Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 April tsamba 20-25
  • Zimene Tingaphunzire kwa “Mulungu Amene Amatitonthoza pa Vuto Lililonse”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Tingaphunzire kwa “Mulungu Amene Amatitonthoza pa Vuto Lililonse”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE BAIBULO LIMANEZA ZOKHUDZA KUTONTHOZA
  • ZIMENE MUNGACHITE POTONTHOZA ENA
  • NGATI MUKUFUNIKA KUTONTHOZEDWA
  • Kulimbikitsa Anthu Omwe Amatumikira pa Beteli
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Sitili Tokha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • ‘Tonthozani Anthu Onse Olira’
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Tizilimbikitsa Anthu Amene Achitiridwa Zoipa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 April tsamba 20-25

JUNE 22-28, 2026

NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana

Zimene Tingaphunzire kwa “Mulungu Amene Amatitonthoza pa Vuto Lililonse”

“Tizitonthoza ena . . . chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.”—2 AKOR. 1:4.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene tingamatonthozere ena potengera chitsanzo cha Yehova komanso anthu amene amatsanzira Yehovayo.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kumatonthoza ena?

TONSEFE timavutika “chifukwa cha mayesero osiyanasiyana” ndipo timafunika kutonthozedwa komanso kulimbikitsidwa. (1 Pet. 1:6) Timayamikira ena akatitonthoza, choncho ifenso tisamachedwe kutonthoza amene akukumana ndi mavuto. (Mat. 7:12) Yehova, “Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,” amatiphunzitsa mmene tingatonthozere “amene akukumana ndi mayesero amtundu uliwonse.” Ndiye ‘tikamatonthozana,’ timakhala kuti tikumutsanzira. (2 Akor. 1:​3, 4; 1 Ates. 4:18) Timachita zimenezi osati chifukwa choti ndi udindo wathu koma chifukwa timakonda Akhristu anzathu. Munkhaniyi tikambirana (1) zimene kutonthoza kumatanthauza mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, (2) mmene tingatonthozere ena ndiponso (3) zimene tingachite tikafunika kutonthozedwa.

ZIMENE BAIBULO LIMANEZA ZOKHUDZA KUTONTHOZA

2. Kodi Baibulo likamanena za “kutonthoza” limatanthauza chiyani?

2 M’Baibulo mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kutonthoza” angatanthauze zinthu zosiyanasiyana potengera nkhani yake. Angatanthauze kulankhula zinthu zimene zingachititse munthu kumva bwino, kapena kumulimbikitsa kuti achite zinazake. (Aroma 12:8) M’chilankhulo choyambirira, mawuwa amatanthauza “kuitana munthu kuti adzaime pambali pako.” Zimenezi zikutithandiza kuona m’maganizo mwathu munthu akuthamanga kukathandiza mnzake yemwe akuvutika. Posatengera kuti wathandizidwa m’njira yotani, munthu amene watonthozedwa amalimbikitsidwa komanso amapeza mphamvu.

3. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Baranaba pa nkhani yotonthoza ena? (Onaninso chithunzi.)

3 Taganizirani chitsanzo cha m’Baibulo. Mkhristu wina dzina lake Yosefe ankadziwika kwambiri pa nkhani yolimbikitsa komanso kutonthoza ena moti atumwi anam’patsa dzina lakuti Baranaba, kutanthauza “Mwana Wotonthoza.” (Mac. 4:36) Dzinali linali lomuyenera moti m’Baibulo samatchulidwanso ndi dzina lake loyamba. Baranaba ankachita zinthu mogwirizana ndi dzina lake pothandiza Akhristu anzake amene ankafunika kuthandizidwa. Mwachitsanzo, Saulo amene anali atangokhala kumene Mkhristu atangofika ku Yerusalemu, ankafuna kukumana ndi Akhristu anzake koma iwo ankamuopa chifukwa chakuti poyamba ankawazunza. Komabe Baranaba ankamukhulupirira ndipo anapita naye kwa atumwi.—Mac. 9:​26-28.

Mokoma mtima, Baranaba wapita ndi Saulo kunyumba kwa atumwi ena. Atumwiwo akuyang’ana Saulo mokayikira pomwe Sauloyo akufika.

Baranaba ankachita zinthu zogwirizana ndi dzina lake (Onani ndime 3)


ZIMENE MUNGACHITE POTONTHOZA ENA

4. Kodi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zotonthozera ena ndi iti? (Aroma 1:​11, 12)

4 Muziwayendera ngati n’zotheka. Yehova amagwiritsa ntchito atumiki ake potonthoza ena. Mwachitsanzo, mneneri Eliya ali ndi nkhawa Yehova anagwiritsa ntchito mngelo kuti amulimbikitse. (1 Maf. 19:​4-7) Mtumwi Paulo anazindikiranso ubwino woyendera abale ake n’kuwalimbikitsa pamasom’pamaso. (Werengani Aroma 1:​11, 12.) Mukapita kukalimbikitsa munthu muzicheza naye kwa nthawi yokwanira. (1 Akor. 16:7) Dziwani kuti kumuimbira foni komanso kumulembera kalata, khadi kapena meseji kungamulimbikitsenso kwambiri. Ndiye kodi mungalole kuti Yehova akugwiritseni ntchito potonthoza ena?

5. Kodi tingakumane ndi mavuto ati?

5 Pamene zinthu zikuipiraipira m’masiku otsirizawa, tingayembekezere kuti tizivutika kwambiri kuti titonthoze abale ndi alongo athu pamasom’pamaso. Paulo ali m’ndende ku Roma, Onesiforo wa ku Efeso anamufufuza ngakhale kuti zimenezi zikanachititsa kuti nayenso amangidwe komanso kuphedwa kumene. (2 Tim. 1:​16-18) Abale ndi alongo athu ku Russia amachita zofanana ndi zimenezi Akhristu anzawo akamazunzidwa chifukwa cha zomwe amakhulupirira. A Mboni ena akamazengedwa mlandu, abale ndi alongo amapita kukhotiko kukawalimbikitsa, ngakhale kuti kuchita zimenezo kungachititse kuti nawonso amangidwe. Kuti inunso muzitha kulimbikitsa abale ndi alongo anu mwanjira imeneyi, mungachite bwino kuphunzira mmene atumiki a Yehova akale komanso a masiku ano analimbikitsira ena komanso zimene zinawathandiza kukhala osangalala ngakhale kuti ankazunzidwa.

6. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova tikamatonthoza ena? (Onaninso chithunzi.)

6 Muziwamvetsera. Mneneri Eliya ataona kuti moyo wake uli pangozi, anauza Yehova mmene ankamvera. Mulungu wathu wachikondi anamvetsera pamene Eliya ankafotokoza nkhawa zake ngakhale kuti ankadziwa kale zimene zinkamuvutitsa maganizo. Yehova anapitiriza kumumvetsera moleza mtima ngakhale kuti Eliya ankangonena zomwezomwezo. (1 Maf. 19:​9, 10, 14) Yehova analolanso kuti mneneri Habakuku afotokoze zomwe zinkamudetsa nkhawa m’njira imene ikanaoneka ngati sankalemekeza Mulungu. (Hab. 1:​2, 3) Masiku anonso Yehova amamvetsera chilichonse chimene tikumuuza m’mapemphero athu ngakhale kuti amadziwa kale zimene tikufunikira. Tingamutsanzire pomvetsera mwatcheru komanso mwaulemu abale ndi alongo athu akamalankhula. ‘Muzikhala okonzeka kumvetsera’ akamalankhula ndipo musamawadule mawu kapena kukwiya ngakhale pamene zikuoneka kuti sakulankhula bwino kapena akungonena zomwezomwezo.—Yak. 1:19; Mlal. 7:9.

Mlongo akumvetsera moleza mtima pamene mlongo wina yemwe ali ndi nkhawa wakhala akulankhula mpaka usiku.

Muzitsanzira Yehova pomvetsera mwatcheru abale ndi alongo anu akamalankhula (Onani ndime 6)


7. Kodi tingadziwe bwanji zimene mnzathu amene ali ndi nkhawa akufunikira?

7 Muzizindikira zimene akufunikira. Sitingathe kudziwa za mumtima mwa munthu ngati mmene Yehova amachitira koma tingadziwe zimene tingachite kuti timutonthoze tikamamumvetsera mwatcheru. Tisamaganize kuti tikudziwa zimene munthuyo akufunikira potengera zimene ifeyo tingafunikire ngati titakumana ndi vuto lofanana ndi lakelo. Anthufe ndife osiyana. Choncho musamachite zinthu mwaphuma. Muzimumvetsera mwatcheru ndiponso muzimufunsa mafunso mwaluso amene angakuthandizeni kudziwa mmene akumvera.—Miy. 20:5.

8. Kodi Yesu anachita zotani potonthoza Marita ndi Mariya, Lazaro atamwalira? (Onaninso zithunzi.)

8 Taganizirani zimene Yesu anachita potonthoza Marita ndi Mariya mchimwene wawo Lazaro atamwalira. Azimayi awiriwa anali ataferedwa koma Yesu anawatonthoza m’njira zosiyana. Marita atalankhula naye, Yesu anamufotokozera mfundo za choonadi zokhudza kuukitsidwa ndipo anamuthandiza kuti azizikhulupirira kwambiri. Koma zikuoneka kuti Mariya atabwera kwa iye akulira, Yesu sanamufotokozere chilichonse chokhudza kuukitsidwa, m’malomwake anangolira naye n’kumufunsa kumene Lazaro anaikidwa. (Yoh. 11:​20-35) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikamatonthoza anthu omwe akuvutika, tizizindikira zimene akufunikira m’malo mongoganiza kuti zomwe tachita potonthoza munthu wina zingathandizenso munthu wina.

Zithunzi: Mkulu wapita kunyumba za abale awiri amene akazi awo anamwalira. 1. Mkuluyo akugwira paphewa m’bale amene akulira. 2. Akuwerengera lemba m’bale wachikulire pomwe akuonera limodzi zithunzi.

Mukamatonthoza ena muziyesetsa kuzindikira zomwe akufunikira (Onani ndime 8)a


9. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Baibulo potonthoza ena? (Aroma 15:​4, 5)

9 Muzigwiritsa ntchito Baibulo. Mukagwiritsa ntchito ‘Malemba polimbikitsa’ munthu wina, mumamuthandiza kuti akhale ndi chiyembekezo. (Werengani Aroma 15:​4, 5.) Kenako chiyembekezocho chimamutonthoza komanso kumulimbikitsa. (Yes. 40:31) Koma kodi mungatani kuti mupeze malemba omwe angalimbikitse munthu wina? Ena amalemba mavesi amene angawagwiritse ntchito pamene akufunikira, mwachitsanzo omwe ali pamutu wakuti “Chitonthozo” m’buku la Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kugwiritsa ntchito bwino Mawu ake polimbikitsa ena. Mzimu wake ungakuthandizeni kuti mukumbukire malemba oyenerera omwe mungawagwiritse ntchito.—Yoh. 14:26.

10. N’chifukwa chiyani timafunika kulankhula mokoma mtima tikamalimbikitsa ena?

10 Muzilankhula mokoma mtima. Mawu a m’chilankhulo choyambirira akuti “kutonthoza” angamasuliridwenso kuti “kulimbikitsa.” Nthawi zina mungafunikenso kulimbikitsa munthu amene mukumutonthozayo kuti asinthe mmene akuonera zinthu. Ngati mukufunika kuchita zimenezi, muziganiza kaye musanalankhule n’cholinga choti mawu anu akhale olimbikitsa osati okhumudwitsa. (Miy. 12:18) Yehova anatipatsa chitsanzo chabwino pa nkhaniyi pomwe ankalankhula ndi Eliya, yemwe ankaganiza kuti ntchito yake ya uneneri sinaphule kanthu komanso ankaona kuti mtumiki wa Yehova watsala yekha mu Isiraeli monse. Yehova anathandiza Eliya mokoma mtima kuti ayambe kuona zinthu moyenera popanda kutchula zinthu zomwe ankaziona molakwikazo. (1 Maf. 19:​15-18) Inunso mukhoza kumachita zinthu mokoma mtima komanso kuganiza kaye musanalankhule. Mukamakamba nkhani kapena kupereka ndemanga pamisonkhano, nthawi zonse muzilankhula mokoma mtima komanso mwachikondi kuti mulimbikitse abale ndi alongo anu.

11. Kodi nthawi zambiri anthu amene akukumana ndi mavuto amafunikira chiyani? (1 Yohane 3:18)

11 Muzipeza njira zowathandizira. Anthu amene akukumana ndi mavuto amafunikira zambiri kuwonjezera pa kuwalimbikitsa ndi mawu. (Werengani 1 Yohane 3:18.) Baranaba anasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhaniyi pamene anagulitsa munda wake n’kupereka ndalamazo kuti zithandize abale ndi alongo omwe anali atangobatizidwa kumene. (Mac. 4:​36, 37) Akhristu ambirinso masiku ano amatengera chitsanzo chake pothandiza amene akufunikira kuwathandiza. Gabriela wa ku Poland anali ndi nkhawa madzi osefukira atawonongeratu nyumba yake. Iye anati: “Ine ndi makolo anga omwe ndinkakhala nawo tinali ndi mantha komanso tinkada nkhawa kwambiri. Ndinasoweratu mtengo wogwira koma abale a m’mipingo yapafupi anabwera n’kutikonzera nyumba yathu tsiku limodzi lokha. Zimenezi zinandithandiza kukhulupirira kwambiri kuti Yehova akutsogolera anthu ake kuti azitonthoza omwe akukumana ndi mavuto.”

12. Kodi mungathandize bwanji Akhristu anzanu mukakhalabe okhulupirika pamene mukukumana ndi mavuto?

12 Muzipirira mayesero. Paulo anauza Akhristu a ku Tesalonika kuti anatonthozedwa komanso kulimbikitsidwa atamva za kupirira kwawo. Iye anadziwa kuti zimene anachita powathandiza sizinapite pachabe. (1 Ates. 3:​5-8) Ndipo Paulo ankadziwa kuti kukhulupirika kwake pamene ankakumana ndi mavuto kukanalimbikitsa abale ndi alongo ake kuti nawonso akhale okhulupirika. (Akol. 2:​1, 2) Akhristu anzathu akaona mmene Yehova akutithandizira kupirira mavuto, amalimbikitsidwa kwambiri.

13. Kodi timafunika kuchita chiyani pa nkhani yolimbikitsa ena?

13 Muzikhala oleza mtima. Nthawi zina m’bale kapena mlongo amene wafooka sangalimbikitsidwe pa ulendo woyamba umene tamutonthoza. Mpake Malemba amatiuza kuti “pitirizani kutonthozana.” Mawuwa akusonyeza kuti tiyenera kuchita zimenezi mopitiriza. (1 Ates. 5:11) Muzikhala oleza mtima pamene mukupitiriza kulimbikitsa ndiponso kutonthoza anthu amene mukufunika kuwathandiza. (1 Ates. 5:14) Komabe tonsefe nthawi zina timafunika kutonthozedwa. Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani?

NGATI MUKUFUNIKA KUTONTHOZEDWA

14-15. Kodi tizitani tikakhumudwa kapena tikakhala ndi nkhawa?

14 Muzipemphera kwa Yehova. Muzimupempha kuti akulimbikitseni mukakhala ndi nkhawa. (Sal. 94:19) Muzimuuza mmene mukumvera ndipo muzimukhuthulira zonse za mumtima mwanu. (Sal. 62:8) N’zoona kuti Yehova amadziwa kale mmene mukumvera musanapemphere n’komwe. Koma mukamamuuza za mumtima mwanu mumasonyeza kuti mumamukhulupirira. Yehova amaonetsetsa kuti wayankha mapemphero a anthu amene amamukhulupirira m’njira imene iyeyo akuona kuti ndi yoyenera. (Maliko 11:24) Lemba la Afilipi 4:​6, 7 limatilimbikitsa kuti: “Muzipemphera kwa Mulungu. . . . Mukatero, mtendere wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”

15 Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Muzifotokozera mnzanu kapena mkulu wodalirika mmene mukumvera. Abale ndi alongo anu akhoza kukutonthozani koma sangadziwe mmene mukumvera kapena zimene mukufunikira, pokhapokha mutawafotokozera. (Miy. 14:10) Mungawapemphe kuti akumvetsereni, akuwerengereni lemba kapena akusonyezeni nkhani imene ingakutonthozeni.

16. Kodi n’chiyani chingachitike abale ndi alongo akamafuna kukulimbikitsani, nanga muyenera kukumbukira chiyani?

16 Muzikhala oleza mtima komanso muzikhululuka. Akhristu anzanu akhoza kulakwitsa zinthu akamayesetsa kukulimbikitsani. Mwachitsanzo, akhoza kulankhula kapena kuchita zinazake zomwe zingakukhumudwitseni kwambiri m’malo mokuthandizani kumvako bwino. Ngati zimenezi zitachitika, muziwalezera mtima. (1 Akor. 13:​4, 7) Muzikumbukira mawu a pa Yakobo 3:2 akuti: “Ngati munthu sapunthwa pa mawu, ndiye kuti ndi wangwiro.” Muziona kuti abale ndi alongo anuwo ali ndi zolinga zabwino. Musamaiwale kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”—Mat. 26:41.

17. Kodi tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuchita chiyani?

17 Tonsefe timafunika kutonthozedwa komanso kulimbikitsidwa, makamaka m’masiku otsirizawa pamene zinthu zikuipiraipira komanso adani a Mulungu akutitsutsa kwambiri. Choncho tiyeni titsimikize mtima kuchita zonse zomwe tingathe potonthoza ena.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi m’Baibulo mawu akuti “kutonthoza” amatanthauza chiyani?

  • Tingatani kuti tizitonthoza ena?

  • Kodi tizitani ngati tikufunikira kutonthozedwa?

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu akumvetsera mwachikondi pamene m’bale yemwe mkazi wake wangomwalira chakumene akulankhula. Patapita nthawi, mkuluyo wapita kwa m’bale yemwe mkazi wake anamwalira zaka zapitazo ndipo akukumbutsana zinthu zabwino zomwe mkazi wakeyo ankachita.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena