JULY 13-19, 2026
NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala
Muziphunzitsa Chikumbumtima Chanu Pogwiritsa Ntchito Mfundo za M’Baibulo
“Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”—AGAL. 6:5.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pophunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitithandiza kusankha bwino zinthu.
1-2. (a) Kodi Adamu ndi Hava anapatsidwa mphatso yotani? (b) Kodi akanasonyeza bwanji kuti ankayamikira mphatsoyi?
NYAMA zimachita zinthu mwachibadwa ndipo mashini ambiri amapangidwa m’njira yakuti azigwira ntchito inayake. Koma anthu ndi osiyana ndi zonsezi. Potilenga, Mulungu anatipatsa mphatso yapadera imene Akhristu amaiona kuti ndi yamtengo wapatali. Mphatsoyi ndi ufulu wosankha ndipo imatithandiza kuti tizisankha tokha zochita komanso zimene timakonda pa moyo wathu. Baibulo limatiuza kuti munthu woyamba Adamu, analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, kapena kuti anali wofanana naye. (Gen. 1:26, 27) Monga zolengedwa zanzeru, Adamu ndi Hava anapatsidwa ufulu wosankha okha zochita.
2 Yehova sanapatse Adamu ndi Hava malamulo ambirimbiri. Anangowauza kuti azisamalira dzikoli, abereke ana komanso azilemekeza udindo wa Mulungu wowalamulira. (Gen. 1:28; 2:16, 17) Kodi Adamu ndi Hava akanasonyeza bwanji kuti ankayamikira Mulungu yemwe anawapatsa mphatso ya ufulu wosankha? Poganizira zonse zimene Yehova anawapatsa, iwo ankayenera kumvera malamulo osavutawa chifukwa chomukonda komanso kufuna kumusangalatsa.—Miy. 23:15.
3. Kodi Adamu ndi Hava anagwiritsa ntchito bwanji ufulu wawo wosankha?
3 Monga mmene Baibulo limasonyezera, Adamu ndi Hava sanagwiritse ntchito mwanzeru ufulu wawo wosankha. Iwo anasankha kusamvera Yehova. Anachita zimenezi chifukwa chodzikonda osati chifukwa chokonda Yehova kapena kumuyamikira pa zimene anawachitira. (Gen. 3:1-7) Mpaka pano tikuvutikabe ndi zimene anasankhazi.—Aroma 5:12.
4. (a) Mogwirizana ndi Agalatiya 6:5, kodi tonsefe tiyenera kuchita chiyani? (b) Kodi munkhaniyi tikambirana za mphatso ina iti?
4 Masiku ano, moyo wathu ndi wovuta chifukwa timafunika kusankha zochita pa zinthu zambiri tsiku lililonse. (Werengani Agalatiya 6:5.) Zina mwa zinthu zimene timafunika kusankha zimakhala zosavuta koma zina zimakhala zovuta kwambiri. Ndiye kodi tingatani kuti tizisankha zinthu zomwe zingasangalatse Yehova? Choyamba timafunika kuvomereza kuti timafunika kuthandizidwa ndi Yehova. (Miy. 16:3; Yer. 10:23) Ngakhale Yesu yemwe anali wangwiro, ankazindikira kuti ankafunika kuthandizidwa ndi Mulungu. (Aheb. 5:7) Monga anthu omwe si angwiro, ifeyo timafunika kuthandizidwa kwambiri kuposa mmene zinalili ndi Yesu. Tsopano tiyeni tikambirane mphatso ina yomwe Mulungu anatipatsa, imene imatithandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru, yomwe ndi chikumbumtima.
KODI CHIKUMBUMTIMA N’CHIYANI?
5. (a) Kodi chikumbumtima n’chiyani? (b) Kodi chikumbumtima chimatithandiza bwanji? (Aroma 2:14, 15)
5 Chikumbumtima ndi umunthu wathu wamkati womwe umatithandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Ngakhale munthu amene sadziwa malamulo a Mulungu ali ndi chikumbumtima. (2 Akor. 4:2) Chikumbumtima chili ngati woweruza wamumtima mwathu, yemwe amatiuza kuti zomwe tikuganiza kapena kuchita, n’zabwino kapena zoipa. (Werengani Aroma 2:14, 15.) Chikumbumtima chathu chimatha kutichenjeza kuti tisachite zinthu zimene tikudziwa kuti n’zoipa. (1 Sam. 26:8-11) Kapena chimatha kutilimbikitsa kuti tichite zinthu zimene tikudziwa kuti n’zoyenera. Komabe kukhala ndi mphatso ya ufulu wosankha sikukutanthauza kuti Yehova amasangalala ndi chilichonse chimene tingasankhe. Chikumbumtima chathu chiyenera kutithandiza kuzindikira ngati zimene tikufuna kusankha ndi zabwino kapena zoipa.
6. N’chifukwa chiyani si nthawi zonse pamene chikumbumtima chathu chimatithandiza kusankha zoyenera?
6 N’zomvetsa chisoni kuti si nthawi zonse pamene chikumbumtima chathu chimatithandiza. Popeza si ife angwiro, chikumbumtima chathunso si changwiro ndipo chimakhudzidwa ndi mmene tinaleredwera, chikhalidwe chathu komanso zilakolako zoipa. Baibulo limati chikumbumtima chikhoza kukhala ‘chofooka,’ ‘choipitsidwa,’ ‘cha ngati chipsera chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto’ kapenanso “choipa.” (1 Akor. 8:12; Tito 1:15; 1 Tim. 4:2; Aheb. 10:22) Chikumbumtima choterechi sichingatithandize kusankha bwino zinthu. Chimakhala ngati sikelo yowonongeka yomwe ikufunika kukonzedwa. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tizichiphunzitsa kuti chikhale chabwino. (1 Pet. 3:16) Ndiye kodi tingachite bwanji zimenezi?
MMENE TINGAPHUNZITSIRE CHIKUMBUMTIMA CHATHU
7-8. (a) N’chiyani chingatithandize kuphunzitsa chikumbumtima chathu? (b) Kodi mfundo za m’Baibulo zimatithandiza bwanji? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.)
7 Kodi tingaphunzitse bwanji chikumbumtima chathu? Tiziwerenga Baibulo nthawi zonse kuti tidziwe zinthu zimene Yehova amaziona kuti n’zoyenera kapena n’zosayenera. Tikamaphunzira malamulo a Mulungu, timamvetsa mmene iye amaganizira. Koma monga tinaphunzirira munkhani yapita ija, malamulo amagwira ntchito pa zinthu zochepa. N’chifukwa chake timafunika kuphunzira mfundo za m’Baibulo kuti zizitithandiza kumvetsa mmene Yehova amaonera komanso mmene amamvera pa zinthu zosiyanasiyana.—Yes. 55:9.
8 Moyo wathu tingauyerekeze ndi ulendo wa m’chipululu momwe mulibe misewu, njira komanso zikwangwani. Tikhoza kudziwa kumene tikuyenera kulowera poona dzuwa kapena nyenyezi. Koma zingakhale bwino kwambiri titakhala ndi mapu osonyeza zinthu zimene tiziziona tikamayenda. Mapuwo angatithandize kudziwa ngati tikupita koyenera kapena ngati tasochera. Cholinga chathu chachikulu ndi kusangalatsa Yehova. Baibulo lili ngati mapu amene amatitsogolera koyenera kupita. Ndipo mfundo za m’Baibulo zili ngati zizindikiro zomwe timaziona tikamayenda. Tikamatsatira mfundozo timakwanitsa cholinga chathu chomwe ndi kusangalatsa Yehova.
Mfundo za m’Baibulo zili ngati zizindikiro zimene timazipeza mumsewu zomwe zimatitsimikizira kuti tikupita koyenera (Onani ndime 8)
9. Kodi lemba la Aroma 9:1, limatchulanso chinthu china chiti chomwe chimatithandiza kuphunzitsa chikumbumtima chathu?
9 Kuti tikwanitse kuphunzitsa chikumbumtima chathu, timafunika kuthandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Werengani Aroma 9:1.) Mzimu wa Mulungu umatithandiza kumvetsa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Komanso umatilimbikitsa ndi kutipatsa mphamvu zochitira zimene Yehova amafuna. (Afil. 2:13) Koma kodi tingatani kuti mzimu wa Yehova uzitithandiza?
10. Kodi tingatani kuti mzimu woyera uzitithandiza? (Luka 11:10, 13)
10 Muzipempha mzimu woyera. (Werengani Luka 11:10, 13.) Sitikayikira kuti Yehova amapereka mzimu wake woyera mowolowa manja. (Yoh. 3:34) Iye amapereka mzimuwu kwa anthu omwe amamumvera. (Miy. 1:23; Yak. 1:5) Koma kodi n’chiyaninso chingatithandize kuphunzitsa chikumbumtima chathu?
11. (a) Kodi cholinga chachikulu pa moyo wathu chiyenera kukhala chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuonetsetsa kuti chikumbumtima chathu n’chophunzitsidwa bwino ndipo chikugwira ntchito moyenera?
11 Nthawi zonse muzichita zinthu zomwe zimasangalatsa Yehova. (Miy. 8:34, 35) Chimenechi chiyenera kukhala cholinga chathu chachikulu pa moyo. Ngati timakumbukira cholinga chimenechi pa zinthu zonse zomwe timakumana nazo pa moyo wathu, tikhoza kuphunzitsa chikumbumtima chathu. Munthu wa chikumbumtima chophunzitsidwa bwino, amayesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera ndipo amaganiziranso mmene Yehovayo amamvera pa zinthu zosiyanasiyana. Tikaganizira mmene moyo ulili wovuta masiku ano, timaona kuti n’zofunika kwambiri kukhala ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino. Nthawi zambiri timakumana ndi zinthu zomwe sizinatchulidwe mwachindunji m’Baibulo. Zinthu zake zingakhale zokhudza zosangalatsa, ntchito, maphunziro komanso anthu omwe timacheza nawo. Ndiye tingadziwe bwanji kuti Yehova akusangalala ndi zimene tasankha pa nkhani ngati zimenezi?—2 Akor. 1:12.
12. Kodi n’chiyani chingatithandize kudziwa ngati chikumbumtima chathu chikutithandiza kusankha zinthu moyenera? (Aefeso 5:10)
12 Muziganizira mozama zimene mwawerenga m’Baibulo. (Sal. 49:3) Mukamawerenga Baibulo, muzifufuza mfundo zomwe zingakuthandizeni kumvetsa maganizo a Yehova. (Werengani Aefeso 5:10.) Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwa ngati chikumbumtima chanu chikukuthandizani kusankha zinthu mwanzeru pamene mukuyesetsa kuthana ndi mavuto anu. (Miy. 2:4-9, 11-13) Mfundozi zingakuthandizeni kuti muphunzitse bwino chikumbumtima chanu n’cholinga choti muzichita zimene Yehova amafuna.—Aheb. 5:14.
13. Kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani? Perekani chitsanzo.
13 Musamasankhe zinthu kenako n’kufufuza mfundo zoti zigwirizane ndi zimene mwasankhazo. Sitimafuna kuchita zinthu ngati Aisiraeli omwe anatsalira ku Yuda, Yerusalemu atawonongedwa mu 607 B.C.E. Iwo anauza Yeremiya kuti: “Yehova Mulungu wako atiuze njira yoti tiyendemo ndi zoti tichite.” (Yer. 42:3-6) Koma Ayudawo anali atasankha kale zochita. Ndiye zimene Yehova anawauza zitasemphana ndi zimene ankafuna, iwo sanamvere. Izi zinachititsa kuti akumane ndi mavuto aakulu. (Yer. 42:19-22; 43:1, 2, 4). Choncho tisanasankhe zochita, tizifufuza mfundo za m’Baibulo zomwe zikusonyeza maganizo a Yehova pa nkhaniyo, n’kuzitsatira.
14. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo tikamasankha zochita?
14 Muzigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo posankha zochita. (Mat. 7:24-29; Yak. 1:23-25) Tikamasankha zochita pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, timakhala tikuchita zinthu mogwirizana ndi mzimu woyera. Zotsatira zake Yehova amapitiriza kutipatsa mzimu wake. (Mac. 5:32) Koma ngati sitingalole kuti mzimu wa Yehova utitsogolere, tikhoza kupezeka kuti ‘tikuumvetsa chisoni’ kapena kuchita zinthu zosemphana ndi mzimuwo. (Aef. 4:30; Yes. 63:10; Mac. 7:51) Ndipotu Yehova akhozanso kusiya kutipatsa mzimu wake. (Sal. 51:11; 1 Ates. 5:19) Zimenezitu zingakhale zoopsa chifukwa timafunikira mphamvu zimene mzimu umatipatsa.—Aef. 3:16.
MMENE TINGAPEZERE MFUNDO ZA M’BAIBULO ZOMWE ZINGATITHANDIZE
15-16. (a) Kodi tingatani kuti tizipeza mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize? (b) Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingathandize wophunzira Baibulo kusiya kusuta fodya?
15 Muzigwiritsa ntchito zinthu zophunzirira. Kuti tikwanitse kutsatira mfundo za m’Baibulo, tingafunike kupeza mfundozo m’Malemba. Mwachitsanzo, bwanji ngati wophunzira Baibulo wanu sakumvetsa chifukwa chake ayenera kusiya kusuta fodya? Mwina angamaganize kuti: ‘Kusuta sikunatchulidwe m’Baibulo. Ndiye tingadziwe bwanji kuti n’kolakwika?’ Kodi mungamuthandize bwanji kupeza mfundo za m’Baibulo zomwe zingamuthandize kumvetsa kuti kusuta n’kolakwika? Chimodzi mwa zinthu zimene mungagwiritse ntchito ndi Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Mungamusonyeze mutu wakuti “Fodya.” Pamutuwu mukhoza kupezapo nkhani yakuti, “Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya? (Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 2014.) Ndiye kodi angapeze malemba komanso mfundo ziti akamawerenga nkhaniyi?
16 Tiyeni tione mfundo 5 zomwe zinatchulidwa munkhaniyi. (1) Sitiyenera kukhala akapolo a zinthu zomwe zingachititse kuti tife. (Aroma 6:16) (2) Tiyenera kupewa chilichonse chomwe chingawononge thanzi lathu. (2 Akor. 7:1) (3) Yehova amafuna kuti tizimutumikira ndi moyo wathu wonse. (Mat. 22:37) (4) Sitikuyenera kuwononga moyo wa anthu ena chifukwa cha zochita zathu. (Mat. 22:39; 1 Akor. 10:24) (5) Yehova angatipatse mphamvu kuti tizichita zoyenera. (Afil. 4:13) Choncho ngakhale kuti Baibulo silitchula mwachindunji zokhudza kusuta fodya, mfundo za munkhaniyi zingathandize wophunzira Baibulo kudziwa maganizo a Yehova pa nkhaniyi.
17. Kodi Akhristu omwe akukonzekera ukwati, angatani kuti apeze mfundo za m’Baibulo zomwe zingawathandize?
17 Kodi Akhristu omwe akukonzekera ukwati, angatani kuti apeze mfundo za m’Baibulo zomwe zingawathandize kusankha zinthu mwanzeru? Buku Lofufuzira Nkhani lingawathandizenso. Pamutu wakuti “Ukwati ndi Phwando la Ukwati,” pali nkhani zosiyanasiyana zomwe zili ndi mfundo za m’Baibulo. Taonani mfundo 6 izi zomwe zingawathandize. (1) Zinthu zonse zochitika pa ukwatiwo ziyenera kulemekeza Yehova. (1 Akor. 10:31, 32) (2) Tiyenera kuvala zovala zoyenera komanso zaulemu osati zomwe zingakhumudwitse ena. (1 Tim. 2:9; 1 Pet. 3:3, 4) (3) Tiyenera kupewa kuchita zinthu modzionetsera ngati mmene anthu m’dziko la Satanali amachitira. (Yoh. 17:14; Yak. 1:27; 1 Yoh. 2:15, 16) (4) Zinthu zonse ziyenera kuchitika mwadongosolo. (1 Akor. 14:40) (5) Phwando la ukwati siliyenera kukhala phwando la phokoso pamene anthu amamwa mowa mwauchidakwa. (Agal. 5:21) (6) Ayenera kusankha m’bale yemwe adzayang’anire zonse zomwe zidzachitike.—Yoh. 2:8, 9.
18-19. (a) Kodi ndi buku lina liti lomwe lingatithandize? (b) Kodi ndi mfundo ziti zomwe tingapeze m’bukuli zomwe zingatithandize kusankha mwanzeru pa nkhani ya zikondwerero? (Onani bokosi lakuti “Mfundo Zomwe Mungapeze.”)
18 Buku lina lomwe lingatithandize ndi lakuti, Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu. Bukuli lili ndi malemba pamitu yosiyanasiyana. Mukasankha mutu, muona mafunso omwe ali ndi malemba amene angakuthandizeni kumvetsa mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, Mkhristu akhoza kukhala kuti sakudziwa ngati n’zoyenera kuchita nawo chikondwerero chinachake. Akatsegula mutu wakuti “Zikondwerero,” angapeze kamutu kakuti, “Zikondwerero Zimene Akhristu Sachita Nawo.”
19 Taganizirani zina zomwe zili pakamutuka, monga funso lakuti: “N’chifukwa chiyani n’kulakwa kuchita nawo zikondwerero zokhudzana ndi chipembedzo chonyenga? (1 Akor. 10:21; 2 Akor. 6:14-18; Aef. 5:10, 11).” Pakamutuka palinso zitsanzo za zikondwererozi. Pakamutu kakuti: “Zikondwerero zam’dziko lanu,” pali malemba omwe angathandize Mkhristu kudziwa ngati akufunika kuchita nawo zikondwerero zokumbukira zimene dziko lawo linachita, nkhondo za mayiko, kapena zikondwerero zopereka ulemu kwa anthu otchuka umene Yehova yekha ndi amene ayenera kupatsidwa. Timathokoza kuti gulu la Yehova limatipatsa zinthu zimenezi kuti zitithandize kuphunzitsa chikumbumtima chathu.
MUZISONYEZA KUTI MULI NDI CHIKUMBUMTIMA CHOPHUNZITSIDWA BWINO
20. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tinaphunzitsa bwino chikumbumtima chathu?
20 Timayamikira kwambiri mphatso ya ufulu wosankha. Koma timazindikira kuti timafunikanso kuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti tizigwiritsa ntchito bwino ufulu wathu wosankhawo. Chikumbumtima chophunzitsidwa bwino chimatithandiza kusankha zinthu zogwirizana ndi zimene Yehova amafuna komanso zimene zingamulemekeze. Kuti zimenezi zitheke, timafunika kuthandizidwa ndi mzimu woyera. Choncho tiyenera kupitiriza kupempha mzimu woyera, n’kumaulola kuti uzititsogolera. Mfundo za m’Baibulo zimatithandizanso kuphunzitsa chikumbumtima chathu. Tiyeni tizigwiritsa ntchito bwino mphatso zimenezi ndipo tikatero tidzaona mmene Mawu a Mulungu adzatithandizire pa moyo wathu.—2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 4:12.
NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga Khala Wanzeru”