Kwa Filimoni
1 Ndine Paulo, mkaidi cifukwa ca Khristu Yesu, ndipo ndili ndi Timoteyo m’bale wathu. Ndikulembela iwe Filimoni wanchito mnzathu wokondedwa, 2 mlongo wathu Apiya, msilikali mnzathu Arikipo, ndi mpingo umene umasonkhana m’nyumba mwako.
3 Cisomo ndi mtendele zocokela kwa Mulungu Atate wathu komanso kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale ndi inu nonse.
4 Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikamakuchula m’mapemphelo anga, 5 pakuti ndimamva za cikhulupililo cako ndi cikondi cimene uli naco pa Ambuye Yesu komanso pa oyela onse. 6 Ndimapemphela kuti cikhulupililo cimene iwe ndi anthu ena muli naco, cikuthandize kuzindikila cinthu ciliconse cabwino cimene tili naco kudzela mwa Khristu. 7 Nditamva za cikondi cako m’bale, ndinasangalala kwambili ndipo zinandilimbikitsa cifukwa unatsitsimula mitima ya oyela.
8 Pa cifukwa cimeneci, ngakhale kuti ndili ndi ufulu waukulu wa kulankhula, moti ndingathe kukulamula mwa Khristu kuti ucite zofunikila, 9 ndikuona kuti ndi bwino ndicite kukupempha mwacikondi. Ine Paulo, munthu wacikulile komanso mkaidi cifukwa ca Khristu Yesu, 10 ndikukupempha za mwana wanga Onesimo, amene ndakhala tate wake kuno kundende. 11 Kale anali wosathandiza kwa iwe, koma tsopano ndi wothandiza kwa iwe ndi ine. 12 Conco, ndikumubweza kwa iwe. Iye ndi wapamtima panga.
13 Ndikanakonda kukhalabe naye kuno kuti apitilize kunditumikila m’malo mwa iwe pamene ndili kuno kundende cifukwa ca uthenga wabwino. 14 Koma sindikufuna kucita ciliconse popanda cilolezo cako, kuti zilizonse zabwino zimene ungafune kucita, uzicite mwa kufuna kwako osati mokakamizika. 15 Mwina n’cifukwa cake anacoka kumeneko kwa nthawi yocepa,* kuti udzakhalenso naye mpaka kale-kale. 16 Sukhala nayenso ngati kapolo, koma ngati m’bale wokondedwa amene ine ndimamukonda kwambili. Ndipo iwe uyenela kumukonda kwambili kuposa pamenepo, cifukwa ndi kapolo wako komanso m’bale wako mwa Ambuye. 17 Conco ngati umandionadi kuti ndine mnzako, umulandile ndi manja awili ngati mmene ungalandilile ine. 18 Komanso ngati anakulakwila ciliconse kapena ali nawe nkhongole, nkhongoleyo ikhale pa ine. 19 Ine Paulo, ndikulemba izi ndi dzanja langa: Ndidzabweza nkhongoleyo. Ndipo sindifunika kucita kukuuza zimenezi, pakuti iwenso uli ndi nkhongole kwa ine ya moyo wako. 20 Inde m’bale, ndikupempha kuti undithandizeko mwa Ambuye. Utsitsimule mtima wanga mwa Khristu.
21 Ndili ndi cidalilo cakuti ucita zimene ndapempha m’kalatayi. Ndipo ndikudziwa kuti udzacita zoposa pamenepa. 22 Cinanso, ndikupempha kuti ukonzeletu cipinda cimene ndidzafikilamo. Ndikukhulupilila kuti cifukwa ca mapemphelo anu, adzandimasula kuti ndidzakutumikileni.
23 Epafura, mkaidi mnzanga mwa Khristu Yesu, akupeleka moni. 24 Maliko, Arisitako, Dema, ndi Luka, omwe ndi anchito anzanga, naonso akuti moni.
25 Cisomo ca Ambuye Yesu Khristu cikhale nanu cifukwa ca mzimu umene mumaonetsa.