Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 1/1 tsamba 4-7
  • Chimwemwe Chapadziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimwemwe Chapadziko Lonse
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Chimwemwe Chomwe Palibe Amene Angachilande”
  • ‘Kufikira Malekezero Ake a Dziko’
  • ‘Khalani Nacho Chikondano Wina Ndi Mnzake’
  • Anthu Amtendere
  • ‘Mwapenya Zunzo Langa’
  • Tumikirani Yehova ndi Chimwemwe cha Mtima
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Anthu Achimwemwe—Nchifukwa Ninji?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Dzazidwani ndi Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chimwemwe cha Yehova Ndicho Linga Lathu
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 1/1 tsamba 4-7

Chimwemwe Chapadziko Lonse

‘TAWONANI, atumiki anga adzayimba ndi mtima wosangalala.’ (Yesaya 65:14) Anatero Yehova kupyolera mwa mneneri wake Yesaya, ndipo mawu ake akukwaniritsidwa bwino motani nanga pa Mboni za Yehova! Kodi kusangalala kwa mtima wawo kumachokera kuti? Kumachokera m’kulambira kwawo Yehova Mulungu mogwirizana. Iye ali “Mulungu wachimwemwe,” ndipo awo amene amamlambira iye ali ‘okondwerera mwa Yehova.’ (1 Timoteo 1:11, NW; Zekariya 10:7) Kudzipereka kwachimwemwe kumeneku kumawagwirizanitsa kukhala mtundu umodzi pamene onse pamodzi akulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ndikukweza mfuu yapadziko lonse ya chitamando kwa Mulungu wawo.​—Chibvumbulutso 7:9, 10.

“Chimwemwe Chomwe Palibe Amene Angachilande”

Ndithudi, kufalitsa dzina ndi Ufumu wa Mulungu kuli magwero a chimwemwe chosatha kwa Mboni za Yehova. (Marko 13:10) Iwo amavomereza ku mawu a wamasalmo awa: ‘Mudzitamandire ndi dzina lake loyera; mitima yawo ya iwo ofunsira Yehova ikondwere.’​—Salmo 105:3.

Kaŵirikaŵiri, iwo amalaka zopinga kuti achite chimenechi. Mu Spanya, Isidro anadzipereka yekha kwa Yehova, ndipo anafuna kulankhula ndi ena ponena za Iye. Koma iye ngwoyendetsa galimoto ya mtengatenga wokhala ndi nthaŵi yopumula yochepa, ankapanga maulendo aatali usiku namagona masana. Isidro anafuna kuchitira umboni kwa oyendetsa magalimoto amtengatenga anzake, koma kodi akachita motani zimenezi?

Iye anaika m’galimoto mwake wailesi ya CB (citizens band) imene akanaigwiritsira ntchito kulankhula kwa oyendetsa ena. Posakhalitsa anapeza channel 13, yomwe siinkagwiritsiridwa ntchito kwambiri, ndipo anasankha kuigwiritsira ntchito. Ndithudi, pamene iye poyamba anapereka lingaliro kwa oyendetsa magalimoto a mtengatenga ena kuti akambitsirane za Baibulo pa wailesi ya CB, iwo anakana. Koma ena anamvetsera. Mphekesera inafalikira, ndipo oyendetsa magalimoto owonjezerekawonjezereka Achispanya ankatsegula channel 13. Posachedwapa, Isidro anamva kuti mmodzi akupanga makonzedwe akuwonjezera maphunziro ake a Baibulo.

Mu Italiya mwamuna wina anamva za Mboni za Yehova kupyolera m’kukambitsirana komwe anali nako m’basi. Mkazi wake anakumana nawo kupyolera mwa bwenzi. Onse aŵiri anaphunzira Baibulo ndipo anali ofunitsitsa kugaŵana ndi ena zomwe anaphunzira. Iwo adali ofunitsitsa kwambiri kwakuti mwamunayo anakana kukwezedwa pantchito ndipo mkaziyo analeka ntchito yokhala ndi malipiro abwino kotero kuti angamathere nthaŵi yowonjezereka akuuza ena mbiri yabwino ya Ufumu. Kodi chinali chaphindu? Inde. Mwamunayo akuti: “Kuyambira pamene tinadziŵa chowonadi, mkazi wanga ndi ine takhala ndi chimwemwe chakuthandiza anthu 20 kufikira chidziŵitso cholongosoka cha chifuno cha Mulungu. Pamene madzulo afika, ndipo ndabwerera kunyumba pambuyo pa tsiku lathunthu lothera muutumiki wa Yehova, zowonadi, ndimadzimva wotopa. Koma ndiri wachimwemwe, ndipo ndikuyamikira Yehova pondipatsa chimwemwe chomwe palibe amene angachilande.”

‘Kufikira Malekezero Ake a Dziko’

Anthu amene ali mu mtundu wachimwemwe wa Mulungu amasonyeza changu chofananacho kulikonse kumene ali, ngakhale ‘ku malekezero ake a dziko.’ (Machitidwe 1:8) Pali malo oŵerengeka omwe ali kumalekezero kuposa mbali yakumpoto ya Greenland. Komabe, ngakhale kumeneko, makilomita 320 kumpoto kwa Arctic Circle, kuli mpingo waung’ono wa Ilulissat, wokhala ndi anthu 19. Iwo amalalikira mbiri yabwino imodzimodziyo yofanana ndi ya okwatirana Achitaliyana aja, ndipo anakondweretsedwa chaka chatha kuwona nzika za ku Greenland zisanu ndi ziŵiri zikubatizidwa pochitira chithunzi kudzipereka kwawo kwa Yehova.

Makilomita zikwi zambiri kuchokera ku Greenland, pachisumbu chakumalo otentha cha Mauritius mu Indian Ocean, Anjinee ali ndi chimwemwe chofananacho. Poyamba zinthu zinali zovuta kwa Anjinee. Mu Mauritius, kupezeka pamisonkhano Yachikristu ndikulalikira poyera ponena za Mulungu sizimaonedwa kukhala ntchito zoyenera kwa msungwana wosakwatiwa yemwe ndi Mwenye Wachihindu. Koma Anjinee anapirira. Tsopano, zaka zisanu ndi zinayi pambuyo pakuyamba kwake njira Yachikristu, achibale ake ena akuphunziranso Baibulo.

Titatchula Anjinee sitiyenera kuiwala Emilio, wokhala kumbali ina yadziko, mu Honduras. Emilio anamva antchito anzake akukambitsirana Baibulo pantchito napempha kuti aphatikizidwemo. Iye sankatha kuŵerenga koma anamvetsera mwatcheru pamene malemba Abaibulo anaŵerengedwa. Pamene chowonadi Chachikristu chinaloŵa mumtima mwake, Emilio analeka njira yake ya moyo wachisembwere naleka kumwa mopambanitsa. Mboni za Yehova zinamphunzitsa kuŵerenga ndi kulemba, ndipo tsopano ndiminisitala mumtundu wachimwemwe wa Mulungu.

Makilomita zikwi zambiri kumpoto chakumadzulo kwa Honduras, nakubala wa Chieskimo wa ku Alaska anaphunzira chowonadi Chachikristu chimodzimodzicho. Mkazi ameneyu ankakhala m’mudzi wakutali kwambiri, ndipo anagwirizana ndi Mboni za Yehova mwakungolemberana makalata basi. Chotero anaphunzira mwakulemba makalata, anafunsa mafunso ake m’makalata, ndipo tsopano akugaŵana mwachangu ndi anansi ake zimene amadziŵa. Zitsanzo zonga zimenezi zingachulukitsidwe pafupifupi mopanda malire. Kuzungulira dziko lonse, odzichepetsa mtima akubwera ‘kutumikira Yehova ndi chikondwerero.’​—Salmo 100:2.

‘Khalani Nacho Chikondano Wina Ndi Mnzake’

Chinthu chimodzi chimene chimawakopa onsewa nchikondi chimene chiri mumtundu wachimwemwe wa Mulungu. Yesu anati: ‘Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:35) Chikondi Chachikristu chimawonedwa m’moyo watsiku ndi tsiku wa Akristu owona ameneŵa, ndipo makamaka m’nthaŵi zatsoka.

M’dziko lina la mu Afirika kumene mwachisoni ntchito ya Mboni za Yehova njoletsedwa, kudali chilala chachikulu. Anthu zikwi khumi anamwalira, ndipo nsambi zonse za ng’ombe zinatha psiti. Kodi Mbonizo zinapulumuka motani? Mwakumadya mizu yazomera ndi nthanga zophika za mapeyala! Koma tsoka lawo linapeputsidwa mwadzidzidzi pamene, mwa thandizo la Mulungu, Mboni za m’maiko ena mosayembekezera zinapatsidwa chilolezo chakutumiza matani 25 a zopereka zothandizira. Ndithudi, mosasamala kanthu za chiletsocho, zopereka zimenezi zinaperekezedwa ndi asilikali kutsimikizira kuti zafika mwachisungiko!

Zowonadi, Mboni za mu Afirika zimenezo zinakondwera kwambiri kulandira umboni umenewu wa chikondi cha abale awo pamene mawu a Yesaya anakwaniritsidwa kwa iwo akuti: ‘Tawonani, mkono wa Yehova sunafupika kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake siliri logontha, kuti silingamve.’​—Yesaya 59:1.

