Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2026)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
Chilengezo
Zinenero zatsopano zomwe zilipo: Shilluk, Tsimihety
  • Lero

Lamlungu, April 26

Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.—Akol. 3:13.

Yehova amafuna kuti tizikhululukira anthu amene atilakwira. (Sal. 86:5; Luka 17:4; Aef. 4:32) Tingakhumudwe kwambiri chifukwa cha zimene wina walankhula kapena kuchita makamaka ngati munthuyo ndi mnzathu wapamtima kapena wachibale wathu. (Sal. 55:​12-14) Nthawi zina ululu umene timamva umayerekezeredwa ndi kubayidwa ndi mpeni. (Miy. 12:18) Tingayesetse kunyalanyaza mmene tikumvera koma kuchita zimenezi kungafanane ndi kusiya mpeni pabala pomwepo. Mofanana ndi zimenezi, sitingayembekezere kuti tiyamba kumva bwino pongonyalanyaza mmene tikumvera. Chinthu choyamba chimene nthawi zambiri timachita munthu akatikhumudwitsa ndi kukwiya. Baibulo limavomereza kuti tingathe kukwiya. Koma limatichenjeza kuti tisamalole kuti mkwiyo uzitilamulira. (Sal. 4:4; Aef. 4:26) Chifukwa chiyani? Chifukwa kukwiya sikukhala ndi zotsatirapo zabwino. (Yak. 1:20) Kumbukirani kuti kukwiya kumangochitika kokha, koma timachita kusankha kuti tikhalebe okwiya. w25.02 15 ¶4-6

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026

Lolemba, April 27

Nzeru zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeruzo.—Mlal. 7:12.

Yesu anasonyeza kuti si nzeru kukhala ndi ndalama popanda kukhala “wolemera kwa Mulungu.” (Luka 12:​16-21) Pajatu amati zamawa sizidziwika. (Miy. 23:​4, 5; Yak. 4:​13-15) Akhristufe timakumananso ndi vuto lina. Yesu ananena kuti tiyenera kukhala okonzeka kusiya chuma chathu kuti tikhale ophunzira ake. (Luka 14:33) Akhristu a ku Yudeya analolera kusiya zinthu zawo ndipo sankadandaula. (Aheb. 10:34) Masiku anonso abale ndi alongo ambiri alolera kusiya zinthu zawo kapena ntchito n’cholinga choti asalowerere ndale. (Chiv. 13:​16, 17) Kodi n’chiyani chinawathandiza kuchita zimenezo? Iwo amakhulupirira kwambiri lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Timayesetsa kukonzekera zam’tsogolo, koma tikakumana ndi mavuto amwadzidzidzi timakhulupirira kuti Yehova adzatithandiza. w25.03 29 ¶13-14

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026

Lachiwiri, April 28

Popeza tamaliza kuphunzira mfundo zoyambirira zokhudza Khristu, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale aakulu mwauzimu. Tisayambe kuyalanso maziko.—Aheb. 6:1.

Yehova sayembekezera kuti tizikula tokha mwauzimu. Choncho watipatsa abusa ndi aphunzitsi mumpingo, omwe anaphunzitsidwa bwino kuti azithandiza munthu aliyense n’cholinga choti akhale ‘wachikulire’ mwauzimu n’kufika “pa msinkhu wa munthu wamkulu ngati mmene Khristu analili.” (Aef. 4:​11-13) Yehova amatipatsanso mzimu woyera kuti uzitithandiza kukhala ndi “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:​14-16) Komanso Mulungu anauzira anthu kuti alembe mabuku 4 a Uthenga Wabwino kuti atisonyeze mmene Yesu ankachitira zinthu ali padziko lapansi, mmene ankaganizira komanso mmene ankalankhulira. Tikamatsanzira kaganizidwe ka Yesu komanso mmene ankachitira zinthu, tingakhale Akhristu olimba mwauzimu. Koma kuti tikule mwauzimu tiyenera kuphunzira zambiri osati chabe “mfundo zoyambirira zokhudza Khristu.” Zimenezi ndi zina mwa mfundo zoyambirira zimene Akhristu amazikhulupirira. w24.04 4-5 ¶11-12

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena