Lachitatu, April 15
Muzikondana.—Yoh. 15:12.
Nthawi zonse anthu a Yehova amathandizana. (2 Akor. 8:4) Komabe iwo nthawi zina amafunika kulimba mtima kuti achite zimenezi. Mwachitsanzo kukakhala nkhondo, akulu amazindikira kuti abale ndi alongo awo amafunika kulimbikitsidwa, kupatsidwa zinthu zofunika pa moyo komanso chakudya chauzimu. Chifukwa chokonda nkhosa, iwo amalolera kuika moyo wawo pangozi kuti apereke thandizo lofunika kwa abale awo. Pa nthawi ngati imeneyi, timafunika kuchita zinthu mogwirizana. Tiyenera kutsatira malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumaonanso zimene anakonza pa nkhani yokonzekera ngozi komanso kutsatira malangizo a gulu pa nthawi ya ngoziyo. (1 Akor. 14:33, 40) Muzikhala olimba mtima koma muzichita zinthu mosamala. (Miy. 22:3) Muziganiza kaye musanachite zinazake. Muziyesetsa kuti mukhale otetezeka. Muzidalira Yehova. Iye angakuthandizeni kuti mupereke thandizo kwa abale anu muli otetezeka. w24.07 4 ¶8; 5 ¶11
Lachinayi, April 16
Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova, . . . ndipo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.—Sal. 18:6.
Mfumu Davide ankadziwa Yehova ndipo ankamudalira. Pamene Mfumu Sauli komanso adani ake ankafuna kumupha, Davide anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Mulungu atayankha pemphero lake n’kumupulumutsa, Davide ananena kuti: “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Polankhula mawu amenewa, Davide sankatanthauza kuti ankangodziwa kuti Mulungu aliko. Buku lina linanena kuti Davide ankakhulupirira kuti Yehova “ndi Mulungu wamoyo yemwe nthawi zonse amathandiza anthu ake.” Zimene zinachitika pa moyo wa Davide zinamutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo ndipo zinamulimbikitsa kuti apitirize kumutumikira komanso kumutamanda. (Sal. 18:28, 29, 49) Kukhulupirira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo kungatithandize kuti tizimutumikira ndi mtima wonse. Tidzapeza mphamvu kuti tizipirira mayesero komanso tizichita zambiri pomutumikira. Tidzakhalanso ofunitsitsa kupitiriza kukhala naye pa ubwenzi. w24.06 20-21 ¶3-4
Lachisanu, April 17
Musalole kuti aliyense akusocheretseni.—2 Ates. 2:3.
Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a mtumwi Paulo opita kwa Atesalonika? Tikamva zinazake zomwe sizikugwirizana ndi zomwe timaphunzira m’Baibulo kapenanso mphekesera, tiyenera kuchita zinthu mwanzeru. M’dziko lomwe poyamba linkatchedwa Soviet Union, adani athu anafalitsa kalata yooneka ngati ikuchokera kulikulu lathu. Kalatayo inalimbikitsa abale ena kuti apange kagulu kena kapadera koima pakokha. Kalatayo inkaoneka ngati yachokeradi kulikulu lathu. Koma abale okhulupirika sanapusitsidwe. Iwo anazindikira kuti uthenga wa m’kalatayo sunkagwirizana ndi zomwe akhala akuphunzitsidwa. Masiku anonso adani athu amagwiritsa ntchito njira zamakono pofuna kutisokoneza kapena kutichititsa kuti tisamagwirizane. M’malo molola kuti wina aliyense “asinthe maganizo [athu]” omwe ndi olondola, tingadziteteze poganizira mosamala ngati zimene tamva kapena kuwerenga zikugwirizana ndi mfundo za choonadi zomwe tikuzidziwa kale.—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:1. w24.07 12 ¶14-15