Anthu Amtendere

Anthu ofatsa mtima akukopedwanso kunka ku mtundu wachimwemwe wa Mulungu chifukwa chakuti ziŵalo zake zaleka njira zankhondo za dzikoli ndipo ‘asula malupanga awo kukhala zolimira.’ (Yesaya 2:4) Mu El Salvador, nyumba ya yemwe kale anali msilikali inali yodzaza ndi zikumbukiro za ntchito yake yausilikali. Koma pamene anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, iye anakulitsa zikondwerero zamtendere. Pomalizira pake, iye anachotsa m’nyumba mwakemo zinthu zonse zochita ndi nkhondo natenga ntchito yolalikira mwachangu.

Pamene magulu otsutsana ndi boma analanda mudzi wake, iye anaponyedwa m’ndende​—mwachiwonekere winawake adamuulula kukhala yemwe kale adali msilikali. Komabe, iye analongosola kuti sanalinso msilikali koma mmodzi wa Mboni za Yehova. Ogalukirawo anampatsa mlandu wakukhala ndi zida m’nyumba mwake, koma pamene anafufuza sanapeze nchimodzi chomwe. Mkulu wa ogalukirawo anafunsa anthu oyandikana naye nyumba ponena za iye. Yankho lofala linali lakuti: “Iye amangoyendayenda mkhwalala kulalikira ponena za Baibulo tsiku ndi tsiku.” Munthuyu anamasulidwa. Mosakaikira, changu chake chinapulumutsa moyo wake.

Lipoti lochokera m’dziko la mu Afirika likusimba za asilikali aŵiri omwe anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Wina anatumikira m’gulu lankhondo la boma, winayo ankamenyera gulu la zigaŵenga. Pomalizira pake, onse anasankha ‘kusula malupanga awo kukhala zolimira’ naleka ntchito yausilikali. Pamene anapezeka pa misonkhano Yachikristu kwa nthaŵi yoyamba, msilikali wotsutsa bomayo anafunsa winayo kuti: “Kodi ukufunanji kuno?” Iye anayankha kuti: “Nanga nawenso ukufunanji kuno?” “Kenaka,” lipotilo likumaliza motero, “akumakupatirana, iwo anagwetsa misozi yachimwemwe chifukwa chakuti iwo akakhoza kukhala pamodzi mumtendere.” Mosakaikira onse aŵiriwa omwe kale anali asilikali anapemphera kwa Mulungu motere: ‘Mundilanditse ku mlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.’​—Salmo 51:14.

‘Mwapenya Zunzo Langa’

‘Ndidzakondwera ndi kusangalala m’chifundo chanu: pakuti mudapenya zunzo langa; ndipo mudadziŵa mzimu wanga mu nsautso.’ (Salmo 31:7) Anapemphera motero wamasalmo, ndipo ambiri lerolino amakondwera chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amawathandiza kulaka mazunzo awo. Mu Falansa mmodzi wa Mboni za Yehova amachititsa phunziro kwa mkazi amene amavutika ndi kusokonezeka kwa maganizo. Mkaziyu wakhala akulandira thandizo la mankhwala amisala kwa nthaŵi yaitali, koma sanamthandize. Mlungu umodzi pambuyo pakuyamba phunziro lake, katswiri wa matenda amisala anafunsa kuti: “Kodi ukumvetsetsadi zimene mkaziyu akulongosola kwa iwe kuchokera m’Baibulo?” Choncho mlungu wotsatira, Mboniyo inapita kuofesi ya katswiriyo ndikuphunzira Baibulo ndi mkaziyo iye alipo.

Pambuyo pa phunzirolo, katswiri wa matenda amisalayo anauza Mboniyo kuti: “Kwa zaka zambiri ndakhala ndikusonyeza chikondwerero m’zipembedzo za odwala anga, koma ndinawona kuti panalibe chilikizo lenileni limene linaperekedwa ndi chipembedzo chirichonse. Komabe, kwa inu, zinthu nzosiyana. Akazi a P​——​ amabwera kuno kaŵiri pamlungu kaamba ka kufufuza, ndipo amandilipira. Komabe, inu mukuchita ntchito yabwinoko kwaulere ndi chiphunzitso chanu cha Baibulo ndi uphungu wabwino. Iye akupanga kupita patsogolo kwabwino. Pitirizanibe, ndipo ndikukutsimikizirani za chilikizo langa lokwanira ngati mungalifune.”

Baibulo limati: ‘Odala anthu odziŵa liwu la lipenga; ayenda m’kuunika kwa nkhope yanu, Yehova. Akondwera m’dzina lanu tsiku lonse.’ (Salmo 89:15, 16) Mboni ya Yehova iriyonse imadziŵa kuti salmo limeneli nlowona. Pakamwa pawo pamatuluka mfuu yachimwemwe ku chitamando cha Yehova. Anthu ankhaninkhani akutuluka mwa amitundu kuti atamande Mulungu limodzi nawo. Kodi bwanji osayanjana nawo ndikusangalala ndi chimwemwecho inu eni?

[Chithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu nzosangalala tsopano ndi ufulu wawo watsopano wakulandira ndi kuphunzira “Nsanja ya Olonda” m’zinenero zawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena