Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 3/15 tsamba 21
  • Tiyeni, Mboninu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tiyeni, Mboninu!
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Nkosangalatsa Chotani Nanga Kukhala Pagome la Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Yehova Anatipulumutsa ku Ulamuliro Wankhanza
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Nyimbo Zatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Tiimbile Limodzi Nyimbo ya Ufumu
    Imbirani Yehova Mosangalala
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 3/15 tsamba 21

Tiyeni, Mboninu!

“Olimba mu nthaŵi ya mapetoyi,/​Ali atumiki oimira mbiri./​Ngakhale Satana atsutsa,/​Mwa mphamvu ya Mulungu sawopa.”

Iyi iri mizera yotsegulira ya nyimbo nambala 11 mu bukhu la nyimbo la Mboni za Yehova, “Kuyimba ndi Kutsagana ndi Nyimbo za Malimba M’mitima Mwanu.” Kuyamikira kwanu kwa nyimboyi kuyenera kuzama mwa kuphunzira kuti kaimbidweko kanapangidwa mumsasa wa chibalo mu Nazi Germany. Posachedwapa, antchito ena 500 a banja la Beteli la German mu Selters anamvetsera ku kukambitsirana kojambulidwa pa tepi kwa wokonza wa nyimboyi, Erich Frost, yemwe anasimba zotsatirazi:

“‘Tiyeni, Mboninu!’​—chimenecho chinali chikhumbo cha mtima wathu ngakhale panthaŵiyo, ngakhale kuti tinali kugwira ntchito ya kalavulagaga mumsasa wa chibalo. Malingaliro a wokonza nyimboyo nthaŵi zonse amamvekera ndi kaimbidwe kosiyanasiyana, chotero kaimbidwe ka nyimboyo kakhala m’mutu mwanga kwanthaŵi yaitali. Gulu la ntchito limene ndinaliko, lokhala ndi Mboni 40, linali kuyenda kwa theka la ora tsiku lirilonse kupita ku malo opita zinthu zoipa kunja kwa m’msasawo. Pa ulendo m’mawa umodzi, lingaliro linawonekera kwa ine: ‘Tsopano iri nthaŵi ya kuika mawu ena ku nyimboyo, kotero kuti ingaimbidwe,’ ndipo mwamsanga versi loyamba linayamba kupangika m’maganizo mwanga.

“Ntchito yanga inali kuyendetsa dothi pa wheelbarrow kwa utali wa mamita 30. Kulankhula mkati mwa ntchito kunali koletsedwa kotheratu. Komabe, ndikumasankha mphindi yabwino, mwachinsinsi ndinafunsa mbale wogwira ntchito pafupi nane ngati anali ndi chikumbukiro chabwino. Iye ananena kuti inde, chotero ndinamusungitsa iye versi loyamba. Pambuyo pa ora, ndinafunsa mbale wina, kenaka wachitatu, ndipo kenaka wachinayi. Aliyense anafunsidwa kuphunzira versi limodzi pa mtima.

Nditabwerera mumsasa madzulo amenewo, anayiwo anabwereza maversiwo kwa ine, mmodzi pambuyo pa mnzake. Chotero, ndikawonjezera mawu ku manotsi amenewa. A SS sakanapita patali kokha ngati manotsiwo anagwera m’manja awo. Koma tsopano mkhalidwe unafikira pa kuipa kwambiri. Ngati iwo akanandigwira ine ndi mawu a nyimbowo, akanandipachika ine. Kodi ndikanabisa motani nyimboyo?

“Mbale wachikulire anali kusamalira udzu kunja kwa msasa kumene a SS ena anasunga akalulu awo. Mu udzuwo, iye anapeza malo obisa zokometsera zauzimu zenizeni​—makope athunthu a Nsanja ya Olonda ndi limodzi kapena aŵiri a mabukhu a Sosaite. Mbale ameneyu anatenga moyo wake m’manja mwa kuzembetsa zinthu zoterozo kuzilowetsa mumsasawo, chotero kutipatsa ife ndi zinthu zophunzirira. Pano iye anabisa nyimbo yanga. Tsiku limodzi ananena kuti: ‘Erich, nyimbo yako iri pa ulendo wake. Ndinapeza winawake yemwe anaitumiza iyo ku Switzerland.’ Ndinapuma mpweya wa chitsitsimulo.

“Abale a chiSwiss anatumiza iyo ku Brooklyn, kumene inafika m’manja mwa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Mawu anga a nyimbo osawoneka bwino anasinthidwira kukhala maversi atatu ozizwitsa. Ndinasangalala koposa pamene pambuyo pake ndinapeza kuti nyimbo imeneyi iri m’bukhu la nyimbo latsopano la Mboni za Yehova.a Lerolino, monga nyimbo nambala 11, iyo imasonkhezerabe Mboni zonse kuima nji kaamba ka Yehova ndi chowonadi!”

[Mawu a M’munsi]

a Inaimbidwa kwa nthaŵi yoyamba mu United States ndi gulu loimba la ophunzira la kalasi ya 11 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower monga mbali ya programu yawo ya kumaliza maphunziro, pa August 1, 1948.

[Bokosi patsamba 21]

Erich Frost anamaliza ntchito yake ya padziko lapansi pa October 30, 1987, pa msinkhu wa 86. Wobadwa pa December 22, 1900, iye anabatizidwa pa March 4, 1923, ndipo analowa mu utumiki wa nthaŵi zonse mu 1928. Mu 1936 iye anaikidwa woyang’anira wa ntchito ya chibisira ya mboni zozunzidwa mu Germany, kusamalira bwino kaamba ka gawo limenelo kwa miyezi isanu ndi itatu kufikira pamene iye analoŵetsedwa mumsasa wa chibalo. Pambuyo pa nkhondo, kuyambira mu 1945 mpaka 1955, iye anatumikira monga woyang’anira wa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society mu Germany. (Onani Nsanja ya Olonda, April 15, 1961, masamba 244-9, Chingelezi) Pambuyo pa chimenecho, iye anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. Mulungu sadzaiwala ntchito ya Akristu odzozedwa oterowo kapena chikondi chimene amasonyeza ku dzina lake.​—Ahebri 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena