‘Odzipereka kwa Mulungu Wamkulu Yehova Kosatha’
MU APRIL 1935, mtumiki wodziŵika wa chiAmerica ndi mlankhuli anachezera Hawaii. Ichi chinali chosangalatsa mwapadera kwa Mboni za Yehova, zomwe zinali kokha zokwanira 12 panthaŵiyo, popeza mlendo wolemekezeka ameneyo anali Joseph F. Rutherford, prezidenti wachiŵiri wa Watch Tower Bible and Tract Society. Nkhani yakuti “Ndani Adzalamulira Dziko?” inalongosola ulamuliro womadza wa dziko wa Ufumu wa Mulungu. Iyo inaperekedwa pa bwalo la za maseŵera la pamwamba la kumaloko ndipo inalandira kufalitsidwa kwakukulu.
Dzina la Mulungu ndi Ufumu wake wakhala mutu wa ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova kuyambira kukhazikitsidwa kwawo kwamakono. Chotero chiri chosangalatsa kwa onse omwe amayamikira ndi kugwiritsira ntchito dzina laumwini la Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, kuti kufanana kwa chiHawaii, Iehova, kunagwiritsiridwa ntchito mofala ndi alambiri oyambirira a chiHawaii. Chimodzi cha matchalitchi oyambirira omangidwa ndi atumiki a Chikristu cha Dziko mu Hawaii, tchalitchi cha mwala pa Kawaiahao mu Honolulu, mwala wake wa maziko unakhazikitsidwa mu 1839. Ozokotedwa pa mwala woperekedwa umenewo anali mawu akuti: “Kwa Iehova Mulungu wathu ku nthaŵi zonse.”
Chiyambire 1935, pamene Judge Rutherford anachezera, ntchito ya Mboni za Yehova mu Hawaii yakula kuchokera ku kokha Mboni zokangalika 12 kufika ku zoposa 5,400 lerolino. Iwo mowona ‘adzipereka kwa Mulungu wamkulu Yehova kosatha.’