ZINTHU ZOCHITITSA CHIDWI ZA M’BAIBULO
Maukonde Otchulidwa M’Baibulo
Anthu amene amawerenga Baibulo amadziwa kuti ena mwa otsatira a Yesu anali asodzi. (Maliko 1:16-20) Iwo ankagwiritsa ntchito maukonde akamapha nsomba m’Nyanja ya Galileya.
Maukonde ankapangidwa poluka twayini kapena ulusi. Kukula kwa mabowo a maukondewa, kunkatengera mtundu wa nsomba zomwe akufuna kugwira. Nthawi zambiri kunsi kwa maukonde ang’onoang’ono ankamangirirako mwala kapena zinthu zina zolemera kuti maukondewa azitha kumira. Pamene maukonde akuluakulu ankakhala ndi zinthu zolemera kunsi ndipo pamwamba pake pankakhala zinthu zoti zitha kuyandama monga timatabwa.
Maukonde anali odula. Ankatha kung’ambika chifukwa cha miyala ya pansi pa nyanja kapena kuchuluka kwa nsomba zimene asodzi agwira. (Luka 5:6) Baibulo limanena kuti nthawi ina Yakobo ndi Yohane ‘ankasoka maukonde awo.’ N’kutheka kuti ankagwiritsa ntchito singano wamkulu ndi ulusi. (Mat. 4:21) Asodzi ayenera kuti ankachita zimenezi akabwera kopha nsomba. Luka anafotokozanso kuti asodzi “ankachapa maukonde awo” kuti achotse matope. (Luka 5:2) Pambuyo pake ankawayanika n’cholinga choti asawole.—Ezek. 47:10.
Yesu anaitana anthu amene ankadziwa bwino ntchito yausodzi kuti akhale “asodzi a anthu.”