Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 April tsamba 8-13
  • Nthawi Zonse “Mulungu wa Choonadi” Amakwaniritsa Zimene Walonjeza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthawi Zonse “Mulungu wa Choonadi” Amakwaniritsa Zimene Walonjeza
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAKHULUPIRIRA MULUNGU WA CHOONADI?
  • ZIMENE YEHOVA WAKHALA AKUCHITA POKWANIRITSA CHOLINGA CHAKE
  • YEHOVA AKUSONKHANITSA ONSE AMENE AMAKONDA CHOONADI
  • TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA ADZAKWANIRITSA ZIMENE ANALONJEZA
  • Mupeze Mayankho a Mafunso Awa
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera Wokhala ndi Woimira Nthambi wa 2025-2026
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Mupeze Mayankho a Mafunso Awa
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera Wokhala ndi Woyang’anira Dera wa 2025-2026
  • Muzidalira Wolamulira wa Chilengedwe Chonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 April tsamba 8-13

JUNE 8-14, 2026

NYIMBO NA. 8 Yehova Ndi Pothawirapo Pathu

Nthawi Zonse “Mulungu wa Choonadi” Amakwaniritsa Zimene Walonjeza

“Mwandiwombola, inu Yehova Mulungu wa choonadi.”—SAL. 31:5.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona chifukwa chimene timakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzakwaniritsa zimene walonjeza komanso kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzathetsa mabodza ndi zachinyengo zonse.

1. Mogwirizana ndi Salimo 31:​2-5, n’chifukwa chiyani timakhulupirira Yehova?

TIKUKHALA m’dziko limene likulamuliridwa ndi Satana ndipo anthu ambiri ndi abodza, achinyengo komanso osakhulupirika. Zimenezi zimachititsa kuti zikhale zovuta kudziwa amene tingamukhulupirire. Anthu ambiri a bizinesi amachita zachinyengo. Pofuna kukopa anthu, otsatsa malonda amanena zabodza zokhudza katundu wawo. Ndipo anthu ena anasiya kukhulupirira anzawo apamtima chifukwa sachita zimene alonjeza. Koma n’zolimbikitsa kudziwa kuti tikhoza kumakhulupirira Yehova nthawi zonse. Iye ndi “Mulungu wa choonadi.” (Werengani Salimo 31:​2-5.) Yehova sanganame, nthawi zonse amanena zoona. Tingamudalire chifukwa amakwaniritsa zimene wanena.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munkhaniyi choyamba tikambirana zimene zimatichititsa kuti tizikhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Kenako tikambirana zimene Mulungu wa choonadi adzachite kuti awononge dziko loipa la Satanali komanso zimene akuchita panopa kuti akwaniritse cholinga chake. Kukambirana zimenezi kutithandiza kuti tiziuza ena zokhudza Yehova molimba mtima komanso mopanda mantha.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAKHULUPIRIRA MULUNGU WA CHOONADI?

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kwambiri Yehova?

3 Timakhulupirira Yehova chifukwa ndi Mlengi. Iye ndi amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi komanso ndi Kasupe wa moyo. (Gen. 1:1; Sal. 36:9; Chiv. 4:11) Iye analenga dzikoli m’njira yakuti zamoyo zizipitiriza kukhalapobe. Yehova ali ndi mphamvu zolamulira zinthu zonse za m’chilengedwechi. Choncho tizimukhulupirira ndi mtima wonse kuti azititsogolera pamoyo wathu komanso kuti akutikonzera tsogolo labwino.

4. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amatikonda?

4 Timakhulupirira Yehova chifukwa amatikonda. Yehova analenga anthu chifukwa ankafuna kuti tizisangalala ndi moyo ngati mmene iyeyo amachitira. Pofotokoza za cholinga chake, Yehova ananena kuti: “Tiyeni tipange munthu mʼchifaniziro chathu, kuti akhale wofanana nafe.” (Gen. 1:26) Iye anatipatsa ufulu wosankha zochita. Analenga dziko lokongolali kuti tizikhalamo. (Sal. 115:16) Anadalitsa makolo athu oyambirira powapatsa ntchito yosangalatsa yokonza dzikoli kukhala paradaiso. (Gen. 1:28; 2:15) Anaika zinthu zosiyanasiyana zabwino padzikoli kuti iwo azisangalala nazo. Zimene anachitazi zikusonyeza kuti “Yehova adzapitiriza kusonyeza chikondi chake chokhulupirika mpaka kalekale.”—Sal. 103:17.

5. (a) Kodi Yehova anachita chiyani Mdyerekezi atachititsa kuti Adamu ndi Hava asamvere? (b) Kodi ndi malonjezo ena ati amene Mulungu anakwaniritsa? (Onani bokosi lakuti “Mulungu Wakhala Akunena Zoona Kuyambira Kalekale.”)

5 Timakhulupirira Yehova chifukwa nthawi zonse amakwaniritsa zimene walonjeza. Yehova sanalenge dzikoli “popanda cholinga, koma analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yes. 45:​18, 19) Adamu ndi Hava atasankha kusamvera Yehova, anapatsidwa chilango cha imfa. Choncho zinkaoneka ngati cholinga cha Yehova chalephereka. Koma Yehova amakwaniritsa zonse zimene walonjeza. (Yes. 46:​10, 11) Cholinga chake choti padzikoli pakhale anthu olungama sichinasinthe. N’chifukwa chake Yehova analola kuti Adamu ndi Hava abereke ana. Ndipo anapereka Mwana wake wobadwa yekha monga dipo kuti apulumutse ana a Adamu komanso kuwapatsa chiyembekezo chosangalatsa chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale.—Yoh. 3:16.

Mulungu Wakhala Akunena Zoona Kuyambira Kalekale

Taonani malonjezo ena amene Yehova anakwaniritsa:

  • Analonjeza Mose kuti Aisiraeli adzakhala m’dziko lawolawo loyenda mkaka ndi uchi.—Eks. 3:​6-8; Deut. 27:3.

  • Analonjeza kuti kudzabwera Mesiya amene adzapulumutse anthu ku uchimo ndi imfa.—Yes. 53:​11, 12.

  • Analonjeza kuti padzakhala ntchito yolalikira padziko lonse imene idzathandize kuti anthu amudziwe mapeto asanafike.—Mat. 24:14.

Kodi mukudziwa malonjezo enanso ati amene Yehova anakwaniritsa?

ZIMENE YEHOVA WAKHALA AKUCHITA POKWANIRITSA CHOLINGA CHAKE

6. Kodi Yehova ananena chiyani Adamu ndi Hava atachimwa?

6 “Njoka yakale ija, imene imadziwika kuti Mdyerekezi komanso Satana,”a ndi imene inapusitsa Adamu ndi Hava kuti asamvere Mulungu. (Chiv. 12:9; Gen. 3:​4, 5; Yoh. 8:44) Chifukwa cha zimenezi, Yehova ananeneratu kuti m’tsogolo Satana adzawonongedwa. (Gen. 3:15) Yehova anasonyeza kuti zimenezi zisanachitike, anthu ambiri adzatsatira Satana n’kumachita zoipa. Komabe anthu ena adzakhala okhulupirika kwa Yehova.

7. Ndi ndani amene ali kumbali ya Mdyerekezi, nanga zinthu zidzawathera bwanji?

7 Angelo oipa komanso anthu osamvera akutsatira Satana Mdyerekezi. Popeza amatsutsa komanso kulimbana ndi cholinga cha Mulungu, iwo amakhala kumbali ya Satana. Koma Satana ndi onse amene ali kumbali yake adzawonongedwa pa nthawi imene Yehova anakhazikitsa.—Dan. 2:44; Aroma 16:20.

8. Kodi Yesu anachita chiyani mu 1914? (Onaninso zithunzi.)

8 N’chiyani chimatitsimikizira kuti Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake chowononga Satana ndi onse amene amamutsatira? Mu 1914, Yesu anayambitsa nkhondo yolimbana ndi Satana Mdyerekezi komanso ziwanda zake ndipo anawaponyera padziko lapansi. (Chiv. 12:​7-9) Ngakhale kuti nkhondoyi inachitika kumwamba, zotsatira zake zinakhudzanso anthu padziko lapansi. Baibulo limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu ndipo ali ndi mkwiyo waukulu chifukwa akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chiv. 12:12) Kuyambira mu 1914, Satana wakhala akusocheretsa anthu ndipo zotsatira zake padzikoli zinthu zakhala zikuipiraipirabe. Zoonadi, “tsoka dziko lapansi.” Posachedwapa Yesu ‘adzapambana pankhondo’ ndipo Satana ndi onse amene amamutsatira adzawonongedwa. (Chiv. 6:2) Yesu adzayeretsa dzina la Yehova ndipo silidzadetsedwanso mpaka kalekale. (Sal. 45:​4-6) Aliyense adzadziwa kuti Yehova ndi Mulungu wa choonadi.—Ezek. 38:23.

Zithunzi: Zinthu zomwe zakhala zikuchitika padzikoli kuyambira mu 1914. 1. Satana monga chinjoka cha mitu 7 waponyedwa padziko lapansi. 2. Asilikali anyamula mfuti ndipo akubisalira adani m’ngalande pankhondo. 3. Mtambo ukuoneka ngati bowa pambuyo pa kuphulitsidwa kwa bomba. 4. Mayi wosowa kokhala ali m’mbali mwa msewu ndipo wanyamula mwana wake yemwe akulira. 5. Msilikali akukonzekera kuwombera. 6. Munthu akuyenda m’tauni imene yawonongedwa. 7. Mafakitale akutulutsa mpweya wowononga chilengedwe. 8. Anthu avala masiki ndipo akuyenda mumzinda. 9. Anthu ochita zionetsero akumenyana ndi apolisi.

World War I: U.S. National Archives photo; bomb: USAF photo; pandemic: blvdone/stock.adobe.com; riot: inhauscreative/E+ via Getty Images

Kuyambira mu 1914 zinthu zakhala zikuipiraipira padzikoli (Onani ndime 8)


YEHOVA AKUSONKHANITSA ONSE AMENE AMAKONDA CHOONADI

9. Kodi Yehova akusonkhanitsa ndani masiku ano?

9 Panopa Yehova akusonkhanitsa “zinthu zonse pamodzi kuti zikhale zogwirizana ndi Khristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi.” (Aef. 1:10) “Zinthu zakumwamba” ndi odzozedwa amene Yehova anawasankha kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba. “Zinthu zapadziko lapansi” ndi anthu amene adzakhale ndi moyo mpaka kalekale m’Paradaiso padzikoli. Magulu awiriwa onsewa akugwira mwakhama ntchito yothandiza anthu kuti adziwe Yehova komanso kuwasonyeza kuti Satana ndi wabodza.

10. Kodi Yehova akuthandiza bwanji anthu kuti adziwe choonadi? (Chivumbulutso 14:​6, 7)

10 Yehova akusonkhanitsa anthu okonda choonadi kudzera mu ntchito yaikulu yolalikira, imene ikuchitika padziko lonse kuposa kale. (Werengani Chivumbulutso 14:​6, 7.) Ngakhale kuti Yehova akugwiritsa ntchito anthu kuti aziuza ena uthenga wabwino, angelo nawonso amathandiza kusonkhanitsa anthu amtima wabwino kuti ayambe choonadi. Ntchito yolalikira imathandiza anthu kuzindikira mabodza a Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zabodza, zimene Satana wakhala akuzigwiritsa ntchito kwa zaka zambiri pofalitsa mabodza okhudza Yehova. (Chiv. 18:​2, 4) Posachedwapa zipembedzozi ziwonongedwa ndipo onse amene amakonda Mulungu wa choonadi azidzamupatsa ulemerero umene amafunikira.—Chiv. 17:16.

11. Kodi tingawadziwe bwanji olambira oona?

11 Yehova akukoka anthu osiyanasiyana padziko lonse kuti abwere m’gulu lake. (Chiv. 7:​9, 10) Iwo akamva “uthenga wabwino” amazindikira kuti apeza choonadi ndipo amafunitsitsa kulowa m’gulu lake. (Maliko 13:10) Panopa tikuwadziwa bwino amene akulambira Mulungu movomerezeka komanso amene sakumulambira movomerezeka. Mneneri Malaki analosera kuti: “Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.” (Mal. 3:18) A Mboni za Yehova amasonyeza kuti amalambira Mulungu wa choonadi chifukwa cha makhalidwe awo abwino komanso ntchito yolalikira imene amagwira.

12. Kodi ntchito yolalikira imathandiza bwanji kukwaniritsa chifuniro cha Yehova?

12 Tikamalalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ timakhala tikumvera lamulo la Yesu komanso kukwaniritsa ulosi. (Mat. 24:14; 28:​18-20) Zotsatira zake n’zakuti anthu padziko lonse akukhala ophunzira a Yesu ndipo akuyembekezera kudzalambira Mulungu wa choonadi mpaka kalekale. Ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito imene ikukwaniritsa cholinga cha Yehova.

TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA ADZAKWANIRITSA ZIMENE ANALONJEZA

13. Kodi Satana amalimbana kwambiri ndi ndani, nanga n’chifukwa chiyani?

13 Satana Mdyerekezi ndi wokwiya kwambiri chifukwa akudziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa” kuti awonongedwe. (Chiv. 12:​12, 13) Iye amalimbana kwambiri ndi odzozedwa ‘amene amasunga malamulo a Mulungu ndipo ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.’ (Chiv. 12:17; 14:12) Iye akulimbananso ndi aliyense amene amathandiza odzozedwa komanso kugwira ntchito imene iwo amagwira.

14. Kodi n’chiyani chidzachitike Satana akadzaukira anthu a Yehova? (Onaninso chapachikuto.)

14 Babulo Wamkulu akadzawonongedwa anthu amene ali kumbali ya Satana adzafuna kuwononga anthu a Yehova. Zimenezi zidzayambitsa nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:​13, 14, 16) Yesu ndi magulu ankhondo akumwamba adzapulumutsa anthu a Yehova ndipo adzawononga onse omwe ali kumbali ya Mdyerekezi. (Chiv. 19:​19-21) Padzikoli sipadzapezekanso anthu abodza, oipa komanso achinyengo. (Chiv. 21:8) Dzina la Mulungu wa choonadi komanso wachilungamo lidzayeretsedwa.

Yesu ndi gulu lake lankhondo lakumwamba akwera mahatchi oyera ndipo akumenyana ndi asilikali padzikoli. Yesu akukoka uta wake pomwe angelo akweza malupanga awo.

Yesu ndi magulu ake ankhondo akumwamba akukamenya nkhondo ya Aramagedo kuti awononge adani ake (Onani ndime 14)


15. N’chiyani chimatitsimikizira kuti zimene Yehova walonjeza zidzachitikadi? (Yesaya 65:​16, 17) (Onaninso chithunzi.)

15 Panopa dzikoli ndi logawanika kwambiri kuposa kale. Koma Yehova akuthandiza atumiki ake kuti akhale ogwirizana. Ntchito yosonkhanitsa anthu ili mkati. Palibe chingalepheretse Yehova kudalitsa anthu ake komanso ntchito imene akugwira. (Werengani Yesaya 65:​16, 17.) Sitikayikira kuti Yehova adzakwaniritsa zonse zimene walonjeza. Mawu a mtumwi Paulo opezeka pa Aroma 8:​38, 39 amatitsimikizira kuti: “Imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu, msinkhu, kuzama kapena cholengedwa chilichonse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”

Makolo ndi ana awo akhala pakhonde la nyumba yawo yomwe kutsogolo kwake ndi kokongola kwambiri. Chipembere chikudya chapafupi.

M’dziko latsopano sitidzakumbukiranso mavuto amene tikukumana nawo panopa (Onani ndime 15)


16. N’chifukwa chiyani mumakhulupirira Yehova ndi mtima wonse?

16 Tili ndi zifukwa zonse zotichititsa kuti tizikhulupirira Yehova Mulungu wa choonadi. Iye ndi Mlengi wathu. Amatikonda kwambiri. Khamu lalikulu likuwonjezereka mofulumira pamene anthu amitundu yonse akuyamba kulambira Yehova. (Yes. 60:22; Zek. 8:23) Timadziwa kuti iye amakwaniritsa zimene walonjeza ndipo posachedwapa athetsa mabodza a Satana. Mofanana ndi Davide, ifenso timapemphera kuti: “Atamandike Yehova Mulungu, . . . iye yekha amene amachita zinthu zodabwitsa. Litamandike dzina lake laulemerero mpaka kalekale, ndipo ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.”—Sal. 72:​18, 19.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’chifukwa chiyani timakhulupirira “Mulungu wa choonadi”?

  • Kodi Yehova adzachita chiyani kuti awononge dziko la Satanali, nanga panopa akuchita chiyani kuti akwaniritse cholinga chake?

  • N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yehova adzakwaniritsa cholinga chake?

NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndi Yehova

a Baibulo silitiuza dzina lenileni la mngelo woipayu. Iye amangodziwika ndi mayina monga “Mdyerekezi” [Woneneza] komanso “Satana” [Wotsutsa].

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena