LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • 1 Timoteyo 3
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

Za m’Buku la 1 Timoteyo

      • Ziyenelezo kuti munthu akhale woyang’anila (1-7)

      • Ziyenelezo za atumiki othandiza (8-13)

      • Cinsinsi copatulika ca kudzipeleka kwa Mulungu (14-16)

1 Timoteyo 3:1

Mawu amunsi

  • *

    Kucokela ku Cigiriki, “akunyanyamphila.”

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!, phunzilo 55

    Gulu, masa. 32-33, 40

    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila),

    8/2016, tsa. 21

    Nsanja ya Mlonda,

    9/15/2014, masa. 3-4

1 Timoteyo 3:2

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!, phunzilo 42

    Gulu, masa. 32, 34-37

    Nsanja ya Mlonda,

    11/1/2013, tsa. 30

1 Timoteyo 3:3

Mawu amunsi

  • *

    Kapena kuti, “wandewu; waciwawa.”

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Gulu, masa. 32, 35-36

1 Timoteyo 3:4

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Gulu, masa. 32, 34, 133-134

1 Timoteyo 3:5

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Gulu, masa. 32, 34

1 Timoteyo 3:6

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Gulu, masa. 32, 33-34

1 Timoteyo 3:7

Mawu amunsi

  • *

    Kapena kuti, “Akhalenso woti anthu akunja amamucitila umboni wabwino.”

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Gulu, masa. 32, 34-35

1 Timoteyo 3:8

Mawu amunsi

  • *

    Kapena kuti, “osalankhula mwacinyengo; kambelembele.”

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!, phunzilo 55

1 Timoteyo 3:10

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Gulu, masa. 54-55

1 Timoteyo 3:12

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Gulu, masa. 133-134

1 Timoteyo 3:13

Amlongoza a Zofalitsa

  • Buku Lofufuzila Nkhani

    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!, phunzilo 55

  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
1 Timoteyo 3:1-16

Kalata Yoyamba kwa Timoteyo

3 Mau awa ndi odalilika: Ngati munthu akuyesetsa* kuti akhale woyang’anila, akufuna nchito yabwino. 2 Conco woyang’anila ayenela kukhala wopanda cifukwa comuneneza naco, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodziletsa pa zocita zake, woganiza bwino, wadongosolo, woceleza alendo, ndiponso wodziwa kuphunzitsa. 3 Asakhale munthu womwa mowa mwaucidakwa, kapena wankhanza,* koma wololela. Asakhalenso wokonda mikangano kapena wokonda ndalama. 4 Akhale mwamuna woyang’anila bwino banja lake, ndiponso woti ana ake amamumvela ndi mtima wonse. 5 (Ngati munthu alephela kuyang’anila apakhomo pake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalile bwanji?) 6 Asakhale woti wangotembenuka kumene, kuopela kuti angayambe kudzitukumula cifukwa ca kunyada n’kulandila ciweluzo monga cimene Mdyelekezi analandila. 7 Akhalenso ndi mbili yabwino kwa anthu akunja* kuti asanyozedwe ndi anthu komanso kugwidwa mumsampha wa Mdyelekezi.

8 Naonso atumiki othandiza akhale opanda cibwana, osanena pawili,* osamwa vinyo wambili, ndiponso osakonda kupeza phindu mwacinyengo. 9 Akhale ogwila cinsinsi copatulika ca cikhulupililo, ali ndi cikumbumtima coyela.

10 Ndiponso amenewa ayesedwe coyamba ngati ali oyenelela, ndipo ngati alibe cifukwa cowanenezela angakhale atumiki.

11 Naonso akazi akhale opanda cibwana, asakhale amisece, akhale odziletsa pa zocita zao, komanso okhulupilika pa zinthu zonse.

12 Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi, oyang’anila bwino ana ao ndi onse apakhomo pao. 13 Pakuti amuna amene amatumikila bwino, amakhala ndi mbili yabwino ndi ufulu waukulu wolankhula za cikhulupililo cao mwa Khristu Yesu.

14 Pamene ndikukulembela izi, ndikuyembekezela kuti ndibwela kumeneko posacedwa. 15 Koma zina zikandicedwetsa, zimene ndalembazi zidzakuthandiza kudziwa zoyenela kucita m’nyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo. Mpingowo ndi mzati umene umacilikiza coonadi. 16 Kunena zoona, cinsinsi copatulika ca kudzipeleka kwa Mulungu kumeneku n’cacikulu: ‘Iye anaonekela m’thupi, anaonedwa kukhala wolungama mu mzimu, anaonekela kwa angelo, analalikidwa kwa mitundu ya anthu, anthu padziko lapansi anamukhulupilila, ndiponso analandilidwa kumwamba mu ulemelelo.’

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani