Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 3/15 tsamba 22-23
  • Kufuula Chowonadi mu Austrian Alps

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufuula Chowonadi mu Austrian Alps
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Kuyambira ku Chiyambi Chaching’ono
  • “Kumanga Beteli Yathu”
  • Okonzekeretsedwa kaamba ka Chiwonjezeko Chowonjezereka
Nsanja ya Olonda—1988
w88 3/15 tsamba 22-23

Kufuula Chowonadi mu Austrian Alps

AUSTRIA ali wotchuka moyenerera kaamba ka udzu wake wa alpine, Vienna Woods, ndi Danube wobiriŵira wokongola. Izi ndi zowonekera zina zodziŵika zimakoka alendo ochokera pa dziko lonse kubwera ku dziko laling’ono limeneli mkati mwa Europe.

Pa kaindeinde pa nyengo ya kuchezera August wapita, gulu limodzi la alendo chifupifupi zana limodzi ochokera ku maiko a kunja 17 linabwera kudzawona chinachake chosiyana kotheratu. Anabwera ku Vienna kudzapezekapo pa kuperekedwa kwa ofesi ya nthambi yatsopano ya Austria ya Watch Tower Society, yomwe imatsogoza ntchito yolalikira Ufumu ya Mboni za Yehova mu Austria.

Kuyambira ku Chiyambi Chaching’ono

Ofesi ya nthambi yoyamba ya Sosaite mu Austria inakhazikitsidwa mu Vienna mu 1923. Zinali zaka zochepera pa khumi pambuyo pa kuchezera koyamba pa olembetsa ku Nsanja ya Olonda anayi mu mzinda umenewo. Panthaŵiyo, chiŵerengero cha olalikira Ufumu chinali chitakula kufika ku zana limodzi. Kenaka inabwera Nkhondo ya Dziko II ndi kutenga malo kwa Nazi, nyengo ya ziyeso zoipitsitsa ndi kuvutika kwa abale okhulupirika. Koma iwo anapirira, ndipo pofika kumapeto kwa nkhondo, mathayo awo anali atakula kufika ku oposa pa 700.

Kuti ayang’anire kufutukuka kwa ntchito, nyumba pa Gallgasse 44 inagulidwa mu 1957. Mkati mwa zaka, kukonzedwa kosiyanasiyana kunapangidwa ku nyumbayo kuti akwaniritse chiwonjezeko chomakula cha ntchito ya Ufumu m’dzikolo. Podzafika 1973 chiŵerengero cha ofalitsa a Ufumu chinapitirira pa chizindikiro cha 10,000. Chotero, kumayambiriro kwa ma-1980, makonzedwe anapangidwa kaamba ka kufutukuka. Zokhumudwitsa za lamulo mwamsanga zinachotsedwa, ndipo malo oyandikana ndi nthambiyo anapezedwa. Mu March 1983 kampani ya kunja inayamba ntchitoyo. Pambuyo pa chimenecho, abalewo anaitenga ntchitoyi ndi kumaliza kumangako.

“Kumanga Beteli Yathu”

Mboni zochokera ku mbali zonse za Austria zinadzipereka mwaufulu kaamba ka ntchitoyo. “Tikumanga Beteli yathu” anali mawu ofala. Iwo anabwera pa magalimoto ndi mabasi, kufika ku 190 pa kothera kwa mlungu kumodzi. Chinayerekezedwa kuti mmodzi mwa ofalitsa asanu ali onse m’dzikolo anali ndi mbali mu ntchitoyo. Ena okhala ndi kuzolowera​—odziŵa zomangamanga, oika mapaipi, ndi zina zotero. Ena anapereka zinthu kapena kupereka kugwiritsira ntchito malo awo antchito. Ena anasiya ngakhale ntchito zawo ndi kubwera kudzagwira ntchito kaamba ka nyengo yonse yomanga.

Mbale mmodzi yemwe anatha mbali ya tchuthi chake pa malo omangawo analemba kuti: “Ndingakonde kukuthokozani kachiŵirinso kaamba ka mlungu wabwino wa tchuthi. Chinali monga kukhala pa chisumbu chabata chozunguliridwa ndi nyanja yaukali ya umunthu. Chinali chozizwitsa kusangalala ndi chitsitsimulo choterocho cha kuthupi ndi chauzimu popanda malipiro.” Ngakhale achichepere anatengako mbali. Wa zaka zakubadwa zisanu ndi zitatu analemba kuti: “Ndamva kuti mukufuna ndalama zomangira Beteli. Ndingakonde kukutumizirani inu zina za ndalama zimene ndinasunga. Ndatsekeramo 200 shillings [chifupifupi K128.00, Zambia] ndi kalatayi.” Ena anaphika mkate kapena kutola zipatso ndi kupanga zakumwa kaamba ka antchito odziperekawo. Ofalitsa m’mipingo 36 mu Vienna anapereka zotsitsimulitsa zokoma pa Loŵeruka lirilonse mkati mwa nyengo yonse yomangayo.

Okonzekeretsedwa kaamba ka Chiwonjezeko Chowonjezereka

Ndi kukonzedwanso kwa nyumba yakaleyo ndi kuwonjezera kwa nyumba zatsopano zozungulirazo, malo a nthambiyo tsopano ali aukulu wa kuŵirikiza nthaŵi zitatu kuposa mmene analiri poyamba, ndi chiwonkhetso cha malo osamangidwapo kanthu okwanira 5,400 sq m. Malowa amaphatikizapo zipinda 38, chipinda chodyera kaamba ka anthu 80, kichini yatsopano, ndi malo ochapiramo. Nyumba ya Ufumu yatsopano iri kumbuyo kwa nyumba yakaleyo. Maofesi oyang’anirako ntchito ndi madipatimenti ena osiyanasiyana amatenga malo otsala a nyumbayo.

August 22, 1987 linali tsiku la kuperekedwa kwa malo a nthambi yatsopanowo. Pakati pa alendo 282 panali chifupifupi alendo zana limodzi ochokera ku nthambi 16 za ku Europe ndi mmodzi wochokera ku Korea. Ndiponso omwe analipo anali chifupifupi zana limodzi la anthu a ku Austria akale omwe anapulumuka ziyeso za Nkhondo ya Dziko II. Wamkulu kwambiri pakati pawo anali Maria Hack wa zaka zakubadwa 102 wochokera ku Graz. Khamu la anthu 6,810 m’malo ena asanu ndi aŵiri linamvanso programu ya kuperekako kupyolera mu kulumikizidwa ndi lamya.

Olankhula enieni a pa programu ya kuperekako anaphatikizapo T. Jaracz ndi M. G. Henschel a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova mu Brooklyn, New York. Akulankhula pa mutu wakuti “Nthambi Zimene Zimabala Zipatso ku Ulemerero wa Yehova,” Mbale Jaracz anagwiritsira ntchito Yohane 15:2, 8 kusonyeza kuti: ‘Nthambi’ zimatumikira ku ulemerero wa Yehova pamene zibala zipatso zochuluka. Malo a nthambi atsopanowo adzathandizira mokulira kulinga ku kutulutsa zipatso ku ulemerero wa Yehova.

M’nkhani ya kupereka, Mbale Henschel anagogomezera kuti Yehova ali Mulungu wa chifuno. Iye sanadziŵikitse kokha chifuno chake pasadakhale komanso wachitira chithunzi kuti iye ali ndi kuthekera kwa kuchita tero. Mosasamala kanthu za chitsutso cha Satana, ife tingakhale ndi chidaliro kuti chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwa.

Pamene programuyo inafika ku mapeto ake, onse opezekapo anadzimva olimbikitsidwa kupitirizabe pa ntchito yolalikira ndi mphamvu yatsopano. Mwachiwonekere, malo atsopano abwinowo adzakonzekeretsa Mboni za ku Austria kufuula mbiri yabwino ya Ufumu ngakhale kumlingo wokulira mu dziko la mapiri limeneli, kuchilemekezo ndi chitamando cha Mlengi wamkulu, Yehova.

[Zithunzi patsamba 23]

Nyumba yatsopano, yowonedwa kuchokera m’munda

Nyumba ya Ufumu

Khomo lalikulu lolowera

Nyumba yatsopano, ndi nyumba yokonzedwanso kulamanja

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena