Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 4/15 tsamba 3-4
  • Pamene Ana Akhala ndi Ana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Ana Akhala ndi Ana
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunafuna kaamba ka Mayankho
  • Vuto Lapadziko Lonse la Atsikana Otenga Mimba Ali Aang’ono
    Galamukani!—2004
  • Kuchotsa Mimba Si njira yabwino
    Galamukani!—2009
  • Kutaya Mimba—Kodi Ndiko Yankho?
    Galamukani!—1995
  • Kukhala ndi Pakati kwa Azaka Zapakati pa 13 ndi 19 Kodi Msungwana Angachitenji?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 4/15 tsamba 3-4

Pamene Ana Akhala ndi Ana

“IYE ANAWONEKA ngati chinachake chochokera ku nthano,” mkazi wachichepere amene tidzamutcha Sharon anakumbukira mowawidwa mtima. “Iye anali kundiwuza ine nthaŵi zonse kuti anandikonda ndipo kuti ngati bwenzi lake lachikazi likakhala ndi pakati, iye sadzakhoza kumusiya.”

Tsiku lina Sharon anayendera dokotala wake kukafufuza chimene anaganiza kuti chingakhale kutupa kwa kolekezera matumbo akulu (appendix); chinachitika kuti iye anali ndi pakati pa miyezi itatu. “Ndinaitana bwenzi langa lamwamuna mwamsanga,” Sharon akukumbukira tero. Chivomerezo chake? “Uyenera kuchotsa mimbayo! Tangoichotsa iyo!” Nthanoyo inakhala loto.

Chifupifupi miliyoni imodzi ya atsikana a zaka za pakati pa 13 ndi 19 mu United States mokha amakhala ndi pakati chaka chirichonse. United States iri ndi kusiyana koipa kwa kukhala ndi chiŵerengero chapamwamba koposa cha mimba za apakati pa zaka za 13 ndi 19 pakati pa maiko otukuka​—dziko lokha limene chiŵerengerocho chawonjezereka m’zaka za posachedwapa. Komabe, phunziro la maiko 37 lochitidwa ndi The Alan Guttmacher Institute lavumbula kuti mimba pakati pa achichepere a zaka za pakati pa 13 ndi 19 osakwatiwa liri vuto la dziko lonse.

Analemba tero ofufuza Black ndi DeBlassie m’magazini ya Adolescence: “Atsikana a msinkhu wopita ku sukulu amene amakhala ndi pakati amabwera kuchokera ku magulu onse amayanjano a za chuma ndiponso kuchokera ponse paŵiri ku masukulu aboma ndi apadera. Mafuko onse, zikhulupiriro zonse, ndi mbali zonse zadziko, mbali ya ku midzi ndi m’matauni, amaimiridwa.” Ponena za chifukwa chimene liŵiro la kubala liri lokulira pakati pa atsikana ochokera ku mabanja osawuka kapena ochepa, Journal of Marriage and the Family ikunena kuti: “Azungu ndi atsikana ochokera ku mabanja A[mayanjano] A[chuma] A[pamwamba] kaŵirikaŵiri amachotsa mimba.”

Mu United States, akazi osafika zaka 20 za kubadwa anaŵerengera kaamba ka magawo atatu akuchotsa mimba kwa lamulo konse. Ataika pambali malingaliro a makhalidwe abwino, chosankha cha kuchotsa mimba kaŵirikaŵiri chimatsimikizira kukhala chovuta kukhala nacho. “Ndikhulupirireni,” akukumbukira mkazi mmodzi yemwe anachotsa mimba pamene anali wa zaka za pakati pa 13 ndi 19, “chimapweteka kudziŵa kuti ndinali wopangitsa wa kupha, kupha kumene nkholeyo sidzadziŵa mmene ndiriri wachisoni.”

Kufunafuna kaamba ka Mayankho

Vuto la mayanjano, maukwati osakhazikika, umphaŵi​—izi ziri zochitika zofala za pambuyo pa mimba ya uchichepere. Chotero, nchosadabwitsa m’pang’ono pomwe, kuti nkhani imeneyi yakhala chonulirapo chodetsa nkhaŵa kwa aphunzitsi, adokotala, andale za dziko, ndi makolo. Ena amaitanira pa maprogramu a maphunziro a kugonana, ngakhale kulamulira kuti mautumiki oletsa kubala ndi kutaya mimba apangidwe kukhala ofikirika mopepuka kwa achichepere.

Mosasamala kanthu za chimenecho, achichepere ena ali ndi zosowa za malingaliro zimene maphunziro a kugonana sangakhutiritse. Atsikana ena, mwachitsanzo, m’chenicheni afuna kukhala ndi pakati! Monga mmene mtsikana mmodzi wachichepere anachiikira icho kuti: “Ndinayesera kulowa mu vuto kupeza chisamaliro cha makolo anga. Ndinalingalira kuti [mwana] ameneyu akakhala chinachake chomwe chikakhala changa​—palibe wina aliyense akamtenga iye ndipo ndikakhala ndi mbali yotsalira ya ine yomwe ikandipatsa ine chifukwa cha kukhalira ndi moyo.”

M’kuwonjezerapo, maprogramu a maphunziro a kugonana samapereka kwa achichepere chitsogozo cha makhalidwe abwino. Maiko onga ngati Sweden ndi Netherlands, kumene maprogramu oterowo ali ofala, angakhale ndi mimba za achichepere zochepa koma mkhalidwe wa chisembwere uli wofala. Kodi chingakhale chakuti, m’kuwonjezera ku mimba, mkhalidwe wa chisembwere umapereka malipiro owopsya amalingaliro, makhalidwe abwino, ndi uzimu? Ngati ndi tero, kodi pali chifukwa chenicheni cha kulimbikitsira, osati kupewa mimba, koma chiyero? M’kuyankha, lolani kuti tiyang’ane pa zimene bukhu lakale kwambiri lomwe liripo​—Baibulo​—limanena pa nkhaniyi.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Atsikana a msinkhu wopita ku sukulu omwe amakhala ndi pakati amabwera kuchokera ku magulu onse amayanjano a zachuma ndiponso kuchokera ponse paŵiri kusukulu za unyinji ndi zapadera. Mafuko onse, zikhulupiriro zonse, ndi mbali zonse zadziko, kumudzi ndi kutauni, onse amaimiridwa.”​—Magazini ya Adolescence.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena