Kodi Nkuphonyeranji Iwo?
Pamene anali pa mzera pa banki ya mu mzinda wa New York chirimwe chapita, mkazi wa zaka za chikatikati anawona kuti mwamuna wina yemwe anali kutsogolo kwake anali kuŵerenga magazini ya Nsanja ya Olonda. Iye anali wofunitsitsa kuŵerenga nkhani mu iyo pa pemphero, chotero anasunga tsiku la kopelo.
Masiku ochepa pambuyo pake, Mboni za Yehova zinaitanira pa khomo lake, ndipo anafunsa: “Kodi muli ndi makope a July a Nsanja ya Olonda?” Pambuyo pa kudziŵa chifukwa chimene iye anali wokondweretsedwa mu magazini yokhayo, imodzi ya Mbonizo inadziŵitsa kuti: “Njira yabwino ya kusaphonyera makope alionse osangalatsa iri kulembetsa.”
“Sindinadziŵe kuti ungatero!” Mkaziyo anafuula tero. Pamene anauzidwa kuti kulembetsa kwa chaka chimodzi kunali K32.00, iye anayankha: “Kodi muli otsimikiza? K32.00 yokha kaamba ka chaka chonse?” Pamene anatsimikiziridwa kuti chinali tero, iye anafuna osati kokha Nsanja ya Olonda komanso magazini inzake Galamukani! “Kodi muli otsimikiza kuti ndingapeze magazini onse aŵiri pa K48.00 yokha?” iye anafunsanso.
Mkaziyo anali wosangalatsidwa kukhala ndi Mboniyo ikulembetsa kaamba ka iye. Nanunso mungamatumiziridwe magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kunyumba kwanu. Tumizani kokha K48.00, ndipo mudzalandira magazini aŵiri amenewa (makope atatu pa mwezi) kaamba ka chaka chimodzi.
Chonde tumizani kulembetsa kwa chaka chimodzi kwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndatsekeramo K48.00 (Zambia). (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)