JULY 6-12, 2026
NYIMBO NA. 98 Malemba Anauziridwa ndi Mulungu
N’chifukwa Chiyani Mfundo za M’Baibulo N’zofunika Kwambiri?
“Mupereke matupi anu ngati . . . utumiki wopatulika pogwiritsa ntchito luso la kuganiza.”—AROMA 12:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza kudziwa kuti mfundo ndi chiyani komanso zimene tingachite kuti tizitha kuzizindikira tikamawerenga Baibulo.
1-2. (a) Kodi Baibulo linalembedwa liti? (b) N’chifukwa chiyani Baibulo lili lothandizabe masiku ano?
BAIBULO ndi buku lakale kwambiri. Linayamba kulembedwa pafupifupi zaka 3,500 zapitazo ndipo linamalizidwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Komabe “mawu a Mulungu” amene amapezeka m’bukuli adakali amoyo komanso amphamvu mpaka pano. (Aheb. 4:12; 2 Tim. 3:16, 17) Anthu mamiliyoni ambiri amatsatira malangizo a m’Baibulo ndipo amawathandiza kusankha zinthu mwanzeru komanso kukhala osangalala.
2 Ndiye n’chifukwa chiyani buku lakale chonchi lili lothandizabe masiku ano? Pali zifukwa zikuluzikulu ziwiri. Choyamba, uthenga wa m’Baibulo umachokera kwa “Mulungu wamoyo,” yemwe ndi Mlengi wanzeru kuposa aliyense. (1 Tim. 4:10; Aroma 16:26, 27) Chachiwiri, m’Baibulo muli mfundo za choonadi zochokera kwa Mulungu zomwe sizisintha ngakhale patapita nthawi. N’chifukwa chake malangizo ake amatithandiza pa mavuto athu masiku ano ngati mmene anathandizira anthu ena m’mbuyomu.
3. Kodi tipeza mayankho a mafunso ati munkhaniyi?
3 Kodi mfundo za m’Baibulo n’chiyani? N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kwa ife masiku ano? Tingatani kuti tizizindikira mfundo tikamawerenga Baibulo? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa. Tionanso mmene zimene Yesu anaphunzitsa zinathandizira anthu kumvetsa mfundo za m’Mawu a Mulungu.
KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’CHIYANI?
4. Kodi mfundo za m’Baibulo n’chiyani?
4 Mfundo za m’Baibulo ndi mfundo za choonadi ndipo malamulo a Mulungu amachokera pa mfundo zimenezi. (Mat. 22:37) Nthawi zina zimakhala zosavuta kuzindikira mfundo mulamulo linalake koma mfundo ndi zapamwamba tikaziyerekezera ndi malamulo. Malamulo amatha kungogwira ntchito pa zinthu zinazake, akhozanso kuperekedwa pa nthawi inayake kapena pa zochitika zinazake. Koma mfundo za m’Baibulo zimasonyeza mmene Yehova amaganizira pa nkhani zosiyanasiyana. Tinganene kuti malamulo amapangidwa chifukwa cha mfundo zinazake. Pa lamulo lililonse lomwe Yehova amatipatsa, pamakhala chifukwa chomveka. Koma mfundo zomwe zachititsa kuti pakhale lamulolo zikhoza kugwira ntchito pa zochitika komanso pa nthawi zosiyanasiyana. (Sal. 119:111) Lamulo limatha kusintha koma mfundo sizisintha kapena kusiya kugwira ntchito.—Yes. 40:8.
5. Perekani chitsanzo chosonyeza kusiyana kwa lamulo ndi mfundo. (Onaninso zithunzi.)
5 Kuti timvetse bwino kusiyana kwa lamulo ndi mfundo, tiyeni tiganizire chitsanzo ichi: Mayi angauze mwana wamng’ono kuti, ‘Usagwire mbaula.’ Limeneli ndi lamulo. Koma mfundo ya pa lamuloli ndi yakuti: Usagwire chinthu chotentha chifukwa chikhoza kukuwotcha. Mfundo imeneyi sikuti ikungogwira ntchito pa mbaula yokha. Ikhoza kugwiranso ntchito pa aironi yositira zovala kapena chinthu chilichonse chomwe chingamuwotche. Ndipotu mfundoyi imagwira ntchito kulikonse osati kunyumba kokha. N’zoona kuti mwanayo akamakula akhoza kumagwiritsa ntchito mbaula komabe angafunike kumachita zinthu mosamala kuti asamaigwire m’njira yoti ingamuwotche. Choncho lamulo lingathe kusintha koma mfundo yake simasintha.
Lamulo likhoza kusintha koma mfundo ya lamulolo simasintha (Onani ndime 5)
KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’ZOFUNIKA BWANJI?
6. (a) Kodi Yehova anatipatsa chiyani m’Mawu ake? (b) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatilemekeza?
6 Chifukwa chotikonda, Yehova anatipatsa malamulo kuti tizitha kupewa zinthu zomwe zingativulaze. (Yak. 2:11) Kuwonjezera pamenepa amatithandizanso kumvetsa mfundo, kapena kuti chifukwa chimene amatipatsira malamulowo. Pogwiritsa ntchito Mawu ake, amatitsogolera pambali zosiyanasiyana za moyo wathu pamene palibe malamulo achindunji. Mfundo za m’Baibulo zimatithandiza kusankha zinthu mwanzeru komanso kuchita zoyenera. Potipatsa mfundozi Yehova amasonyeza kuti amatilemekeza ndipo amatilola kusankha zinthu zimene zimasonyeza kuti timamukonda komanso kuti timakonda mfundo zake.—Agal. 5:13.
7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti mfundo za m’Baibulo n’zofunika kwambiri. (Onaninso chithunzi.)
7 Kuti timvetse mmene mfundo za m’Baibulo zimatithandizira, ganizirani za zikwangwani za pamsewu zimene madalaivala amaona m’madera ena. Zambiri mwa zikwangwanizi zimasonyeza malamulo amene ngati munthu sangatsatire amalandira chilango. Zikwangwanizi zimasonyeza liwiro limene dalaivala angayendetsere galimoto yake komanso nthawi imene angafunike kuima pa nsewu. Komabe zikwangwani zina zimathandiza dalaivala kudziwa zoopsa zimene angakumane nazo. Mwachitsanzo, zikhoza kumuchenjeza kuti msewu ndi woterera kapena ndi malo amene nyama zimawolokerapo. Dalaivala wabwino amachita zinthu mwanzeru ndipo amayendetsa mosamala akaona zikwangwani zosonyeza kuti pali zoopsa. Mwachitsanzo ngati kukugwa mvula kapena kuli chifunga, amachepetsa liwiro kuti asachite ngozi. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu amapewa zinthu zimene Mawu a Mulungu amaletsa mwachindunji. Amapewanso kuganizira kapena kuchita zinthu zimene zingawapangitse kuphwanya malamulo a Mulungu. Kuti athe kuchita zimenezi amafunika kukhala oganiza bwino.
Zikwangwani zambiri zapamsewu zimachenjeza madalaivala zokhudza zinthu zimene zingachititse ngozi. Ndi mmenenso zilili ndi mfundo za m’Baibulo (Onani ndime 7)
8. Mogwirizana ndi Aroma 12:1,2, kodi timaphunzira chiyani tikamafufuza mfundo za m’Baibulo?
8 Kufufuza mfundo za m’Baibulo komanso kuzitsatira kumatithandizanso m’njira zina. Mwachitsanzo, timaphunzira komanso kumvetsa mmene Yehova amaganizira pa nkhani zosiyanasiyana. Tikamawerenga nkhani za m’Baibulo, timafufuza mfundo zomwe tingazigwiritse ntchito. Timadzifunsa chifukwa chake Yehova anaika nkhanizi m’Mawu ake komanso mmene zingatithandizire. Tikamachita zimenezi timaphunzira kugwiritsa ntchito “luso la kuganiza” potumikira Yehova. Ndipo timazindikira “chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—Werengani Aroma 12:1, 2.a
9. Kodi kutsatira mfundo za m’Baibulo kumatithandizanso bwanji? (Aheb. 5:13, 14)
9 Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kuti tikhale Akhristu olimba mwauzimu. Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Werengani Aheberi 5:13, 14.) Ana amafunika malamulo ambiri kuti adziwe zoyenera kuchita pa zinthu zosiyanasiyana. Iwo angamatsatire malamulowo chifukwa choopa kuti alandira chilango. Koma Yehova amachita nafe zinthu monga anthu akuluakulu osati ana. Iye amakhulupirira kuti tikhoza kumasankha zinthu mogwirizana ndi zimene amafuna ndipo tikachita zimenezo amasangalala kwambiri.—Sal. 147:11; Miy. 23:15, 26; 27:11.
TINGATANI KUTI TIZIZINDIKIRA MFUNDO ZA M’BAIBULO?
10. Kodi tingatani kuti tizizindikira mfundo za m’Baibulo?
10 Tikamawerenga Baibulo ndi bwino kuti tizifufuza mfundo zotithandiza kumvetsa mmene Yehova amaganizira komanso mmene amamvera pa nkhani zosiyanasiyana. Tingapezenso mfundo tikamaganizira chifukwa chake anatipatsira malamulo enaake. Tikamamvetsa bwino zifukwazo m’pamenenso timadziwa bwino Yehova. Koma kuti tizimvetsa mmene Mulungu amaganizira, tiyenera kumupempha kuti atithandize komanso kuyesetsa kukulitsa luso lathu loganiza. (Miy. 2:10-12) Tingadzifunse mafunso ngati awa: ‘N’chifukwa chiyani Yehova anapereka lamuloli? Ngati Yehova sasangalala ndi khalidwe limeneli, ndiye kodi angamve bwanji ngati nditachita khalidwe lofanana ndi limeneli? Kodi ndikuphunzira chiyani pa nkhaniyi, nanga ndingazigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanga?’ Tikamvetsa chifukwa chake Yehova anapereka malamulo enaake komanso zimene tikuphunzira pa nkhani za m’Baibulo, timatha kusankha bwino zochita pa moyo wathu, zomwe zimagwirizana ndi zimene Yehova Mulungu amafuna.
11. Kodi Yesu anatisonyeza bwanji mmene tingapezere mfundo za m’Baibulo pa ulaliki wapaphiri? (Onaninso zithunzi.)
11 Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anatisonyeza mmene tingapezere mfundo za m’Baibulo. Tiyeni tione zitsanzo zitatu. Pa chitsanzo chilichonse Yesu ankayamba ndi kutchula lamulo. Kenako ankafotokoza mfundo yake kapena chifukwa chake lamulolo linaperekedwa. Tikamaganizira zimene Yesu anaphunzitsazi, tiona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimenezi masiku ano. Tionanso mmene mfundozi zingatithandizire kuti tizisankha zinthu mwanzeru.
Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anatisonyeza mmene tingapezere mfundo pa malamulo a Mulungu (Onani ndime 11)
12. Kodi ndi mfundo imodzi iti yomwe ili pa Mateyu 5:21, 22? (Onaninso chithunzi.)
12 Werengani Mateyu 5:21, 22. “Musaphe munthu.” Kodi imodzi mwa mfundo ya pa lamuloli ndi yoti chiyani? Yehova safuna kuti tizidana ndi ena kaya m’zochita, zolankhula kapenanso m’maganizo. Yesu anasonyeza kuti ngakhale zitakhala kuti munthu sanaphe mnzake, akhoza kuphwanya mfundo za mulamuloli ngati atamadana ndi m’bale wake. Ngati munthu atapitiriza kupsera mtima m’bale wake kapena kumunyoza amakhalabe kuti “wapalamula mlandu.” Ndipotu zimenezi n’zomwe zimachititsa kuti munthu afike popha mnzake.—1 Yoh 3:15.
13. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Mateyu 5:21, 22 pa moyo wathu? (Onaninso zithunzi.)
13 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Mateyu 5:21, 22 masiku ano? Tizipewa kusunga chakukhosi kapena kukhala wokwiya. (Lev. 19:18; Yobu 36:13) Chifukwa kuchita zimenezi kungachititse kuti tikhale ndi chidani mumtima mwathu zomwe zingatipangitse kuti tilankhule kapena kuchita zinthu zomwe zingakhumudwitse komanso kuvulaza ena. (Miy. 10:12) Zinthuzi zikuphatikizapo miseche komanso kulankhula zoipa zokhudza anthu ena zomwe zikhoza kuwononga mbiri yawo. (Miy. 20:19; 25:23) Ngakhale kuti pa nthawiyo kunalibe intaneti, malo ochezera a pa intaneti kapena mapulogalamu otumizirana mameseji, Yesu anafotokoza mfundo zomwe zimathandiza Akhristu olimba mwauzimu kupewa mavuto amene angakhalepo akamagwiritsa ntchito zinthu zamakonozi. Choncho nthawi zonse tizipewa kulankhula zinthu zoipa zomwe zingachititse kuti anthu asiye kulemekeza munthu wina.
(Onani ndime 12-13)
14. Kodi ndi mfundo iti yomwe ili pa lamulo la pa Mateyu 5:27, 28? (Onaninso chithunzi.)
14 Werengani Mateyu 5:27, 28. “Musachite chigololo.” Kodi pa lamuloli pali mfundo yotani? Yehova amadana ndi chiwerewere komanso sasangalala anthu akamaganizira zinthu zoti zingawachititse chiwerewere. Yesu anafotokoza kuti ngati munthu wokwatira akuyang’anitsitsa mkazi (yemwe si mkazi wake) mpaka kufika pomulakalaka ndiye kuti wachimwa. Choncho tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tisamaganizire zinthu zolakwika, ngakhale kuti zimenezi zingafunike kuchita khama kwambiri. (Mat. 5:29, 30) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa Akhristu omwe sali pabanja.
15. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Mateyu 5:27, 28 masiku ano? (Onaninso zithunzi.)
15 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Mateyu 5:27, 28 masiku ano? Tiyenera kupewa kumangoganizira zinthu zachiwerewere. (2 Sam. 11:2-4; Yobu 31:1-3) Apatu ndi zodziwikiratu kuti Mkhristu wolimba mwauzimu amapewa kuonera zolaula za mtundu uliwonse. Iye saganiza kuti popeza akungoonera chabe zinthu zolaulazo, ndiye kuti palibe cholakwika chilichonse. Sadziikira kumbuyo n’kumaganiza ngati anthu a m’dzikoli omwe amaona kuti zolaula zina si zoipa kwenikweni. M’nthawi ya Yesu kunalibe zipangizo zamakono, mafilimu kapena zithunzi zojambula ndi kamera. Ngakhale zili choncho, Yesu anatiphunzitsa mfundo imene imatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa zinthu zomwe zimaikidwa pa zipangizo zamakono. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa kuti Yehova sasangalala ngakhale pang’ono ndi zinthu zomwe ndi zofala masiku ano monga kukambirana, kutumizirana zithunzi, mavidiyo komanso mameseji okhudza zinthu zachiwerewere. Kutsatira mfundo imeneyi kungathandize munthu wokwatira kuti asachitire zachinyengo mwamuna kapena mkazi wake. (Mal. 2:15) Kungathandizenso Akhristu onse, kaya ali pa banja kapena ayi, kupewa chilichonse chimene chingawachititse chiwerewere.—Miy. 5:3-14.
(Onani ndime 14-15)
16. Kodi ndi mfundo iti yomwe ili pa lamulo la pa Mateyu 5:43, 44? (Onaninso chithunzi.)
16 Werengani Mateyu 5:43, 44. “Uzikonda mnzako.” Kodi pa lamuloli pali mfundo yotani? Yehova amafuna tiziona kuti anthu onse ndi anzathu ndipo tiziwakonda. N’zomvetsa chisoni kuti Ayuda a m’nthawi ya Yesu ankaganiza kuti lamuloli limatanthauza kuti azikonda Ayuda anzawo okha n’kumadana ndi adani awo. Koma Yesu ankadziwa kuti chimenechi si chifukwa chimene Yehova anaperekera lamuloli. Iye ankadziwa kuti Atate wathu wachikondi amafuna kuti tiziona aliyense monga mnzathu posatengera mtundu wake kapena kumene akuchokera.—Mat. 5:45-48.
17. Kodi kutsatira mfundo ya pa Mateyu 5:43, 44 kungatithandize bwanji pa moyo wathu? (Onaninso zithunzi.)
17 Kodi tingatsatire bwanji mfundo ya pa Mateyu 5:43, 44 masiku ano? Kukonda anzathu kumatithandiza kuti tisamalowerere nkhondo ndiponso mikangano ya m’dzikoli. (Yes. 2:4; Mika 4:3) Chikondichi chimatithandizanso kuti tizichita zinthu mokoma mtima ndi anthu omwe timasiyana nawo mtundu, kochokera kapena chipembedzo. (Mac. 10:34, 35) Timathanso kukhululukira anthu omwe atilakwira kapena amene alakwira anthu omwe timawakonda.—Mat. 18:21, 22; Maliko 11:25; Luka 17:3, 4.
(Onani ndime 16-17)
TSIMIKIZANI MTIMA KUTI MUZITSATIRA MFUNDO ZA M’BAIBULO PA MOYO WANU
18. (a) Kodi tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuchita chiyani? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhani yotsatira?
18 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa amachita nafe zinthu monga anthu akuluakulu osati ana. Iye amafuna kuti tizigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo zomwe zimatithandiza kusankha zinthu mwanzeru. (1 Akor. 14:20) Tikamasankha zinthu tizionetsetsa kuti ‘tikupitiriza kuzindikira chifuniro cha Yehova.’ (Aef. 5:17) Kukonda Yehova, osati kuopa kulangidwa, kumatithandiza kuti tizisankha zinthu mogwirizana ndi zimene amafuna. Koma pali mphatso inanso imene imatithandiza pa nkhaniyi, yomwe ndi chikumbumtima chathu. Munkhani yotsatira tidzakambirana za mphatso imeneyi.
NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe
a Nthawi zambiri Akhristu amalimbikitsidwa kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo. Timafunika kuganizira mavesi osiyanasiyana a m’Baibulo n’kugwiritsa ntchito mfundo za m’mavesiwo kuti tisankhe zinthu mwanzeru. Tiyenera kumagwiritsa ntchito luso loganiza limene Yehova anatipatsa kuti tizisankha zinthu zomwe angasangalale nazo komanso kuzidalitsa. N’zimenenso Akhristu ambiri m’nthawi ya atumwi ankafunika kuphunzira kumachita. Asanakhale Akhristu, Ayuda ankatsatira malamulo ambirimbiri amene atsogoleri awo achipembedzo anapanga.