, ndiyochititsa manyazi: kupachikidwa pa milongoti yowongoka. Kunyonga koteroko kunali kofala m’nthaŵi za Roma, motero kukayembekezeredwa kuti kupha kwa pa Paskha panthaŵiyi kunaiŵalidwa kalekale. Komabe, mmodzi wa amuna ophedwawo anali Yesu Kristu. Imfa yake inabutsa masinthidwe aakulu achipembedzo ndi mkangano.
Papita pafupifupi zaka zikwi ziŵiri kuchokera pa chochitikacho, chotero mungachilingalire monga chochitika wamba cha mbiri yamakedzana. Komabe, kodi mumadziŵa kuti mkangano umene unabukapo uli kutalitali nkuthetsedwa?
Monga momwe mungadziŵire, anthu mamiliyoni ambiri amanena kuti Yesu anawafera. Amakhulupirira mwamphamvu kuti imfa ya Kristu ndiyo mfungulo ku kuwomboledwa ndi kukhululukidwa machimo, kuti kukhulupirira imfa yake ndiko njira yachipulumutso. Komabe, modabwitsa, nkhani ya mu Anglican Theological Review ikusimba kuti chiphunzitso chokondedwa chimenechi chiri “m’vuto.” Ndipo “vuto” limenelo likuchokera kwa atsogoleri achipembedzo.
Anglican Theological Review ikufotokoza kuti: “Chiphunzitso cha chitetezero m’lingaliro Lachikristu chiri m’vuto chifukwa chakuti maziko ake Abaibulo akukaikiridwa, kupangidwa kwake kwadzazidwa mopambanitsa ndi malingaliro osakhalitsa . . . , ndipo kulongosoledwa kwake mumkhalidwe wauzimu wokondedwa kwakhala mwamtundu wa kutengeka maganizo ndi kudzilungamitsa kwaumwini.” Zowonadi, ponse paŵiri akatswiri a maphunziro a zaumulungu Achiprotestanti ndi Achikatolika alephera kufikira chimvano chirichonse, ngati chiripo, ponena za chimene imfa ya Yesu Kristu imatanthauza.
Mungalingalire kuti izi ziri chabe kukangana kwa akatswiri a maphunziro azaumulungu oŵerengeka, kuti sizimakhudza moyo wanu. Koma talingalirani za ichi: Ngati imfa ya Yesu imaloŵetsamodi kaimidwe kanu pamaso pa Mulungu ndi ziyembekezo zanu za kukhalapo kosatha (kumwamba kapena kwina kulikonse), pamenepo nkofunikira kuti muulingalire mkanganowu.
Kodi nchifukwa ninji akatswiri a maphunziro azaumulungu akutsutsanabe pankhaniyi? Mwachitsanzo, talingalirani Tchalitchi cha Roma Katolika. Icho chiri ndi chiphunzitso choikidwiratu cholongosoledwa bwino lomwe pa kusakhoza kufa kwa moyo ndi pa Utatu. Komabe, tchalitchicho nchosatsimikiza kwenikweni ponena za kuwomboledwa kupyolera mu imfa ya Kristu. New Catholic Encyclopedia ikuvomereza kuti: “Madongosolo ambiri ndi osiyanasiyana apangidwa kulongosola mmene munthu anamasulidwira ku ukapolo wa uchimo ndikubwezeretsedwa ku chisomo . . . Koma palibe nlimodzi lomwe la madongosoloŵa limene lakhala lachipambano kotheratu. . . . Maphunziro azaumulungu a chiombolo m’mbali zinazake ngosafikirika ndipo apitirizabe kukhala vuto m’maphunziro azaumulungu.”
Pamenepo, siziyenera kukudabwitsani, kuti mwa anthu mamiliyoni omwe amanena mwamphamvu kuti ‘Yesu anatifera,’ ndi oŵerengeka okha omwe ali ndi lingaliro lotsimikizirikako pang’ono ponena za chimene ichi chimatanthauzadi. Anglican Theological Review ikunena motere: “Atafunsitsidwa . . . Mkristu wokhulupirira kaŵirikaŵiri amalephera kutchula magwero Abaibulo a chiphunzitsocho, kapena kufotokoza mmene chimagwirira ntchito.” Polemetsedwa ndi chiphunzitso chimene satha kuchimvetsetsa kaya kuchilongosola, alambiri a matchalitchi akulephera kuwona mmene imfa ya Kristu iliri yoyenera ku miyoyo yawo.
Kulephera kwa Chikristu Chadziko kulinganiza chiphunzitso chomveka pa kuwomboledwa kwalepheretsanso zoyesayesa zake zakufikira Ayuda, Ahindu, Abuda, ndi ena ndi uthenga Wachikristu. Pamene kuli kwakuti ambiri oterowo amakhumbira ndikulemekeza ziphunzitso zambiri za Yesu, msokonezo wozungulira imfa ya Kristu ndi chimene imatanthauza ukukhala chopinga panjira ya kuchikhulupiriro.
Kodi kufunika kwa imfa ya Kristu kwangokhala chinsinsi—chosakhoza kumvetsetsedwa ndi anthu? Kapena kodi pali malongosoledwe ake anzeru, ozikidwa pa Baibulo? Mafunso ameneŵa amafunikira kuti muwalingalire, popeza kuti Baibulo likupereka chilengezo chozizwitsa ichi ponena za Kristu: ‘Yense wokhulupirira iye sadzataika koma adzakhala nawo moyo wosatha.’—Yohane 3:16.