Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 1/1 tsamba 3-4
  • Mtundu Wachimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtundu Wachimwemwe
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtundu Wachimwemwedi
  • Mtundu Wachimwemwe Wamakono
  • Yehova Ndi Mfumu
    Imbirani Yehova Mosangalala
  • Yehova ndi Mfumu Yathu
    Imbirani Yehova
  • Tumikirani Yehova ndi Chimwemwe cha Mtima
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Chimwemwe cha Yehova Ndicho Linga Lathu
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 1/1 tsamba 3-4

Mtundu Wachimwemwe

MTUNDU wachimwemwe! Kodi kalongosoledwe kameneka kakuyenerera mtundu uliwonse wa anthu lerolino? Kodi mtundu uliwonse unganene mwachimwemwe kuti wachotsa chiwawa, upandu, umphaŵi, kuipitsa, matenda opundula, kuipitsa kwa ndale zadziko, ndi chidani chachipembedzo? Kodi mtundu uliwonse umapereka chiyembekezo chenicheni chakufikiritsa zonulirapo zimenezo? Kutalitali!

Bwanji ponena za mkhalidwe wa dziko lonse? Mikhail Gorbachev, pulezidenti wa U.S.S.R., ananena motere pa July 16 yapita: “Tikuchoka m’nyengo ina ya maunansi amitundu yonse, ndipo tikuloŵa mu ina, imene ndikuganiza kuti ndinyengo ya mtendere wamphamvu, wokhalitsa.” Komabe, magazini a Time a tsiku limodzimodzilo anasimba kuti United States idakalozetsabe zida zanyukliya zokwanira 120 pa Moscow, chimodzi chokha cha izo chingapululutsiretu mzindawo. Ndipo mosakaikira anthu a ku Soviet ngokonzekera kubwezera. Pokhala ndi mamembala ambiri a Mitundu Yogwirizana okhoza kupanga zida zanyukliya tsopano, pali chimwemwe chochepa polingalira za amene angakhale woyamba kukhala wachimwemwe kuziphulitsa.

Mtundu Wachimwemwedi

Panthaŵi ina m’mbiri​—zaka 3,500 zapitazo​—padali mtundu wachimwemwedi. Anali Israyeli wakale. Pamene Mulungu anapulumutsa anthu amenewo kuchitsenderezo cha Igupto, iwo anagwirizana ndi Mose m’kuimba nyimbo yachilakiko yachisangalalo, ndipo anapitiriza kusangalala kwautali umene anamvera Mulungu wawo ndi Mpulumutsi.​—Eksodo 15:1-21; Deuteronomo 28:1, 2, 15, 47.

Mu ulamuliro wa Solomo ‘Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.’ Imeneyo idali nthaŵi yakukondwera kwakukulu, yofika pachimake ndikumangidwa kwa imene mwinamwake inali nyumba yaulemerero koposa m’mbiri yonse, kachisi wa kulambiridwa kwa Yehova m’Yerusalemu.​—1 Mafumu 4:20; 6:11-14.

Mtundu Wachimwemwe Wamakono

Israyeli wakale anachitira chithunzi mtundu wamakono. Utiwo? Kodi ndi Israyeli wandale zadziko wa ku Middle East? Malipoti a nyuzi akusonyeza kuti mtundu wolimbana ndi ina umenewo ulibe chimwemwe konse. Kodi Mitundu Yogwirizana yabweretsa chimwemwe chenicheni ku maboma omwe ndimamembala ake? Ayi, chimwemwe chowona sichikupezeka konse pakati pa mitundu yandale zadziko ya lerolino. Umbombo, kupereka ziphuphu, ndi kusawona mtima n’zofalikira, ndipo m’maiko ambiri anthu wamba amavutika mopanda chimwemwe kokha kuti akhale ndi moyo.​—Miyambo 28:15; 29:2.

Komabe, pali mtundu umodzi wozizwitsa lerolino umene uli ndi chimwemwe chachikulu. Iwo siwandale zadziko, popeza kuti Mtsogoleri wake, Kristu Yesu, ananena motere ponena za anthu ake: “Simuli a dziko lapansi.” (Yohane 15:19) Pamene kuli kwakuti Mitundu Yogwirizana njogwirizana mwa dzina lokha, mtundu wachimwemwe umenewu umatenga achilikizi ake okonda mtendere kuchokera mwa ‘mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ (Chibvumbulutso 7:4, 9) Iwo tsopano waposa mamiliyoni anayi, kotero kuti chiŵerengero cha anthu ake n’chachikulu kuposa cha mamembala 60 a mitundu 159 ya UN. Zinenero za nzika za anthu mamiliyoni anayi ameneŵa zimakwanira pafupifupi 200; komabe onse ngwogwirizana polankhula “chinenero choyera.”​—Zefaniya 3:9, NW.

Kodi sichachilendo kuti anthu amiyambo yambiri yosiyanasiyana yoteroyo angamalankhule chinenero chimodzi? Osati kwenikweni, popeza kuti chinenero chimodzi chogwirizanitsachi chimaphatikizapo uthenga wa Ufumu wolungama wa Mulungu ukudzawo. Mtundu wachimwemwe umenewu umachokera ku “malekezero a dziko lapansi” ndipo ukudziŵika padziko lonse monga ‘Mboni za Yehova.’ (Yesaya 43:5-7, 10; Zekariya 8:23) Pafupifupi kulikonse kumene mungapite pankhope ya dziko lino, mudzawapeza iwo.

Pa Yesaya 2:2-4, mneneri wa Mulungu akulongosola khamu limene likutuluka m’mitundu yonse, namati: ‘Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.’ Mwachangu, awa amaitananso ena kudzalandira malangizo ochokera kwa Yehova kupyolera m’Mawu ake, Baibulo, kuti nawonso aphunzire kuchita chifuniro chake. Mtundu umodzi umenewu umatsatira njira ya mtendere weniweni, popeza kuti anthu ake anasula kale ‘malupanga kukhala zolimira ndi nthungo kukhala anangwape, osaphunziranso nkhondo.’ Mtundu wachimwemwedi!

Nanunso mungakhale ndi phande m’chimwemwechi. Mungaphunzire za tsiku lomayandikira mofulumira pamene Mfumuyo, Kristu Yesu, adzachotsa anthu ndi maboma owononga ndikubwezeretsa Paradaiso pa dziko lapansi. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Ngakhale tsopano lino, monga mtundu wogwirizanadi, Mboni za Yehova zimapeza chimwemwe chachikulu m’ntchito yawo yokonzekera kaamba ka nyengo yaulemerero ya mtendere weniweni imeneyo, monga momwe masamba otsatirawa adzasonyezera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena