Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 2/15 tsamba 22-23
  • Chisumbu cha Thursday Chimva Mbiri Yabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chisumbu cha Thursday Chimva Mbiri Yabwino
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Mbiri Yabwino Ifika pa Zisumbu Zimenezi
  • Mpingo Upangidwa
  • Kufikira Zisumbu Zina
  • Malo Osonkhanira Abwino
Nsanja ya Olonda—1988
w88 2/15 tsamba 22-23

Chisumbu cha Thursday Chimva Mbiri Yabwino

PAMENE ndege inazungulira, zonse zomwe tinawona zinali unyinji wa zisumbu zamapangidwe ndi ukulu wosiyanasiyana pakati pa nyanja yobiriŵira. Tiri pafupi kutera, tinawona msewu woyenda ndege​—unali waung’ono chotani nanga​—koma ndi mpumulo wotani nanga!

Tinatera pa Chisumbu cha Horn. Pambuyo pa ulendo wa pa basi kupita ku malo amene zombo zimatsitsira katundu, chikwepe chaching’ono chinatitenga ife ku Chisumbu cha Thursday, pakati pa Zisumbu za Torres Strait. Tizisumbu timeneti tiri tofutukuka monga miyala yopondera kuchokera ku nsonga ya kumpoto ya Queensland, Australia, mtunda wonsewo ndi kudutsa Papua New Guinea.

Mkati mwa nyengo yotentha, ya chinyezi (January mpaka May), chirichonse chimakhala chobiriŵira ndipo chokongola. Mphepo ya mkuntho ya chiŵaŵa nthaŵi zina imayambika, kupangitsa njira yodutsira tizisumbuyo kukhala yowopsya. Kaamba ka kulinganizika kwa chaka, kuwuma ndi fumbi ziri zozoloŵereka.

Mbiri Yabwino Ifika pa Zisumbu Zimenezi

Munali mu 1938 pamene Lightbearer ya Watch Tower Society ya 16 m inaima kwakamphindi pa zisumbu zimenezi pamene inali pa ulendo wake wopita ku Dutch East Indies (tsopano Indonesia). Mu bwatomo munali Mboni za Yehova, zisanu ndi ziŵiri zofunitsitsa kugawana uthenga wa chiyembekezo wa Baibulo.

Chosadziŵika kwa abale amenewa, ngakhale kuli tero, mmodzi wa amishonale a Chikristu cha Dziko anali atafika chifupifupi panthaŵi imodzimodziyo. Iye anauza anthu a pa chisumbupo kusamvetsera kwa Mboni za Yehova kapena kulandira lirilonse la mabukhu awo. Koma pamene abalewa anafika panyumba yake ndi kulankhula ndi iye, iye analandira mabukhu anayi. Ena a anthu a pa chisumbuwo anawona ichi, chotero analingalira: ‘Ngati iye angakhale nawo, nchifukwa ninji ife sitingatero?’ Madzulo amenewo, pamene Mboni zina zinali kuwonetsa zithunzithunzi, mmodzi wa abalewo anakhala kunja ndi makatoni a mabukhu. Mobwerezabwereza, mumdima, dzanja lokhala ndi ndalama linawonekere, ndipo liwu linapempha kaamba ka bukhu. Kokha mu ora limodzi, mabukhu 200 anagawiridwa! Pambuyo pake, m’mishonaleyo anayesera mopanda chipambano kugwiritsira ntchito mabukhu amene anawapezawo monga chitsimikiziro chotsutsana ndi Mboni.

Mpingo Upangidwa

Mbewu zoyambirira za chowonadi zimenezo sizinathiriridwe kwa nthaŵi yaitali. Kufikira kumapeto kwa ma-1950 ndi pamene thandizo lowonjezereka linafika mu zisumbu zakutali zimenezi. Ogwira ntchito anthaŵi zonse aŵiri anatumizidwa ndi Watch Tower Society. Iwo anatsatiridwa ndi a Rudds, banja la atatu omwe anabwera kudzatumikira kumene chifuno chinali chokulira. Mwamsanga, mpingo waung’ono unapangidwa pa Chisumbu cha Thursday.

Izi zinali nthaŵi zovuta, akumakhala popanda malo ogona aliwonse ndi chitsutso chokulira kuchokera ku boma ndi zipembedzo zokhazikitsidwa. Poyambirira mpingowu unakumana m’chipinda chaching’ono pamwamba pa mauvuni a wophika mkate wakumaloko. Tangolingalirani mmene kunaliri kotentha m’malo otenthawo!

Zikumazindikira chifuno cha kukhala zamphamvu mwauzimu, Mbonizo zinagamulapo kupezeka pa msonkhano pa gombe la ku Australia, chifupifupi 1,300 km kutali. Alibe ndalama zokwanira za ndege, iwo mwapemphero anafuna njira ina ya kupitira ku msonkhanoko.

Choyamba, abalewo anagula bwato lofufuzira miyala ya mtengo wapatali lakale lomwe linalibe injini, choyendetsera, choyandamitsira, ndi choimikira. Akumafunafuna pakati pa mabwato osiidwa, iwo potsirizira pake anapeza imodzi imene inali ndi injini yaikulu ya diesel ya masilinda asanu ndi gearbox. Akumagula iyi, abalewo anasangalatsidwa kupeza zoyandamitsira, zoimitsira, ndi zitsulo zina zambiri. Komabe, analibe shaft kapena choyendetsera.

Mbale Rudd anafunsa mwini wa mosungira zitsulo ngati akanafunafuna pamalopo. Mwiniwakeyo moseka ananena kuti ngati angapeze shaft pena paliponse pamalopo, Mbonizo zikakhoza kuitenga iyo. Kukudabwitsidwa kwa mwiniyo, shaft inapezedwa. Pamene anali kupita ku nyumba ndi nyumba m’mawa woŵerengeka pambuyo pake, Mbale Rudd anakankha chinachake mu udzu wautali. Chinali choyendetsera chomwe chikayenerana ndi bwato lawo!

Pambuyo pa kukonza bwatolo, mpingo wa anthu 25 unali wokonzekera paulendo wa pamadzi wa masiku asanu ndi aŵiri. Pamene iwo ananyamuka, sing’anga waufiti wa kumaloko anaika “m’tsiriko” pa iwo. Usiku wina bwatolo linatitimira pamalo omwe sanali akuya kwenikweni. Abalewo anagwiritsira ntchito nthaŵiyo mwamwaŵi kugwira nsomba. Pamene funde la m’mawa linabwera, bwatolo linachokapo, ngakhale kuti anayenera kuchotsamo madzi kaamba ka ulendo wonsewo.

Pamene anafika pa Townsville, Australia, mwiniwake wa mosungira zitsulo wolemera anakumana nawo. Mwachiwonekere iye anaŵerenga mu nyuzipepala nkhani yonena za kuyesayesa kwawo kwa kukapezeka pa msonkhano, ndipo anasonkhezeredwa kuwathandiza. Iye analimbikira pa kukonza kuwonongeka kwa bwatolo ngakhale kuti iwo sakanatha kulipira kapena kuthandiza kukonzanso chifukwa anali pa msonkhano. Pambuyo pake, iwo analipiritsidwa kokha 40 pounds (K640.00, Zambia) m’malo mwa 500 pounds (K8,000.00, Zambia) zomwe zinakakhala zoyenerera.

Kufikira Zisumbu Zina

Ndi chitsogozo cha Yehova, uthenga wa Ufumu wafikanso ku zisumbu zina za kunja. Mwachitsanzo, Mbale Rod Anderson ndi Allan Webster, omwe anapita ku Chisumbu cha Thursday zaka zingapo zapita, agwiritsira ntchito bwato lawo m’kuchitira umboni pa zisumbu zina. Kufikira tsopano, kulalikira kwachitidwa pa 12 za zisumbu zokhalidwa 17.

Malo Osonkhanira Abwino

Abalewo kwa nthaŵi yaitali anadabwa, ngakhale kuli tero, ngati iwo adzapeza Nyumba ya Ufumu yawoyawo pa Chisumbu cha Thursday. Kenaka kugwira ntchito kwa mzimu wa Yehova kunawonekera. Mu September 1983, Mbale Graham Keen, womanga waluso, anafika kudzathandiza ndi kumanga nyumbayo. Unyinji wa mipingo ya ku Australia mooloŵa manja inapereka zinthu zofunikira kaamba ka kumangako. Izi zinalongedwa m’zotengera ndi kutumizidwa pamadzi kuchokera ku Cairns, Queensland. Anthu pa chisumbupo anadabwitsidwa kuwona unyinji wa zinthu zomangira pa malo a dziko omwe poyamba anali opanda kanthu. Chinatenga kokha masiku 140 ogwira ntchito kumaliza holoyo, limodzi ndi nyumba kumbuyo kwake. Panali 120 opezekapo mwachimwemwe pa tsiku la kuperekedwa kwa holo yatsopanoyo.

Zinali zachimwemwe chotani nanga Mboni zonse kukhala ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano imeneyi kutumikira monga malo apakati a ntchito ya kubukitsa mbiri yabwino mu Zisumbu za Torres Strait. Ndi thandizo la mzimu wa Yehova, iwo amasangalala kunenera ulemerero wa Yehova Mulungu.​—Yesaya 42:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena