Citatu, April 15
Muzikondana.—Yoh. 15:12.
Anthu a Mulungu amakonda kuthandizana. (2 Akor. 8:4) Komabe nthawi zina zimafunikila kulimba mtima kuti ticite zimenezi. Mwa citsanzo, nkhondo ikabuka, akulu amazindikila kuti abale na alongo awo amafunikila cilimbikitso, thandizo la kuthupi komanso lauzimu. Cifukwa ca cikondi cawo pa nkhosa, akulu amaika miyoyo yawo pa ciopsezo kuti apeleke zofunikila kwa nkhosazo. Pa nthawi zovuta ngati zimenezo, tifunikila tizikhalabe ogwilizana. Tsatilani malangizo ocokela ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Akulu nthawi zonse ayenela kumabwelelamo m’malangizo kuti azikhala okonzeka komanso odziŵa mocitila tsoka likagwa. (1 Akor. 14:33, 40) Khalani olimba mtima komabe osamala. (Miy. 22:3) Ganizilani mofatsa musanacitepo kanthu. Musaike moyo wanu pa ciopsezo mwadala. Dalilani Yehova. Iye angakuthandizeni kuti mupeleke thandizo kwa abale anu muli otetezeka. w24.07 4 ¶8; 5 ¶11
Cinai, April 16
Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova, . . . ndipo makutu ake anamva kulila kwanga kopempha thandizo.—Sal. 18:6
Davide anali kum’dziŵa bwino Yehova, ndipo anali kum’dalila. Pomwe Mfumu Sauli na anthu ena anali kufuna kupha Davide, iye anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize. Mulungu atayankha pemphelo lake na kumupulumutsa, iye ananena kuti: “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Ponena mawu amenewa, Davide sanali kungovomeleza kuti Mulungu aliko ayi. Pothilila ndemanga pa mawu amenewa, buku lina linanena kuti Davide anali kuonetsa cidalilo cake mwa Yehova “monga Mulungu wamoyo amene nthawi zonse amathandiza anthu ake.” Inde, Davide anadzionela yekha pa zocitika za pa umoyo wake kuti Mulungu wake ni wamoyo, ndipo zimenezi zinam’sonkhezela kupitiliza kum’tumikila na kum’tamanda. (Sal. 18:28, 29, 49) Kukhala otsimikiza kuti Yehova ni Mulungu wamoyo kumatithandiza kumutumikila na mtima wonse. Kumatithandizanso kupilila mavuto amene tingakumane nawo na kupitiliza kugwila nchito molimbika pom’tumikila. Cina, kumatithandiza kukhalabe naye pa ubwenzi. w24.06 20-21 ¶3-4
Cisanu, April 17
Musalole kuti aliyense akusoceletseni mwa njila iliyonse.—2 Ates. 2:3.
Tiphunzilapo ciyani pa mawu amene mtumwi Paulo analembela Atesalonika? Tikamva nkhani inayake imene sigwilizana na zimene tinaphunzila m’Baibo, kapena tikamva nkhani inayake yocititsa cidwi koma yodabwitsa, tiyenela kukhala osamala. Mu ulamulilo wakale wa Soviet Union, adani athu anapatsa abale kalata yooneka ngati yacokela ku likulu lathu. Kalata imeneyo inalimbikitsa abale na alongo kuti adzipatule ku gulu la Yehova na kupanga gulu lawo lodziimila palokha. Kalata imeneyo inali kuoneka ngati yacokeladi kulikulu lathu. Koma abale na alongo okhulupilika sanapusitsidwe. Iwo anazindikila kuti zimene kalatayo inakamba zinali zosiyana na zimene anaphunzila. Masiku anonso, adani a coonadi amaseŵenzetsa njila zamakono na colinga cakuti atisokoneze na kubweletsa magaŵano pakati pathu. M’malo molola “kuti wina aliyense asinthe maganizo” athu mosavuta, tiyeni tidziteteze mwa kuganizilapo mozama ngati zimene tamva kapena kuŵelengazo zigwilizana na coonadi cimene tinaphunzila kale.—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:1. w24.07 12 ¶14-15