Chidziŵitso pa Nyuzi
“Atate Wathu . . . ”
“Akazi kuzungulira m’dziko akhala akuuza alambiri anzawo kuti sichiwasangalatsa iwo kugwiritsira ntchito kotheratu chinenero cha amuna (‘Atate Wathu wa Kumwamba’) mu mautumiki akulambira,” ikusimba tero Minneapolis Star and Tribune. “Chimawapangitsa iwo kudzimva monga nzika zachiŵiri, akutero akazi, ndipo iwo sangalankhule kwa mulungu wamwamuna.” Kuchirikiza nkhaniyi, bungwe lolamulira la Tchalitchi cha United Methodist mu Minneapolis, Minnesota, U.S.A., linavomereza mwachiyanjo cha ndandanda yatsopano ya mawu ogwiritsidwa ntchito ndi ansembe pamene akulozera kwa Mulungu mkati mwa pemphero, mautumiki a kulambira, ndi machitachita ena a tchalitchi.
Mawu ena osakambitsiridwapo okonzekeretsedwa ndi bungwe la tchalitchilo ali akuti “magwero a mtendere, magwero a chifundo, wosasunthika ndi wachikondi, mphamvu ya moyo wathu, . . . malingaliro a chilengedwe, . . . wapamwamba ndi woyera.” Kugwiritsira ntchito kwa mawu amenewo kudzalimbikitsidwa monga olowa m’malo ku alowa m’malo a mawu a amuna limodzinso ndi mawu akuti Ambuye, Mfumu, ndi Atate, amene amasonyeza Mulungu kukhala wamwamuna.
Komabe, kukana kugwiritsira ntchito kwa Baibulo kwa chilozero cha mwamuna kwa Mulungu kuli kopanda chiyambi. Mwamsanga isanafike imfa yake, Yesu, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, mwachindunji anagwiritsira ntchito liwu la Aramaic Abba, kutanthauza “Atate,” pamene anapemphera kwa Yehova Mulungu. (Marko 14:36) Mofananamo, mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito liwu limeneli kusonyeza unansi wathithithi pakati pa Akristu odzozedwa ndi mzimu ndi Atate wawo wa kumwamba, Yehova. (Aroma 8:15; Agalatiya 4:6) Chotero, ngati, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti, “Atate wathu wa kumwamba,” kodi Akristu onse lerolino safunikira kuchita chofananacho?—Mateyu 6:9.
Matchalitchi M’ngongole
Pambuyo pa msonkhano wa tchalitchi wa Tchalitchi cha Dutch Reformed kumpoto kwa Transvaal, South Africa, chinasimbidwa kuti mipingo 134 ya tchalitchiyo inali m’ngongole ku ndalama zokwanira R13,890,000 (K53,336,000, Zambia). Kuchitira ndemanga pa vutolo, mkonzi mu nyuzipepala ya chiAfrikaans Beeld anafunsa kuti: “Kodi cholakwacho, ngakhale kuli tero, nthaŵi zina sichikhala ndi atumiki ndi bungwe la tchalitchi?” Nyuzipepalayo ikulongosola kuti: “Chimachitika kaŵirikaŵiri kuti dikoni mokhazikika amabwera pa maulendo a kunyumba a pa mwezi ndi mwezi kudzasonkhetsa ndalama, pamene mtumikiyo samawonekera mwa kusakhalapo kwake ndipo mkuluyo amakhala mlendo m’dera lake. Kodi ziwalo za tchalitchi, mu zochitika zoterozo, ziyenera kupatsidwa thayo kaamba ka kupeza chitsimikiziro chakuti tchalitchi chiri chokondweretsedwa kokha mu ndalama zawo, osati mu ubwino wawo wauzimu?”
Mosiyanako, utumiki wa Yesu ndi ophunzira ake unaika chigogomezero pa kupatsa kwauzimu. (Mateyu 10:8) Pamene kuli kwakuti amvetseri oyamikira kaŵirikaŵiri amabwera ku chithandizo chawo mwakupereka kwaufulu zosowa zawo zofunikira monga ngati zakudya ndi malo ogona, Yesu osati ngakhalenso ophunzira ake sanafune mapindu akuthupi. (Luka 10:5-9) Monga mmene mtumwi Paulo ananenera: “Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.” M’malo mwake, iye anachenjeza atumiki owona a Mulungu kuti: “Alole njira [yawo] ya moyo kukhala yomasuka ku chikondi cha ndalama.” Maulendo ake a kunyumba ndi nyumba anapangidwa kotero kuti iye ‘angachitire umboni ku kulapa kulinga kwa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu.’ (Machitidwe 20:20, 21, 33; Ahebri 13:5, NW) Anali atsogoleri achipembedzo a tsikulo amene analongosoledwa ndi mlembi wa Baibulo Luka kukhala “okonda ndalama.”—Luka 16:9-15.
Zosangulutsa Zoipa
Kokha kaamba ka zoseketsa, ophunzira a chiGerman mu Lahnstein anayamba kusonkhezera mizimu ya matsenga kulankhula kupyolera mu chikho chomwera madzi kumasintha kuchokera ku lemba limodzi kupita ku linzake, “kumalemba” uthenga. Nchiyani chimene chinali chotulukapo chake?
“A zaka zakubadwa khumi ndi zisanu, amachita mantha kupita okha ku chipinda chosambiramo, amalankhula mosokonezeka ponena za ziwanda. Usiku, achichepere amafuna kugona ndi makolo awo,” ikusimba tero nyuzipepala ya chiGerman Rhein-Zeitung. Kusakhazikika kumabuka pakati pa ambiri a awo amene “m’misonkhano ya chinsinsi anaitana pa mizimu ndipo pomalizira pake pa ‘Lusifa.’” Kuchitira ndemanga pa chivomerezo cha anacho “pamene ‘Lusifa’ moyerekezera analankhulana ndi iwo,’ mphunzitsi mmodzi anawona kuti: “Ngakhale ana ochenjera kwambiri mwadzidzidzi anakhala ogonjetsedwa kotheratu. Iwo anakanthidwa ndi mantha.” Kutsatira chokumana nachocho, malo apakati a achichepere a mumzindawo analetsa “maseŵera” oterowo, ndipo makolo anapemphedwa kusasiya ana awo ochititsidwa mantha okha.
Mogwirizana ndi pepalalo, “funde la matsenga likusefukira pa makanema, TV ndi marekordi.” Komabe, kuseŵera ndi matsenga kaamba ka zosangulutsa sikunapereke pa ana a chiGerman a ku Lahnstein ndi zoseketsa zoyembekezeredwa. Nchifukwa ninji ayi? Chifukwa Baibulo limatidziŵitsa ife kuti Mdyerekezi ali wochenjera ndipo “akusokeretsa dziko lonse lokhalidwa ndi anthu.” Limagwirizanitsa chisonkhezero cha Mdyerekezi padziko lapansi ndi “tsoka.” Satana ndi “mphamvu za mizimu yoipa” (ziwanda) ziyenera kulingaliridwa mosamalitsa monga ngozi yeniyeni yauzimu, ndipo ayenera kupewedwa.—Chivumbulutso 12:9, 12; Aefeso 6:11, 12; yerekezani ndi Machitidwe 19:19.