Chizunzo mu Burundi—Lonjezo Losweka la Ufulu Wachipembedzo!
Ufulu wachipembedzo umatengedwa mosasamala m’maiko ambiri a Kumadzulo. Ngakhale kuli tero, chizunzo chachipembedzo chomwe chikuchitika m’dziko la mu Africa la Burundi chikuchitira fanizo mmene ufulu umenewo ungakhalire wokhoza kusweka. Ndithudi, malinga ngati kuyenera kwakukulu kwa munthu kwa gulu lirilonse la anthu kukuponderezedwa, palibe kuyenera kwa wina aliyense kumene kuli kwa chisungiko. Chotero tikufulumiza aŵerengi athu kusanthula chimene chikuchitika mu Burundi.
FEBRUARY 16, 1989, inawona chithunzi cha Nyengo Zakuda chikugwera pa dziko la mu Africa la Burundi. Pa deti limenelo prezidenti wa Republic of Burundi, Pierre Buyoya, anapangitsa msonkhano ndi abwanamkubwa a madera. M’kukambitsirana kwa kukumana kumeneko, chizunzo chachipembedzo chofalikira, choipitsitsa, chinabuka motsutsana ndi Mboni za Yehova. Amuna, akazi, ndipo ngakhale ana mwamsanga anakhala minkhole ya kumangidwa, kumenyedwa, kuzunza, ndi kumanidwa chakudya kosakhala kwa lamulo.
Kuti nkhalwe zoterozo zingachitike m’tsiku lino ndi nyengo chiri mwa icho chokha chamanyazi. Ngakhale kuli tero, chizunzo cha ku Burundi cha Akristu chiri chokwiyitsa mwapadera. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti icho chiri kulakwira lonjezo la ufulu wachipembedzo.
Kulakwira kwa Boma
Burundi liri mtundu wa mkati mwenimweni wa Africa wokhazikitsidwa kokha kum’mwera kwa equator, ngakhale kuti dziko la mapiri limeneli limasangalala ndi mkhalidwe wa mphepo wozizirira, ndi wosangalatsa. (Onani mapu.) Anthu ochepera kuzungulira dziko ndi amene anadziŵa za kukhalapo kwa Burundi kufikira mu August 1988, pamene linakhala pa mitu ya nkhani za dziko. Pa nthaŵi imeneyo mkangano wokhetsa mwazi unabuka pakati pa mitundu ya magulu aŵiri a mafuko ake aakulu, Tutsi ndi Hutu. Ichi mosakaikira chinasiya chithunzi choipa cha Burundi pa maganizo a ambiri.
Mosasamala kanthu za icho, pali zinthu zabwino zambiri zofunikira kunenedwa ponena za dziko lopita patsogolo limeneli. Anthu ake ali a maluso ndi ogwira ntchito molimba. Nkhani mu The New York Times Magazine mowonjezereka ikunena kuti “m’njira zosiyanasiyana zowonekeratu kwa wochezera, dziko la Burundi, losauka monga mmene liliri, limagwira ntchito. Maurice Gervais, nzika yoimira ya World Bank, akulitcha ilo ‘dziko logwira ntchito moposerapo.’”
Mkhalidwe wachipembedzo wa Burundi, ngakhale kuli tero, ukuwopsyeza kawonedwe kabwino kameneka. Chifupifupi 80 peresenti amadzinenera kukhala Akristu, unyinji wa iwo a Roma Katolika. Komabe, mabungwe a ndale zadziko kumeneko akhazikitsa chitsanzo chovutitsa cha kusalekerera kwachipembedzo. Pa October 16, 1985, The Christian Century inasimba kuti: “Kwa chaka chapita boma la Burundi lakulitsa mpambo wa machitidwe olinganizidwa pa kuzimiriritsa kukhalapo kwa tchalitchi . . . Kuyenera kwa kulambira kwapoyera ndi kwaumwini ndipo pemphero lachepetsedwa mokulira. Matchalitchi onse a magulu ena . . . atsekedwa ndi kuletsedwa kugwira ntchito; . . . unyinji wa Akristu mwaumwini aikidwa m’ndende, ena ngakhale kuzunzidwa . . . onsewo kaamba ka kuchita kuyenera kwawo kwachipembedzo.”
Ziyembekezo chotero zinakulirako pamene, mu September 1987, boma latsopano pansi pa utsogoleri wa Prezidenti Pierre Buyoya linayamba kulamulira mu Burundi. Prezidenti watsopanoyu analonjeza mtundu wake ufulu wachipembedzo, ndipo mwamsanga anatenga masitepi kukhalitsa bwino mawu ake. Ripoti loperekedwa ndi Dipatimenti ya Boma la U.S. linanena kuti: “Mkati mwa chaka chake choyamba mu ofesi, Prezidenti Buyoya anapanga masinthidwe ofulumira m’malamulo a Burundi kulinga ku chipembedzo cholinganizidwa, kuchotsapo kupondereza kwa kulankhula kwa chipembedzo pansi pa ulamuliro [wakale]. Buyoya anamasula andende achipembedzo onse; kutsegulanso matchalitchi otsekedwa; kubwezeretsa zinthu zolandidwa zonse za tchalitchi.” Machitidwe owunikira amenewa anapezera Prezidenti Buyoya kukwezedwa ndi okonda ufulu kuzungulira dziko lonse.
Nchifukwa ninji, kenaka, chimene Mboni za Yehova posachedwapa zinasankhidwa monga chandamale cha kupondereza kwachipembedzo?
Mboni za Yehova—Zimenyera kaamba ka Kuzindikiridwa
Kwa zaka makumi angapo, Tchalitchi cha Chikatolika “chinasintha kukhala magwero amphamvu m’zachuma ndi ndale zadziko,” ikusimba tero The New York Times. M’masiku akumbuyo a kulamuliridwa ndi mphamvu za kunja, tchalitchi chinaloledwa “m’chenicheni kulamulira dzikolo,” popeza kuti “chinachita mbali yaikulu m’kupereka chisamaliro cha umoyo ndi maphunziro.” Nchosadabwitsa, kenaka, kuti bomalo lingakhale linadzimva lowopsyezedwa ndi chipembedzo cholinganizidwa.
Ngakhale kuli tero, pamene Mboni za Yehova zinayamba ntchito yawo ya kulalikira poyera mu Burundi mu 1963, iwo sanapange kuyesera kwa kusokoneza ndi zochita za Boma. M’malomwake, iwo anasungilira ntchito yawo ku kulalikira “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Popeza kuti Baibulo limanena kuti Akristu owona safunikira kukhala “mbali ya dziko,” Mboni za Yehova zinakhala zauchete ku ndale zadziko, kaimidwe kotengedwa ndi Mboni kuzungulira dziko lonse.—Yohane 17:16, NW.
Mbonizo zinakana molimba mtima kudziloŵetsa m’zipani za ndale zadziko ndi kufuula mawu onyada a chipani cha ndale za dziko. Maboma kaŵirikaŵiri amvetsetsa molakwa kaimidwe kauchete kameneka kukhala kusoŵeka kwa kunyadira dziko lawo kapena ngakhale kuwunikira kuwukira boma. Koma mmenemo simmene ziliri. Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zikudziŵidwa kukhala nzika zomvera lamulo, za chitsanzo chabwino. Iwo amatenga mosamalitsa lamulo la Baibulo la “kumvera” maboma a ku dziko. (Aroma 13:1) Ngakhale kuti amakana kuchita sawatcha kapena njira ina iriyonse kusonyeza ulemu kaamba ka zizindikiritso za mtundu zonga ngati mbendera, iwo samachita ndi zizindikiro zimenezi mopanda ulemu.—Eksodo 20:4, 5.
Mu 1975 Mboni za Yehova zinapempha kuzindikiridwa kwa lamulo kwa ntchito yawo. Koma mu 1976 kuwukira kwa asilikali kunalanda boma ndi kuika Prezidenti Jean–Baptiste Bagaza mu ulamuliro. Iye analonjeza ufulu wa kulambira. Komabe mu March 1977, Mboni za Yehova zinaletsedwa mwa lamulo! Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zinayesayesa kumveketsa nkhaniyo kwa ziŵalo za boma la Bagaza, koma makalata, kuchezera maofesi a akazembe a Burundi mu France ndi Belgium, ndi kukumana ndi nduna za boma mu Burundi zonsezo sizinaphule kanthu. Mu 1987 Mboni zina 80 mu Burundi—amuna ndi akazi—anaponyedwa m’ndende kwa miyezi ingapo. Mboni imodzi inafa mmenemo.
Kenaka mu 1987 kuwukira boma kunabweretsa Major Pierre Buyoya pa ulamuliro. Akatolika ndi Aprotesitanti mwamsanga anapindula kuchokera ku kulekerera kwake kwa chipembedzo—koma osati Mboni.
Kuwulika kwa Chizunzo Chachipembedzo
Kutsatira kukumana kwa Prezidenti Buyoya ndi abwanamkubwa a madera pa February 16, 1989, chinalengezedwa pa wailesi kuti limodzi la mavuto aakulu amene Burundi inayenera kuyang’anizana nawo linali kufutukuka kwa Mboni za Yehova. Monga ngati kuti akuchita motsatizana, abwanamkubwa a madera amkati anayambitsa funde la chizunzo. Ngakhale kuti tsatanetsatane adakali wosakwanirabe, maripoti otsatirawa amapatsa lingaliro la chimene chikuchitika kumeneko:
Dera la Gitega: Bwanamkubwa Yves Minani analamula kuti apolisi ndi anthu apange magulu kumanga Mboni za Yehova zonse. Pambuyo pake, nthumwi za polisi ya chisungiko zinathyola ndi kuloŵa m’nyumba ya Ntibatamabi Edmond, mlengezi wachipainiya wapadera, ndi kum’manga iye. Pamene iye anali m’kubindikiritsidwa, anamanidwa chakudya. Nthaŵi zambiri iye anakomoka ndi njala. Iye anazunzidwanso m’kuyesera kumpangitsa iye kutsimikizira mphekesera yakuti Mboni za Yehova zimadya mwazi wa anthu—bodza lamkunkhuniza!
Pambuyo pa kumangidwa kwa Edmond, Ntikarahera Aaron ndi Ntimpirangeza Prime, nawonso Mboni za Yehova, anamangidwa ndi kuikidwa m’ndende mu Gitega. Iwo anachitiridwa mwankhalwe mofananamo.
Nijimbere Charlotte, mkazi wa woyang’anira wadera—mtumiki woyendayenda yemwe amachezera unyinji wa mipingo—anamva za tsoka la abale ake Achikristu. Iye anayesera kupereka chakudya kundendeko koma anamangidwa pa March 16, 1989, ndi kusungidwa monga chigwiriro m’kuyesera kwa maulamuliro kuti agwire mwamuna wake.
Dera la Muramvya: Bwanamkubwa Antoine Baza anatumiza mauthenga kwa Mboni zodziŵika zonse kukumana naye ndi kuyankha mafunso. Pa March 4 gulu linalabadira kuitanako. Ngakhale kuti anali kuyankha mafunso ake mwaulemu, iwo anakana kufuula mawu onyada a chipani cha ndale zadziko.
Mochitapo kanthu bwanamkubwayo anasonkhezera anthu a kumaloko kuwukira Mboni za Yehova. Pa March 16 apolisi analoŵa m’nyumba za Mboni zodziŵika ndi kuyamba kumenya amuna ndi akazi chifukwa chokana kufuula mawu onyada a chipani. Sitolo ina ya Mboni inalandidwa ndi kutsekedwa—kutsekereza kakhalidwe ka moyo ka banjalo.
Pa March 17 akazi anayi anamenyedwa chifukwa chakuti anakana kukana chikhulupiriro chawo. Iwo anaikidwa m’chipinda cha ndende chopanda poloŵera mpweya, ngakhale kuti mmodzi wa iwo anali mayi wa khanda la masiku 20 akubadwa.
Pa March 20 gulu lokonzekeretsedwa ndi ndodo ndi matochi linathyola ndi kuloŵa m’nyumba za Mboni zazikazi zina, zomwe zinamenyedwa ndi kuthamangitsidwa m’nyumba zawo. Pakati pa owopsyezedwawo panali mkazi wa zaka 75 zakubadwa yemwe anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndi chiŵerengero cha achichepere a msinkhu wa zaka za pansi pa 14!
Pierre Kibina-Kanwa, mtsogoleri wa sukulu ya pulaimale ya pa Nyabihanga, anayesera kukakamiza ana a Mboni a pa sukulu kupereka sawatcha ku mbendera ya mtundu. Polephera kutero, iye anawathamangitsa iwo. Mboni makumi aŵiri mphambu ziŵiri kuchokera ku tauni imeneyo zinakakamizidwa kuthaŵa, kusiya chirichonse chomwe anali nacho. Pakati pa awo omangidwa panali Ndayisenga Leonidas, Kanyambo Leanard, Ntahorwamamiye Abednego, Bankangumurindi P., Kashi Grégoire, ndi Mbonihankuye Thadée.
Dera la Bujumbura: Wolamulira wa bungwe la m’mudzi wa Muhuta, Nahimana Macaire, anaitanitsa Kavunzo Vincent, Ndabazaniye Sylvestre, ndi Ndizwe-Nzaniye—onse omwe ali Mboni—ku msonkhano. Kumeneko iye anawapatsa mlandu wa kukhala oloŵetsedwamo m’kukanthana kwa magulu aufuko kwa mu August 1988. Ngakhale kuti Mboni za Yehova mowonekera sizinali zoloŵetsedwamo, kumenyedwa ndi kumangidwa kunatsatira.
Dera la Bubanza: Mboni ziŵiri zinamangidwa kokha chifukwa cha kukhala ndi mabukhu a Baibulo. Pamene iwo anakana kupereka sawatcha ya chipani, Bwanamkubwa Kimbusa Balthazar anawatumiza iwo ku msasa wa asilikali. Kumeneko iwo anazunzidwa mwa kuwatswanya dzala.
Chimene Inu Mungachite
Kochuluka kwa kuchitiridwa moipa kumeneku kwachitikira mkati mwenimweni mwa dziko, kutali ndi maso a openyerera a maiko ena. Ngakhale kuli tero, makope oposa pa 13 miliyoni a nkhani ino adzagawiridwa kuzungulira dziko lonse m’zinenero 106. Nkhanza za ku Burundi sizidzakhalanso zamseri. Anthu okonda ufulu adzadabwitsidwa kuti kulakwira kuyenera kwa munthu koipitsitsa koteroko kukuchitika—kuyenera kumene mazana a anthu mu Africa akhala akumenyera.
Burundi chotero ikukhala pa ngozi mokulira ya kulephera kusunga lonjezo lake la ufulu wachipembedzo. Iyo ikukhala pa ngozi ya kuwononga kutchuka kumene yagwirira ntchito molimba chotero kukukhazikitsa, kuja kwa mtundu wopita patsogolo, wogwira ntchito molimba. Kodi Burundi imafuna vuto la kuwonedwa kukhala mtundu wa ozunza mopanda chifundo a chipembedzo? Sitiganizira tero. Tikungolingalira kuti Prezidenti Buyoya wadziŵitsidwa molakwika, kusocheretsedwa ndi alangizi ake.
Milandu yoikidwa motsutsana ndi Mboni za Yehova iri mabodza kotheratu olinganizidwa kuputa udani wosalingalira. Mboni za Yehova siziri chiwopsyezo ku chisungiko cha boma la Burundi kapena mtundu wina uliwonse. Iwo ali a mtendere ndi osunga lamulo, aulemu ku zizindikiritso za mtundu. Mosemphana ndi mphekesera, iwo amakana kotheratu kutenga mwazi mu mtundu uliwonse—ngakhale pamene miyoyo yawo iri pa ngozi.—Machitidwe 15:28, 29.
Akristu owona kuzungulira dziko lonse chotero adzapemphera mogwirizana kaamba ka abale awo mu Burundi. (1 Timoteo 2:1, 2) Aŵerengi ambiri nawonso adzasonkhezeredwa kulemba mwachindunji kwa Prezidenti Pierre Buyoya, akumapempha mwaulemu kuti kuzunza kwa chipembedzo kuimitsidwe ndi kuti Mboni za Yehova zilandire kuzindikiridwa kwa lamulo monga chipembedzo chokhazikitsidwa. Burundi iyenera kuyankha ku chifukwa ngati ifuna kudziwombola m’maso mwa dziko.
His Excellency Major Pierre Buyoya
President of the Republic of Burundi
Bujumbura
REPUBLIC OF BURUNDI
[Mapu patsamba 22]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
RWANDA
ZAIRE
BURUNDI
TANZANIA
LAKE TANGANYIKA