Anthu a ku Guatemala Akupatira Mbiri Yabwino
MAPIRI obiriŵira ndi zitunda zazikulu za matanthwe otentha a pansi panthaka zikuwonekera mwadzidzidzi patali pamene ndege ikuyandikira likulu la dzikolo. Okweramo ku mbali imodzi akuyang’ana kunja pa mazenera awo ndi kuwona Phiri la Pacaya likuphulika, ndi kutulutsa utsi wochuluka umene ukupanga mzera umene ukukwera ndi kusungunuka mumlengalenga. Okweramo ku mbali inayo akuyang’ana pansi ndi kuwona mabwato aang’ono ndi mabwato aakulu akudutsa mwabata Nyanja ya Amatitlán. Imeneyi ndiyo Guatemala, dziko la kusiyana kwakukulu.
Yokhazikitsidwa mu Central America, Guatemala imakuta malo a ukulu wa chifupifupi makilomita 109,000 mbali zonse zinayi. Mkhalidwe wake wa dziko umasiyanasiyana kuchokera ku mapiri okwezeka—kuphatikizapo matanthwe otentha a pansi panthaka 33, 4 a iwo amene akutenthabe—kufika ku nkhalango za kumalo otsika, nkhalango za mvula, ndi nyanja ndi mitsinje ya madzi oyera mbe. Mtunda wa dziko umakwera kuchokera pa nyanja kufika ku mamita 4,211. Mu mzinda wa likulu ladzikolo, muli nyengo ya ngululu yamuyaya, yokhala ndi avereji ya 24° C. ya kutentha chaka chonse. Pamene kuli kwakuti pamwamba m’mapiri kutenthako kungatsike kupitirira mlingo wa kuzizira kowundanitsa madzi, malo a m’mphepete mwa gombe angafikire kutentha kwa 38°C. Limeneli ndi dziko limene lingayenerere chikhumbo cha aliyense, ndi magombe, nkhalango, mapiri, malo owuma, ndi zigwa zopereka zipatso. Ndipo m’malo onse amenewa, mbiri yabwino ya Ufumu ikulalikidwa.
Kulengeza Ufumu Kuyambika
Kulalikira Ufumu kunayamba mu Guatemala chifupifupi chaka cha 1920. M’kupita kwa nthaŵi magulu aang’ono a anthu okondwerera ndi alengezi a Ufumu anayamba kupangika m’mbali zosiyanasiyana za dzikolo. Pamene amishonale aŵiri oyambirira anafika pa May 21, 1945, iwo anapeza chikondwerero chochuluka. Mmodzi akusimba kuti: “Pa Loŵeruka lachiŵiri pambuyo pa kufika kwathu, ndinagamulapo kuchita ntchito ya m’khwalala ndi magazini. Madzulo amenewo ndinanyamuka ndi chola changa chodzala ndi mabukhu, ndipo mu ora limodzi ndi theka, ndinamaliza onse, kugaŵira magazini 32, timabukhu 34, mabukhu 4, ndi Baibulo limodzi.” Mwezi woyamba umenewo iwo anayamba kutsogoza maphunziro a Baibulo a panyumba 17! Mlongo wachimishonale woyambirira kumeneko adakali kulalikirabe motenthedwa maganizo mbiri yabwino ya Ufumu zaka 44 pambuyo pake.
Kusiyana kumakula m’gawo lolalikira. Likulu la dzikolo, Mzinda wa Guatemala, uli ndi zimango zamakono zazitali zambiri, limodzinso ndi malo okhalako abwino koposa ndi nyumba zokongola, kumene ogwira ntchito pa nyumba aakazi amayankha ku khomo mwa kugwiritsira ntchito lamya. Koma kunja kwa bwalo kuli nyumba zomangidwa ndi njerwa zosawotcha ndi madenga a udzu kumene magetsi ndi madzi a m’mipopi ziri kokha maloto. Ndi kusiyanasiyana kodziŵika koteroko kwa gawo, kulibe chinthu choterocho chonga ngati tsiku lozoloŵereka mu utumiki wa m’munda.
M’zaka za posachedwapa zitseko zambiri sizikutsegulidwa chifukwa chakuti ponse paŵiri mwamuna ndi mkazi amapita kukagwira ntchito. Chotero ndi cholinga chofuna kuchitira umboni kwa anthu oterowo, Mboni kaŵirikaŵiri zimatengamo mbali mu ntchito ya m’khwalala. Ena amayamba pa 5:30 a.m., akumagawira mabukhu pa malo oimira mabasi otanganitsidwa. Mboni iyenera kukhala mu mkhalidwe wabwino wakuthupi kuti iyendere limodzi ndi liŵiro la anthu othamangira kukakwera basi yawo. M’mawa mwina gulu la Mboni linagamulapo kufikira oyendetsa matakisi ena chifukwa chakuti kugwirira ntchito pa mizera ya mabasi kunali kumacheperako. Ku kudabwitsidwa kwawo oyendetsa matakisi oŵerengeka anatulutsa makope awo a magazini ya Nsanja ya Olonda ochongedwa kale. Mmodzi kapena aŵiri anali ndi mafunso, amene abalewo anali achimwemwe kuwayankha mwa kugwiritsira ntchito Mabaibulo a oyendetsa matakisiwo.
Kulalikira m’Malo a m’Maphiri
Panajachel uli umodzi wa midzi yozungulira Nyanja ya Atitlán, nyanja yokongola yobiriŵira yozunguliridwa ndi mapiri aakulu ndi matanthwe otentha a pansi panthaka atatu. Midzi ina imatchedwa ndi maina a atumwi. Chifupifupi 95 peresenti ya anthuwo ali a fuko la Mayan, Cakchiquel ndi Tzutuhil zikumakhala ziŵiri za zinenero zazikulu. Pamene kuli kwakuti amuna amalankhulanso Chispanya, ochulukira a akazi samatero, popeza kuti amathera nthaŵi yawo yochuluka pa nyumba. Mudzi uliwonse uli ndi zovala zawo za mwambo zokongola, kaŵirikaŵiri zolukidwa pa manja ndi akaziwo.
Pofika mu Panajachel, mudzawona kuti siiri yofanana ndi matauni ena aang’ono mu Guatemala. Motsatizana ndi nyumba za njerwa zosawotchedwa kapena za njerwa za simenti, mukuwona nyumba zosanjikana. Osiyana ngakhale mokulira ali mahotela amakono. Anthu kuchokera ku mbali zonse za dziko amabwera ku Panajachel kudzakhumbira Nyanja ya Atitlán.
Mboni imodzi ikulongosola mmene ntchito yolalikira ikuchitidwira kumeneko: “Pasadakhale bwato limabwerekedwa kaamba ka malipiro kwa tsiku limodzi, ndipo abale athu kuchokera ku Sololá ya pafupi, limodzinso ndi ena ochezera kuchokera ku Mzinda wa Guatemala, amaitanidwa kuthandiza kukwaniritsa gawo lalikululo. Abale ochokera ku Sololá ali thandizo lalikulu chifukwa chakuti ambiri a iwo amakhala m’malo a mapiri ofanana ndi amene tidzakhala tikuchezera. Iwo amalankhulanso chinenero cha kumaloko. Ulendowo umayambika m’mamawa. Pamene bwato likudutsa nyanja, ana amakhumbira madzi oyera mowala ndipo makolo amayesera mawu oŵerengeka m’chinenerocho.
“Nthaŵi ino midzi isanu idzachezeredwa. Choyamba, magulu atatu akupangidwa. Kenaka akuikidwa aŵiriaŵiri—aja olankhula chinenerocho ndi aja omwe samatero. Pali kokha madoko aang’ono atatu pomwe tingatsikireko kuti tifikire midzi imeneyi, chotero gulu limodzi litsitsidwa pa doko lirilonse. Chiri chotenthetsa maganizo kuwona abale athu m’zovala zawo za kumaloko zokongola akugwirira limodzi ndi aja ovala zovala za mtundu wa kumadzulo. Chimenecho mwa icho chokha chiri umboni wabwino kwambiri kwa anthu a m’mudziwo. Ana ofunitsitsa kudziŵa nthaŵi zambiri amatipatsa moni. Pambuyo popeza cholinga cha kuchezera kwathu, iwo amathamanga napita kukawuza anthu onse a m’mudzi.
“Podzafika nthaŵi imene tifika pa nyumba zodekha, anthu ambiri amakhala akuyembekeza molakalaka kuwona mabroshuwa athu okongola kapena Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo zimene anawo awawuza ponena za izo. Lirilonse la mabukhu a Baibulo losiidwa panyumba yoyambirira lidzakhala lomwe lidzafunsidwa pa nyumba zotsatira chifukwa chakuti aliyense amafuna kukhala ndi chinthu chokongola chofananacho chimene mnansi wake walandira. Ambiri sakhoza kuŵerenga, chotero iwo makamaka amasangalala ndi zithunzithunzi zonena za Paradaiso ikudzayo. Nkhope zawo zisangalala pamene amvetsera ku chiyembekezo kaamba ka mtsogolo chimene Baibulo likulonjeza pa Chibvumbulutso 21:3, 4. Timaima mwachidule kaamba ka kukumana kwa chakudya cha pamasana kosangalatsa ndipo kenaka tipitiriza kulankhula kwa anthu mpaka 3:00 p.m. Kenaka tibwerera ku doko kukayembekezera kaamba ka bwato kutitenga. Pamene aliyense wakwera m’bwato, abalewo mwachimwemwe agawana zokumana nazo zawo.
“Mlongo wina akumbukira chisangalalo chimene anakhala nacho pamene anamva mkazi akuitana mofuula, ‘Mlongo, mlongo, ndiri pano. Mwabweranso kudzandichezera. Zikomo, zikomo kwambiri.’ Iye anayang’ana pamwamba ku malo okwezeka otsatira a phirilo ndi kuzindikira mkazi akumapatsa moni mwa kugwedeza dzanja mwa chisangalalo. Nthaŵi yapita pamene anachezera mudziwo, mkaziyo anali atasonyeza chikondwerero chachikulu pamene analingalira Baibulo limodzi. Mkaziyo anali kuyembekezera kubwerera kolonjezedwako. Iwo anakhalanso pansi ku phunziro la Baibulo lina losangalatsa.
“Ngakhale kuti aliyense ali wotopa kaamba ka kuyenda maulendo aatali pa malo a m’mapiri a miyala, iwo ali olakalaka kudziŵa pamene ulendo wotsatira udzakhala. Pamene bwatolo lifikira gombe, titsanzikana wina ndi mnzake ndi ndemanga zonena za nthaŵi yathu yotsatira yosangalatsa.”
Kutsikira ku Malo Otsika a Mphepete mwa Gombe
Guatemala irinso ndi magawo a gombe aŵiri osiyana: gombe la Pacific lokhala ndi madoko ake a mchenga wakuda osangalatsa ndi a gombe la Caribbean lokhala ndi m’chenga wake woyera.
Mkati mwa kuyendetsa galimoto kwa mphindi 45 kuchokera ku likulu la dzikolo kulinga ku Pacific, kusintha kwa malo ozungulira ndi mtunda kuli kwakukulu. Mphepo yotentha ndi yachinyontho imafalikira m’malo a m’mphepete mwa gombelo, motsagana ndi kuchuluka kwa tizirombo. Mitengo ya kanjedza, ngole, ndi ceiba limodzi ndi unyinji wa zomera imapereka umboni wakuti muli m’malo otentha. Kuli mipingo yaikulu ya Mboni za Yehova mu ambiri a matauni m’gawolo.
Kuno njinga yaloŵa m’malo kavalo wa nthaŵi zonse, chotero sichiri chachilendo kuwona abale athu akupalasa mofulumira kupyola minda ya nzimbe pamene akuchitira umboni kuchokera ku msasa ndi msasa. Mbale wina anatsogoza phunziro la Baibulo ndi mwamuna yemwe anali kukhala makilomita 35 kutali. Mlungu ndi mlungu iye ankapanga ulendo pa njinga yake kuwirikiza kaŵiri mtunda umenewo kukaphunzitsa chowonadi cha Baibulo kwa munthu wokondwerera ameneyu.
Inu mungaganize kuti mwaloŵa m’dziko lina ngati muchezera madoko a kunyanja aŵiri a Santo Tomas de Castilla ndi Puerto Barrios pa doko la Caribbean. Njira ya moyo iri yosiyana ndi mbali ina iriyonse ya Guatemala. Nyumbazo ziri ndi kapinga ndi maluŵa owonekera kwa onse; simungapeze kaŵirikaŵiri chipupa cha njerwa zosawotchedwa mozungulira malo, chimene chiri chizindikiro chosiyanitsa cha Mexico ndi Central America. Kuwonjezerapo, simungapeze kuno zovala za kumaloko zimene ziri zofala chotero mu Guatemala yonse.
“Chifukwa iyi iri tauni ya kudoko, muli ndi mwaŵi wa kulongosola uthenga wa Baibulo kwa anthu a mtundu uliwonse,” analongosola tero mtumiki wa nthaŵi zonse wina. “Ndinayenda kupyola zitseko zotsegukira mbali zonse za bawa ina. ‘Madamu’ anatenga chogaŵira cha bukhu ndi Baibulo, ndipo anandiitanira kubwerera kukamphunzitsa mmene angaziphunzirire izo. Pamene ndinabwerera mlungu wotsatira, iye anali kudikira pa tebulo lalikulu wokhala ndi Baibulo ndi bukhulo. Akumapanga kulozera kwaubwenzi ndi dzanja kuti ndikhale pansi, anandiwuza kuyembekeza kwa kamphindi pamene anaitana ‘atsikana’ onse. Iye anafuna iwo kuphunzira nawonso. Ndisanadziŵe chimenecho, tebulo lonse linazungulidwa ndi ‘atsikana’ ake. Akumatembenukira kwa ine, ananena kuti, ‘Tsopano tisonyezeni mmene tingaphunzirire Baibulo.’ Ndinalingalira kuti: ‘Kodi ndimotani mmene ndadziloŵetsera inemwini munomu?’ Koma mwa bata ndinapitirizabe, ngati kuti nthaŵi zonse ndinaphunzira Baibulo m’bawa.” Madamuyo anapita patsogolo mofulumira, kuleka ntchito yake, ndi kukhala Mboni yobatizidwa. Lerolino iye ali wokangalika mu mpingo wina ndipo iyemwini akutsogoza maphunziro a Baibulo ndi anthu okondwerera.
Ulendo wa ora limodzi ndi bwato kudutsa chikwekwe pali tauni yowoneka mokongola ya Livingston, mudzi wachete wa anthu aubwenzi amene akhala osonkhezeredwa mwamphamvu ndi kukhulupirira malaulo ndi nyanga za mu Africa. Sichachilendo kumeneko kumva kulira kwa ng’oma nthaŵi ya usiku ndi kuwona mtundu wa kavinidwe wa Chiafrica m’makwalala mkati mwa mapwando. Inu mungazindikirenso katchulidwe ka mawu kamene kali kachilendo ku makutu—Caribe, kapena Garifuna. Gulu laling’ono koma lokula mofulumira la alengezi a Ufumu amatumikira zikondwerero zauzimu za anthu kumeneko.
Chiwawa ndi Chizunzo Zisiyana Ndi Mtendere
Mavuto ena anabuka mu 1982 pamene prezidenti watsopano wa Guatemala anayesera kupondereza machitachita a gulu la chiweniweni lomwe linawonjezeka mu mphamvu mkati mwa utsogoleri wa woloŵedwa m’malo ndi iye. Cholinga chake chinali kupanga magulu oyendera m’bomalo okhala ndi anthu wamba okonzekeretsedwa ndi zida omwe anayendera makwalala usiku, kutetezera matauniwo ndi kuchenjeza asilikali za m’chitidwe uliwonse wokaikiritsa. M’malo ambiri gulu loyendera la anthu wamba limeneli linatsimikizira kukhala chiyeso cha uchete wa abale athu.
Mu tauni imodzi mpingo wonse unadidikizidwa kuti upandukire uchete wawo Wachikristu mwa kutengamo mbali m’machitachita a kuyendera. Atawopsyezedwa ndi imfa, iwo anathaŵira ku likulu la dziko, kumene anapatsidwa malo okhala pa Nyumba ya Ufumu kufikira atayikidwa m’nyumba za abale. Inde, abale ambiri apirira ziyeso zowopsya ndi chizunzo pamene asilikali anayesera kuwakakamiza iwo kuyendera.
Mbale mmodwzi akusimba kuti: “Ndine wa zaka 20 zakubadwa ndipo ndimakhala ndi mbale wanga ndi mkazi wake. Mavuto anga anayambika pamene ntchito ya gulu la chiweniweni ndi ya asilikali inafika pa farmu pamene ndinkagwira ntchito. Pa nthaŵi ina, pamaso pathu penipeni, anthu asanu ndi atatu anatengedwa mwa kulozedwa ndi mfuti. Kokha aŵiri anabwerera; asanu ndi mmodzi enawo sanawonedwe kachiŵiri.
“Mu April 1984 magulu a asilikali anabwera pa farmu kudzafuna antchito atsopano. Iwo anafunsa antchito anzanga ndi ine kuti tigwirizane nawo. Pamene ndinakana, iwo anandimenya mosalekeza. Pakuwona chimenechi, antchito anzanga analira ngati ana, akundipempha ine kuti nditenge chida ndi kugwirizana nawo. Msilikali mmodzi anajinya zala zake m’khosi mwanga ndi kupotoza makutu anga pamene winayo anandigwiririra kotero kuti winanso andiwombe mbama ndi kundikantha. Ndunayo inafuula mwaukali kuti, ‘Nchiyani cholakwika ndi iwe? Kodi ndiwe nyama, kapena kodi ndiwe Mulungu?’ Pomalizira nduna ina inafika ndi kunena kuti, ‘Musiyeni chifukwa ndi mmene Mboni ziriri. Sangagonjere mpaka mutawapha.’ Nduna yoyambayo inati, ‘Muwombereni mfuti!’ Koma m’malomwake anandibaya m’mimba ndi kumbuyo kwa mfuti yake. Pamene iwo anakhutiritsidwa kuti sindikagwirizana nawo, analeka kundimenya. Pambuyo pa masiku atatu, anandimasula. Ndi thandizo la Yehova sindinaswe umphumphu wanga. Ndicho chifukwa chake ndimawuza achichepere ena kukhala ndi chidaliro chochuluka mwa Yehova, yemwe adzatithandiza kukhala ndi chipiriro pamene tichifunikira icho.” Mwachimwemwe, mkhalidwewo unasintha mokulira pambuyo pakuti prezidenti watsopano anatenga malo mu January 1986.
Posachedwapa kwenikwnei kusiyana kwa nkhondo ndi mtendere, chuma ndi umphaŵi, imfa ndi moyo, kudzazimiririka kosatha. Mu Paradaiso irinkudza ya chiwunda chonse, kusiyana kosangalatsa kwa usiku ndi usana, mapiri ndi zigwa, nyanja za mkokomo ndi nyanja za bata, zidzasangalalidwa monga mmene Yehova Mulungu anafunira. Mungakhale kumeneko nanunso ngati, mofanana ndi alengezi a Ufumu ena oposa zikwi khumi a ku Guatemala, mukupatira mbiri yabwino ndi mtima wonse.