Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 March tsamba 8-13
  • Muzidalira Wolamulira wa Chilengedwe Chonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzidalira Wolamulira wa Chilengedwe Chonse
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • SATANA ANAFIKA PAKATI PAWO
  • YEHOVA ANAIKA MALIRE
  • YEHOVA ANATHETSA MAVUTO A YOBU
  • YEHOVA AMAKONDA ATUMIKI AKE OKHULUPIRIKA
  • MUZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI YEHOVA
  • Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Yobu Analemekeza Dzina la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Yembekezera Yehova”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mukulowetsedwa m’Nkhani Yofunika
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 March tsamba 8-13

MAY 11-17, 2026

NYIMBO NA. 7 Yehova Ndi Mphamvu Yathu

Muzidalira Wolamulira wa Chilengedwe Chonse

“Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.”—SAL. 83:18.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona chifukwa chake tingakhulupirire kwambiri kuti Yehova adzatithandiza tikamakumana ndi mavuto panopa komanso m’tsogolo.

1. Kodi Yobu anakumana ndi mavuto ati?

YOBU anataya zinthu zambiri m’kanthawi kochepa. Ana ake onse anafa, chuma chake chinatha komanso anadwala kwambiri. Kuwonjezera pamenepa mbiri yakenso inaipa. Anthu atatu amene ankati ndi anzake anamunenera zinthu zambiri zoipa. Ngakhalenso mkazi wake anakhumudwa kwambiri moti anamuuza kuti ‘atukwane Mulungu kuti afe.’ (Yobu 2:9; 15:​4, 5; 19:​1-3) Mavuto onsewa akanamuchititsa kuti asiye kudalira kwambiri Mulungu woona kapenanso kumakayikira kuti Yehova amateteza anthu amene amamukonda komanso kumutumikira.

2-3. Kodi tingayambe kukayikira za chiyani, nanga tingaphunzire chiyani pa nkhani ya Yobu?

2 Ifenso nthawi zina timakumana ndi mavuto amene angachititse kuti zikhale zovuta kuti tizidalira Yehova. Tikukhala ‘m’nthawi yapadera komanso yovuta.’ (2 Tim. 3:1) Tikamakumana ndi mavuto otsatizanatsatizana tikhoza kumaona kuti tapanikizika ndipo sitingathe kupirira. Zimenezi zachititsa kuti ena ayambe kukayikira ngati Yehova amawakondadi.

3 Ngati inunso nthawi ina munamvapo choncho, musataye mtima. Yobu anaphunzira mfundo yakuti Yehova amapulumutsa anthu okhulupirika. Mofanana ndi Yobu, ifenso tikhoza kumadalira kwambiri Atate wathu wakumwamba. Kuti tikwanitse zimenezi, tiyeni tikambirane nkhani ya Yobu ndipo tiona kuti imatitsimikizira mfundo ziwiri zofunika izi: Yoyamba, Yehova yekha ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Yachiwiri, Mulungu wathu wamphamvuyonse ali ndi mphamvu zosankha kuti zinthu zinazake m’dzikoli zichitike mogwirizana ndi cholinga chake, komanso kuonetsetsa kuti atumiki ake ndi otetezeka ndipo ali pa ubwenzi wabwino ndi iye.

SATANA ANAFIKA PAKATI PAWO

4. Kodi ndi ndani amene anapezeka nawo pamsonkhano umene unachitika kumwamba wotchulidwa m’buku la Yobu?

4 Tsiku lina “ana a Mulungu woona” anasonkhana pamaso pa Yehova kumwamba. Nkhaniyi imapitiriza kuti: “Satana nayenso anafika pakati pawo.” (Yobu 1:6) Amenewa ndi malo oyamba m’Baibulo amene mdani wamkulu wa Yehovayu anatchulidwa ndi dzina lomufotokoza lakuti “Satana,” kapena kuti “Wotsutsa.” Pofika pa nthawiyi, Satana anali atasiya kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Iye anakhala mdani wa Yehova, angelo okhulupirika komanso wa anthu okhulupirika padzikoli. Pa Genesis 3:​15, Yehova anasonyeza kuti Satana sanalinso m’banja la Mulungu lakumwamba. Choncho Satana sali mbali ya “mkazi” yemwe akuimira banja la Yehova la angelo okhulupirika. ‘Mkaziyu’ anali woti adzabereka “mbadwa” yotchulidwa palembali.

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinalankhulidwa pamsonkhano womwe unachitika kumwamba?

5 Yehova anasankha kuti zomwe zinalankhulidwa pamsonkhano wakumwambawo zilembedwe m’Baibulo. Zimene Satana analankhula zimangosonyezeratu kuti iye ndi woipa kwambiri komanso wabodza. (Yobu 1:9; yerekezerani ndi Chivumbulutso 12:10.) Zimene zinachitika pamsonkhanowu zimatitsimikizira kuti Yehova akamagwiritsa ntchito mphamvu zake zolamulira, zomwe ndi zopanda malire, amachita zimenezi moyenera komanso mwachilungamo. Zimasonyezanso kuti Mulungu Wamphamvuyonse amaika malire pa zimene ena angachite.

YEHOVA ANAIKA MALIRE

6. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi amene ankatsogolera pamsonkhano womwe unachitika kumwamba? (Yobu 1:​7, 8)

6 Werengani Yobu 1:​7, 8. Yehova ndi amene ankasankha zoyenera kuchitika pamsonkhanowo. Iye anafunsa Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu?” Yehova ankadziwa kuti Satana akufuna kulimbana ndi Yobu. Tsopano tiyeni tikambirane mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake zopanda malire pothandiza Yobu.

7. Mogwirizana ndi Yobu 1:​10, 11, kodi Satana anasonyeza kuti anthu amatumikira Yehova chifukwa chiyani?

7 Werengani Yobu 1:​10, 11. Yehova ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse ndipo amagwiritsa ntchito mphamvu zake mmene akufunira komanso m’njira yabwino kwambiri. (Yer. 32:17; Dan. 4:35) Ngakhale zili choncho, Satana ananena kuti Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika. Zili ngati iye ankanena kuti Mulungu amapatsa Yobu ziphuphu kuti azimutumikira. Anasonyezanso kuti anthu amatumikira Yehova chifukwa cha zimene Yehovayo amawapatsa. Ndiye kodi Yehova anatani?

8-9. Kodi ndi malire ati amene Yehova anamuikira Satana, nanga n’chifukwa chiyani? (Yobu 1:12) (Onaninso chithunzi.)

8 Werengani Yobu 1:12. Yehova anamulola Satana kuti asonyeze ngati zimene ananenazo zinali zoona koma anamuikira malire. Ponena za Yobu, Mulungu anamuuza momveka bwino kuti: “Dzanja lako lisakhudze munthuyo.” Yehova anaikira malire Satana angelo onse akuona. Iye sakanachitira mwina koma kutsatira zimene Yehova anamuuzazi ndipo ndi mmene zililinso masiku ano. Yehova anagwiritsa ntchito udindo komanso mphamvu zake poteteza Yobu komanso posonyeza kuti ndi Mulungu wachikondi.

9 Satana analephera mochititsa manyazi kugonjetsa Yobu pa ulendo woyamba. Yobu anapitiriza kukhala wokhulupirika kwa Atate wake wakumwamba. (Yobu 1:22) Komabe Wotsutsayo anali asanamalize kumuyesa.

Satana ali kumwamba, akulankhula ndi Yehova mopanda ulemu angelo akuona.

Yehova analola kuti Satana asonyeze pamaso pa angelo onse ngati zimene ananena zinalidi zoona (Onani ndime 8 ndi 9)


10. N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti Satana apitirize kuyesa Yobu? (Yobu 2:​2-6)

10 Werengani Yobu 2:​2-6. Kenako Satana ankafuna kuchita zinthu zina zankhanza kwambiri kuti Yobu asiye kutumikira Yehova. Iye ananena kuti Yobu akhoza kutukwana Mulungu kuti apulumutse moyo wake. Pofuna kuthetsa nkhaniyi, Yehova analola kuti Mdyerekezi adwalitse munthu wokhulupirikayu. Koma anamuikiranso malire n’kumuuza kuti: “Usachotse moyo wake.” Ulendo umenewunso Satana sakanachitira mwina koma kutsatira zimene anauzidwa. Apanso tikuona kuti Wam’mwambamwamba ndi amene ankasankha zochita ndipo Satana sakanachita zinthu zodutsa malire amene anamuikira.

YEHOVA ANATHETSA MAVUTO A YOBU

11. Yehova atathetsa mayesero a Yobu, kodi anamudalitsa bwanji? (Yobu 42:​10-13)

11 Werengani Yobu 42:​10-13. Zinali zoonekeratu kuti Yobu sangagonje ndipo Yehova sanalole kuti Satana apitirize kumuyesa. Yehova anathetsa mavuto a mtumiki wake wokhulupirikayu. Pa nthawiyinso, Satana analibe mphamvu zolepheretsa Yehova kuteteza Yobu komanso kumudalitsa.

12. Perekani chitsanzo cha zomwe zimachitikira anthu amene amakhulupirira kuti Yehova akhoza kuwapulumutsa.

12 M’masiku otsiriza ano, anthu ambiri akhala akuona Yehova akuwapulumutsa. Mwachitsanzo, mu 1945 asilikali a Nazi anakakamiza a Mboni okwana 230 kuyenda ulendo wautali kuchokera ku Germany kupita ku nyanja yaikulu kuti akawaphe. Koma a Mboni onsewo anapulumuka. Pambuyo pokumana ndi zinthu zochititsa manthazi, iwo analemba kuti: “Takumana ndi mayesero oopsa kwa nthawi yaitali ndipo ngakhale kuti zimangokhala ngati tapulumutsidwa mung’anjo yoyaka moto, sitimveka fungo lamoto ngakhale pang’ono. . . . M’malomwake, Yehova amatipatsa mphamvu zambiri.” Iwo anawonjezeranso kuti: “Tikungofuna chinthu chimodzi basi . . . kuti [pambuyo] pokhala m’dzenje la mikango chonchi, Yehova atilole kumutumikira . . . mpaka kalekale. Imeneyi payokha ndi mphoto yaikulu kwambiri yomwe tingalandire.”—Yerekezerani ndi Danieli 3:27; 6:22.

13. Kodi tisamakayikire chiyani tikakumana ndi mayesero? (Onaninso zithunzi.)

13 Ifenso tikhoza kukumana ndi zinthu zina zomwe zingatichititse kumva ngati tili m’dzenje la mikango. (1 Pet. 5:​8-10) Nthawi zina tingamaone ngati tagonjetsedwa n’kumakayikira ngati mavuto athu adzathe. Pa nthawi ngati imeneyi, kukumbukira chitsanzo cha Yobu kungatithandize. Tisamakayikire kuti Yehova adzathetsa mavuto athu, kaya panopa kapena m’dziko latsopano. Iye sadzalola kuti nthawi imene anaika kuti awononge dzikoli idutse ngakhale ndi tsiku limodzi.

Zithunzi: Atumiki a Yehova akuvutika m’njira zosiyanasiyana. 1. M’bale wachinyamata akutonthoza m’bale wachikulire pamene onse akulira kumanda. 2. Makolo akuoneka ankhawa, ali pambali pa mwana wawo wamkazi yemwe wagona pabedi kuchipatala. 3. M’bale yemwe ndi mkaidi akukumba dothi ndi fosholo kunja kukutentha kwambiri, kwinaku msilikali akumulondera.

Yehova adzathetsa mavuto amene atumiki ake okhulupirika akukumana nawo (Onani ndime 13)


YEHOVA AMAKONDA ATUMIKI AKE OKHULUPIRIKA

14-15. Kodi Yehova amafuna kudzawachitira chiyani atumiki ake okhulupirika, nanga n’chifukwa chiyani? (Yobu 14:15) (Onaninso chithunzi.)

14 Werengani Yobu 14:15. Atate wathu wakumwamba amakonda kwambiri anthu okhulupirika. Iye amawaona kuti ndi amtengo wapatali moti ngati angafe, adzawaukitsa. Ndipo adzathetsa ululu umene imfa imabweretsa.—Yes. 65:17.

15 Ngakhale kuti Yobu anapitiriza kukhala m’dziko lolamulidwa ndi Satana, Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova anamuchiritsa ndiponso anamudalitsa ndi zinthu zambiri kuposa zomwe anali nazo poyamba. Koma Yehova adzamupatsanso zinthu zoposa pamenepa m’tsogolomu. Yehova anasonyeza kuti amafuna kuti atumiki ake onse okhulupirika azikhala osangalala kwambiri. Ndipo iye adzawapatsa mwayi wokhala ndi moyo wangwiro m’paradaiso padzikoli. (Chiv. 21:​3, 4) Monga Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse, Yehova amafunitsitsa kuchita zimenezi. Kudziwa zimenezi kumatilimbikitsa kwambiri tikamakumana ndi mavuto.

Yobu akuoneka wa thanzi komanso watchena, akusangalala pamene anzake ambiri akubwera kudzaona iyeyo ndi mkazi wake kunyumba kwawo.

Yehova anadalitsa kwambiri Yobu ndi mkazi wake pambuyo pa mayesero ake (Onani ndime 14 ndi 15)


16. Kodi n’chiyaninso chimatichititsa kuti tizikhulupirira Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu?

16 Yobu anamwalira atakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali. Koma Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu komanso Wamphamvuyonse, ali ndi mphamvu zodzamuukitsa. (Deut. 32:39) Iye anasankha nthawi yodzaukitsa anthu amene amawakonda ndipo palibe amene angamulepheretse kuchita zimenezi.—Aroma 8:​38, 39.

MUZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI YEHOVA

17. Kodi timadziwa bwanji kuti Satana sangawononge anthu a Yehova?

17 Nkhani ya Yobu imatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova. Timathokoza kwambiri Yehova chifukwa sanalole kuti Satana awononge anthu ake okhulupirika. Masiku ano pali atumiki okhulupirika a Yehova pafupifupi 9 miliyoni ndipo umenewu ndi umboni wakuti Wolamulira Wamkulu ali ndi mphamvu zambiri. Nthawi ndi nthawi takhala tikuona kuti zida zopangidwa pofuna kulimbana ndi atumiki a Yehova sizipambana. (Yes. 54:17) Mayiko komanso zipembedzo zikuluzikulu sizinakwanitse kugonjetsa atumiki a Yehova, omwe amaoneka ngati osatetezeka. Ndipo palibe chomwe chingatilepheretse kuuza ena mfundo zoona zokhudza Yehova komanso kuwathandiza kudziwa kuti Satana ndi wabodza ndiponso wakupha. Ngakhalenso imfa siingatilepheretse kuchita zimenezi chifukwa Yehova adzaukitsa aliyense wokhulupirika.—Hos. 13:14.

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa zimene zidzachitike m’tsogolo?

18 Kuganizira zimene zinachitikira Yobu kumatithandiza kuti tisamachite mantha n’kumakhulupirira kuti Yehova adzakhala nafe kaya tidzakumana ndi zotani m’tsogolomu. Pachisautso chachikulu, Satana ndi magulu ake azidzaona ngati anthu a Yehova ndi osatetezeka ndipo adzawaukira. Koma mofanana ndi zimene zinachitika m’nthawi ya Yobu, Yehova ndi amene azidzayendetsa zinthu ndipo sadzalola kuti Satana awonongeretu anthu ake. Posachedwapa Yehova athetsa mavuto onse amene Satana anayambitsa. Mdyerekezi ndi ziwanda zake adzaponyedwa kuphompho kwa zaka 1,000. (Luka 8:31; Chiv. 20:​1-3) Pamapeto pake, Satana komanso onse amene adzakhale kumbali yake adzawonongedwa. (Chiv. 20:10) Monga mmene Yehova ananenera, mutu wa Satana udzaphwanyidwa, kutanthauza kuti adzawonongedwa mpaka kalekale.—Gen. 3:15; Aroma 16:20.

19. Kodi anthu amene amakhulupirira Yehova ndi mtima wonse adzapeza madalitso ati? (Onaninso chithunzi.)

19 Tikuyembekezera mwachidwi dziko latsopano chifukwa pa nthawiyo tidzakhala angwiro komanso tizidzasangalala kwambiri. Moyo udzakhala wabwino kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Yehova akulonjeza kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.” (Chiv. 21:5) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kwa nthawi yoyamba pambuyo pa zaka masauzande, anthu sazidzasokonezedwanso ndi Satana komanso ziwanda zake. Pa nthawiyi tizidzamva ngati tatula chimtolo cholemetsa. Tizidzagonanso tulo tokoma chifukwa zinthu zonse zodetsa nkhawa zam’dzikoli zidzakhala zitatha. Padziko lonse, anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo adzaona anthu ambiri akuchiritsidwa modabwitsa komanso achibale ndi anzawo akuukitsidwa. Pa nthawiyo tizidzakhala mosangalala ngati mmene Atate wathu ankafunira poyamba.

Abale ndi alongo a m’chithunzi cham’mbuyo chija akusangalala m’dziko latsopano. M’bale wachikulire yemwe tsopano ndi wachinyamata, akuyenda ndi mkazi wake. Makolo akuyenda limodzi ndi mwana wawo wamkazi, yemwe tsopano ali ndi thanzi labwino. M’bale amene nthawi ina anali mkaidi uja, wakhala pansi pa mtengo, akuwerenga Baibulo, pambali pake pali mwana wa mkango.

Yehova adzadalitsa kwambiri anthu okhulupirika amene anapirira mayesero (Onani ndime 19)


20. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

20 M’masiku otsiriza ano tizikumanabe ndi mavuto ndipo tikufunika kukhala olimba mtima kuti tikhalebe okhulupirika. Choncho tiyenera kumakhulupirira kwambiri Yehova komanso kumumvera monga wolamulira wathu. Tiyeni tizisonyeza kuti timakonda Atate wathu wakumwamba komanso kuti Satana ndi wabodza. Tisamakayikire kuti tikakhala okhulupirika kwa Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu, tsogolo lathu ndi lowala. Tikutero chifukwa Yehova ndi wofunitsitsa kudzapereka mphoto kwa atumiki ake okhulupirika ndipo adzawachitiradi zimenezi.

KODI NKHANI YA YOBU IMASONYEZA BWANJI KUTI . . .

  • Yehova ndi Wolamulira Wam’mwambamwamba m’chilengedwe chonse?

  • Yehova amafunitsitsa kudalitsa atumiki ake okhulupirika?

  • mukhoza kumakhulupirira kwambiri Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse?

NYIMBO NA. 153 Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena