Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/15 tsamba 4-6
  • Utumiki wa Mayanjano—Mmene Umayambukirira Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Utumiki wa Mayanjano—Mmene Umayambukirira Anthu
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifunsiro Champhamvu cha Utumiki wa Mayanjano
  • Kodi Chipatso Chake Nchiyani?.
  • ‘Kulalikira Uthenga Wabwino’ Kudzera mu Ntchito ya Mayanjano
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Ziyembekezo za Mtsogolo Kaamba ka chiProtestanti—Ndi Inu!
    Galamukani!—1988
  • Carici Coona ndi Maziko Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/15 tsamba 4-6

Utumiki wa Mayanjano​—Mmene Umayambukirira Anthu

KUYAMBA ndi mitanda isanu ya tirigu ndi tinsomba tiwiri, Yesu Kristu mozizwitsa anadyetsa amuna oposa 5, 000, akazi, ndi ana chifupifupi nthawi ya Paskha (March-April) mu 32 C.E. (Mateyu 14:14-21; Yohane 6:1-13) Kuzindikira kuthekera kochititsa chidwi komwe Yesu anachita, anthu anafuna kumupanga iye kukhala mfumu yawo. Mwachidziwikire iwo anadzimva kuti iye akawapulumutsa iwo ku goli la Aroma ndi kuongolera zosowa zawo mu moyo. Kodi nchiyani chomwe chinali yankho la Yesu?

Mmalo mwa kugonjera ku chifunsiro chotchuka, Yesu “anachokanso kunka kuphiri pa yekha.” (Yohane 6:15) Koma khamu silinagonjere mokhweka chotero. Iwo anabweranso kwa iye tsiku lotsatira. Kuzindikira cholinga chawo chenicheni, Yesu anati kwa iwo: “Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimukhuta.” Iye kenaka anaonjezera: “Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha.”​—Yohane 6:25-27.

Kodi nchiyani chomwe tingaphunzire kuchokera ku nkhaniyi? Pakati pa zinthu zina, iyo mwachionekera ikusonyeza kuti ndi mapindu akuthupi chiri moonekera chapafupi kukopa anthu. Komabe, kumanga chiyamikiro chenicheni kaambaka zinthu zauzimu​—zinthu za mtengo wosatha—​chiri kwenikweni chinthu chosiyanako. Lerolino, chikhoterero cha kuyang’ana zinthu kwenikweni mukaonedwe kazinthu zakuthupi chiri chokulira.

Chifunsiro Champhamvu cha Utumiki wa Mayanjano

Mmaso mwa anthu a mu maiko otukuka kumene, mitundu yopita patsogolo ya Kumadzulo imaimira mwawi wonse ndi mapindu akuthupi omwe wina angafune​—mwawi womwe supezeka m’dziko lawo. Kupita patsogolo kumakhumbiridwa, ndipo njira ya kakhalidwe kamoyo imatsanziridwa. Mwawi kaamba ka maphunziro apamwamba umakhala patsogolo makamaka kwa wophunzira aliyense monga pasipoti yakupita patsogolo ndi chipambano. Motsutsana ndi chiyambi chimenecho sichiri chovuta kumvetsetsa nchifukwa ninji mapro gramu amayanjano a matchalitchi akunja akhala ndi chifunsiro champhamvu m’maiko amenewa. Koma kodi zoturukapo zake nchiyani?

Kum’mawa, mwachitsanzo, kufunitsitsa kwa anthu kuchita kokha chifupifupi chiri chonse chimene matchalitchi amafuna ndi cholinga chofuna kuyeneretsedwa kaamba ka mphatso kapena zoperekedwa kwatsogolera ku kuonjezeka kwa “Akristu onyenga adyera.” Mbali yomvetsa chisoni kwambiri, komabe, iri yakuti pamene thandizo limenelo kapena chirikizo litalekedwa, chomwechonso chikondwerero cha anthu chimaleka. Ambiri a Akristu adyera amaziririka pa chionetsero. Mwakutero, pakati pa anthu a ku Cantoni, pali mawu ofala omwe amatembenuzidwa mu china chake chonga ngati ichi: “Mulungu amalikonda dziko, koma dziko limakonda mkaka waufa.”

Ngakhale kuti magulu ambiri a matchalitchi lerolino satsogoza maprogramu achithandizo, kupatulako kokha mkati mwa tsoka, zomwe zinachitika pa nthawi yapita zinasiya chizindikiro chake. Kwa anthu ambiri a Kum’mawa, matchalitchi ali ofanana ndi magulu achithandizo, ndipo chifukwa Chokha chopitira ku tchalitchi chiri kukapeza osati kupereka. Iwo samaona kufunika kwa kupanga kudzipereka kwa umwini kuli konse kaamba ka tchalitchi. Mkhalidwewu ukusonyezedwa, mwachitsanzo, mu kuzengeleza kwawo kwa kupereka chopereka kaamba ka mabukhu a Baibulo chifukwa, m’malingaliro awo, china chake choturutsidwa ndi tchalitchi chiyenera kukhala chaulere.

Kugwiritsira nchito tchalitchi monga njira yakufikira ku mapeto kumaonekera kwambiri mu za maphunziro. Mu maiko ambiri otukuka kumene, kupeza maphunziro a Kumadzulo kumaonedwa kukhala njira imodzi yokhazikika ya kukhala wotchuka ndi wopambana. Malinga ndi gwero limodzi, pa nthawi imene India ina landira ufulu kuchokera ku Britain, 85 peresenti ya mamembala a nyumba ya malamulo a mtundu umenewo anali atapezeka ku “sukulu za Chikristu.” Ndipo, malinga ndi malingaliro a chiConfucian, ku Far East, kukhala wophu nzira bwino chiri chonulirapo chapamwamba kwambiri mu moyo. Mwachibadwa, ambiri amayang’ana ku masukulu a tchalitchi, omwe mwachisawawa amagwiritsira ntchito njira ndi mikhalidwe ya Kumadzulo, monga njira kaamba ka kupita patsogolo kwa umwini. Ndipo, ndi chiyembekezo chofuna kuika ana awo mu imodzi ya masukulu otsogozedwa ndi tcha litchi ndipo mwina mwake kupita ku maiko akunja mtsogolo, makolo ambiri a Kum’mawa omwe mwachibadwa amatsatira miyambo ya chipembedzo mwachimwemwe amapita ku tchalitchi iwo eni ndi kufulumiza ana awo kuchita chimodzimodzi.

Kodi Chipatso Chake Nchiyani?.

Kuyerekezedwa ndi matchalitchi kale kwambiri kumayambiriro, ku matchalitchi a mamishoni kawirikawiri kumapezekako anthu ochuluka. Anthu ambiri mwakutero amayambitsidwa ku ziphuhzitso za tchalitchi ndipo kwa ena lingaliro la Chikristu. Koma kodi kusonyezedwa poyera kumeneku kwawathandiza iwo kumvetsetsa Baibulo ndi uthenga wake? Kodi iwo kwenikweni wapangitsa iwo kukhala Akristu, kunena kuti, otsatira a Yesu Kristu?

Tengani, mwachitsanzo, Kuo Tung, mwamuna wachichepere yemwe anatchulidwa poyambirira. Pamene anafunsidwa kuti kaya iye tsopano amakhulupirira mwa Mulungu pambuyo pa kupezeka ku tchalitchi kwa nthawi yakuti yakuti, iye anayankha kuti: “Ayi. Chitsimikiziro chakuti Mulungu aliko sichinakambitsiridwe ndi komwe.” Mu chenicheni, iye anavomereza kuti sanali wotsimikizira ngati ena a mabwenzi ake amakhulupirira mwa Mulungu wa umunthu, angakhale kuti iwo anapezeka ku tchalitchi ndi iye. Iwo anapita limodzi kokha chifukwa cha mwawi wakuphunzira Chingelezi, iye anatero.

Mwamuna wina wachichepere anafika ku mudzi kaamba ka tchuthi kuchokera ku koleji mu United States. Pamene m’modzi wa Mboni za Yehova anaitana pa iye, iye anafunsa ngati Mboni zimakhala ndi misonkhano yawo mu Chingelezi. Chifukwa ninji? “Kotero kuti ndi pitirizebe kusunga Chingelezi changa,” iye anatero. Pamene iye anauzidwa kuti misonkhano imachitidwa mu zinenero za kumaloko kotero kuti onse apindulemo mwa uzimu, mwamuna wachichepereyo ananena kuti iye adzapita kumene misonkhano imachitidwa mu Chingelezi kawiri pa mlungu.

Angakhale awo omwe anakhala mamembala a tchalitchi ndipo anabatizidwa anasonyeza kusintha kochepera mu kayang’anidwe kawo. Ambiri a iwo amamamatirabe ku zikhulupiriro zawo ndi zizolowezi zawo zapoyamba, kawirikawiri zokhala ndi chivomerezo, ndipo ngati osatinso dalitso, la tchalitchi chawo. Mu China, mwachitsanzo, Akatolika amaloledwa kupitiriza kulambira kwawo kwa makolo, ngakhale kuti ichi chiri choletsedwa kwina kuli konse. Zithunzithunzi zopempha modera nkhawa dalitso la mulungu wapakhomo zimaonedwa kawirikawiri kuzungulira m’makomo anyumba za “Akristu”. Ndipo mu Okinawa, zithunzithunzi za nyama za milungu yamdzikolo zimaikidwa padenga m’ngodya kuchinjiri zabanja.

Bwanji ponena za awo omwe anapindula kuchokera ku maprogramu atchalitchi? Mu chisungiko chawo chopezeka chaposachedwa cha ndalama ndi zinthu zakuthupi, sichiri chachilendo kuwamva iwo akunena kuti yankho ku mavuto a lerolino liri kudzidalira iwe mwini. Choturukapo chiri chakuti ambiri a iwo adzipatula iwo eni kotheratu kuchokera ku kudzilowetsa mu zochitika za tchalitchi ziri zonse kapena, kukuthekera kwabwino koposa, adziika iwo eni pautali wolemekezeka.

Amishonale amatchalitchi anakhala ndi mwawi wabwino kwambiri wa kulangiza anthu ponena za zimene Baibulo limaphunzitsa. Koma m’malo mwa kuwaphunzitsa iwo kutsatira chenjezo la Yesu la “muthange mwafuna Ufumu wache ndi chilungamo chache, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu,” iwo aika chigogomezero pa “zinthu zina.” (Mateyu 6:33) Kudzera m’maprogramu awo amayanjano, iwo achita zambiri kuthandiza anthu mwa kuthupi, mwa mankhwala, ndi m’maphunziro. Koma mapindu amenewa ali kwenikweni akanthawi. Popanda kupereka kaonedwe kauzimu, kawirikawiri maprogramu oterowo anakhala chifukwa cha kuchirimikira kaamba ka zinthu za kanthawi, kapena zikondwerero za dziko.

Matchalitchi anakonzekera kukalalikira uthenga wabwino, koma zomwe zinaturukapo, mu zitsanzo zambiri, kuli kupititsa patsogolo kwa moyo wokonda zinthu za kuthupi, wa kumaiko a Kumadzulo. Inde, iwo anapeza akhulupiriri ambiri. Koma monga taonela, ambiri a amenewa akhala oyedzamira kwambiri pa zinthu za dziko ndi zinthu za kuthupi kuposa ndi kale lonse. Mtsiku la Yesu, iye ananena ponena za atsogoleri achipembedzo:“Mupitapita ku nyanja ndi kumtunda kuyesamunthu mmodzi mtembenuki; ndipo m’mene akhala wotere, mumsandutsa mwanawa gehena woposa inu kawiri.” (Mateyu 23:15) Mulingaliro limeneli, zoyesayesa za Chipembedzo cha Dziko m’kulalikira uthenga wabwino kudzera mu mayanjano kwabwerera m’mbuyo. Iko kwagwa m’mbuyo kopambana kuposa ntchito yokulira yopatsidwa ndi Yesu Kristu: “Chifukwa chake mukani phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”​—Mateyu 28:19, 20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena