Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 June tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yomwe ndi Yofunika Kwambiri kwa Ife
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Pangano la Mulungu ndi “Bwenzi” Lake Likupindulitsa Kale Mamiliyoni Ambiri
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yofunika kwa Ife
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mapangano Ophatikizapo Chifuno Chosatha cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 June tsamba 31

MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA

Kodi Paulo ankanena za mapangano awiri ati pa Agalatiya 4:24?

Atafotokoza za Sara yemwe anali mkazi wa Abulahamu komanso Hagara, yemwe anali kapolo wawo wamkazi, mtumwi Paulo ananena kuti: “Zinthu zimenezi zili ndi tanthauzo lophiphiritsira, chifukwa azimayi amenewa akuimira mapangano awiri.”(Agal. 4:​22-24.) Poyamba tinkakhulupirira kuti mapangano awiriwa ndi pangano la Chilamulo komanso pangano latsopano. Koma titafufuzanso nkhaniyi, taona kuti pakufunika kusintha. Zikuoneka kuti Paulo sankanena za pangano latsopano koma ankanena zokhudza pangano la Abulahamu. Taganizirani mfundo zotsatirazi.a

Paulo anayerekezera Hagara yemwe anali kapolo ndi phiri la Sinai. (Agal. 4:25) Hagara ankatanthauza pangano la Chilamulo limene linakhazikitsidwa paphiri la Sinai mu 1513 B.C.E. (Eks. 19:​5, 6) Palibe munthu yemwe si wangwiro amene akanatha kutsatira Chilamulo popanda kulakwitsa chilichonse. Choncho chilamulocho chinkakumbutsa Ayuda kuti anali akapolo a uchimo. Panganoli likanathandizanso Aisiraeli kudzazindikira Mesiya, yemwe ndi munthu yekhayo amene akanatha kutsatira Chilamulo osalakwitsa chilichonse. Mesiya atapereka moyo wake wangwiro kuti ukhale nsembe, anachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu omwe si angwiro amasulidwe ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Agal. 3:​19, 24, 25) Yesu atakwaniritsa cholinga cha Mulungu chimenechi, Chilamulo chinasiya kugwira ntchito.—Aroma 10:4.

Paulo anasiyanitsa Hagara ndi Sara, “mkazi yemwe anali mfulu,” amene anabereka mwana “kudzera mu lonjezo.” (Agal. 4:23) Lonjezo limeneli linali pangano la Abulahamu. (Agal. 3:29; 4:​28, 30) Panganoli timalipeza palemba la Genesis 22:​18, lomwe limati: “Kudzera mwa mbadwa yako, mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.”

Pangano limene Yehova anapanga ndi Abulahamu linafotokoza mfundo zina zokhudza lonjezo limene Yehova anapanga m’munda mwa Edeni. (Gen. 3:15) Linasonyeza kuti “mbadwa” yolonjezedwa idzachokera mumzere wa Abulahamu. Paulo anafotokoza kuti ‘mbadwayi,’ choyamba ikuimira Yesu Khristu. Komanso a 144,000 omwe ndi “a Khristu,” amene adzalamulire naye limodzi kumwamba, ndi mbali ya mbadwa yapadera imeneyi. (Agal. 3:​16, 29; Chiv. 14:​1-3) Kukwaniritsidwa kwa lonjezo limene Yehova anapangana ndi Abulahamu kudzachititsa kuti anthu amene amavomereza komanso kumvera Yesu adzapeze madalitso ambiri.

Ndiye kodi Paulo ankafuna kutiphunzitsa chiyani pa “tanthauzo lophiphiritsira” limene anafotokoza? Mfundo yake inali yakuti ngati Ayuda a m’nthawi yake akanakakamirabe kuti azisunga Chilamulo, akanapitiriza kukhala akapolo ngati mmene zinalili ndi Hagara. Koma ngati akanavomereza Yesu Khristu, yemwe ndi mbali yoyamba ya “mbadwa” ya Abulahamu, akanakhala pa ufulu ngati Sara. Akanamasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Yoh. 8:​32-34) Iwo akanakana Yesu, zikanasonyeza kuti sanamvetse cholinga chachikulu cha pangano la Chilamulo, chimene chinkawatsogolera kwa Khristu.

Anthu ambiri a ku Galatiya amene Paulo anawalembera kalatayi sanali Ayuda ndipo anali asanatsatirepo Chilamulo. Anthu ena olimbikitsa Chiyuda ankanena kuti Akhristuwa azitsatira Chilamulo, kuphatikizapo zoti azidulidwa. Paulo anasonyeza kuti kuchita zimenezi kukanakhala kusaganiza bwino. Sankafunika kukhala ‘akapolo’ a Chilamulo popeza anali kale pa “ufulu” chifukwa anali atavomereza Khristu.—Agal. 5:​1, 10-14.

a Zimenezi zikusintha zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2006, tsamba 10-12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena