Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 March tsamba 14-19
  • Zimene Mungachite Kuti Mulimbane ndi Zosokoneza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Mulimbane ndi Zosokoneza
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI NDI ZINTHU ZITI ZOMWE ZINGATISOKONEZE?
  • KODI YESU ANKATANI POLIMBANA NDI ZINTHU ZIMENE ZIKANAMUSOKONEZA?
  • KODI TINGATANI KUTI TILIMBANE NDI ZINTHU ZOSOKONEZA?
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Mupeze Mayankho a Mafunso Awa
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera Wokhala ndi Woyang’anira Dera wa 2025-2026
  • Mupeze Mayankho a Mafunso Awa
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera Wokhala ndi Woimira Nthambi wa 2025-2026
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 March tsamba 14-19

MAY 18-24, 2026

NYIMBO NA. 35 “Muzitha Kusankha Zinthu Zimene Ndi Zofunikadi Kwambiri”

Zimene Mungachite Kuti Mulimbane ndi Zosokoneza

“Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.”—AEF. 5:17.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene tingachite kuti tisasiye kuchita zinthu zokhudza kulambira ngakhale titakumana ndi zosokoneza.

1-2. Kodi zingatheke bwanji kuti zinthu zofunika zikhale zosokoneza?

KODI ndi nthawi iti imene munakumana ndi zinthu zosokoneza? Mwina zinakuchititsani kusiya zinthu zimene munkachita pa nthawiyo ndipo munkafunika kusankha chinthu chomwe ndi chofunika kwambiri. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti foni yanu yayamba kuitana mukuyendetsa galimoto. N’kutheka kuti foniyo ndi yofunika, komabe pa nthawiyi ikhoza kukusokonezani. Apa chofunika kwambiri ndi kuika maganizo anu onse pa kuyendetsa galimotoyo.

2 Tonsefe tili ndi zinthu zofunika zimene timayenera kuchita. Komabe timadziwa kuti chofunika kwambiri ndi kuchita zinthu zauzimu.a (Mat. 6:33) Mofanana ndi madalaivala amene amachita zinthu mosamala, anthu a Yehova amayesetsa kuzindikira zinthu zimene zingawasokoneze.—Miy. 4:25; Mat. 6:22.

3. Kodi nkhaniyi itithandiza bwanji?

3 Sitimachita kufuna kuti tisokonezedwe pa zinthu zokhudza kulambira. Komabe, tonsefe timakumana ndi zinthu zomwe zingatisokoneze mosavuta. (Luka 21:​34-36) Choncho kuti tiziika kutumikira Yehova pamalo oyamba, tiyeni tikambirane (1) zinthu zimene zingatisokoneze, (2) zimene Yesu anachita polimbana ndi zinthu zimene zikanamusokoneza komanso (3) zomwe tingachite polimbana ndi zosokoneza.

KODI NDI ZINTHU ZITI ZOMWE ZINGATISOKONEZE?

4-6. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatisokoneze mosavuta?

4 Pali zinthu zambiri zimene anthufe timafunika kuchita. Mwachitsanzo, tingakhale kuti tikulimbana ndi matenda enaake, tikufunika kusamalira banja lathu kapena kuchita zinthu zokhudza ifeyo. N’zoona kuti zinthu zimenezi ndi zofunika ndipo zimafuna nthawi yathu. Koma kodi zikhozanso kutisokoneza? Inde, ngati timangokhalira kuziganizira komanso zimatidyera nthawi yathu yonse.

5 Kuwonjezera pamenepa, ambiri a ife tikukhala m’madera amene anthu akulimbana pa ndale ndipo muli mavuto a zachuma ndi miliri. (2 Tim. 3:1) Zinthu zimenezi zingachititse kuti tizingokhalira kuda nkhawa.

6 N’kutheka kuti mwaonapo anthu ena moyo wawo utasintha kwambiri chifukwa cha zinthu ngati zimenezi. N’zomveka kuti anthu amada nkhawa chifukwa cha zimene anakumanapo nazo. Anthufe sitinalengedwe kuti tizikumana ndi mavuto. M’pake kuti anthu ena amaona kuti moyo wawo unasokonekera chifukwa chokumana ndi mavuto kwa nthawi yaitali. Zotsatira zake, ena amachita zosangalatsa pofuna kuchotsa nkhawa. Ndiye kodi tingatani ngati takumana ndi zoterezi? Tiyeni tione zomwe tingaphunzire kwa Yesu, zimene zingatithandize kulimbana ndi zinthu zomwe zingatisokoneze pa kulambira kwathu.

KODI YESU ANKATANI POLIMBANA NDI ZINTHU ZIMENE ZIKANAMUSOKONEZA?

7. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanamusokoneza Yesu?

7 Pali zinthu zambiri zimene zikanamusokoneza Yesu monga zochitika pa moyo wa anthu komanso nkhani zandale. M’nthawi yake, panali anthu ambiri osauka komanso odwala. (Mat. 14:14; Maliko 14:7) Anthuwa ankaponderezedwa ndi Aroma ndiponso Ayuda anzawo. Anthu ataona kuti Yesu ali ndi mphamvu yochita zodabwitsa, ankafuna kumuveka ufumu. (Yoh. 6:​14, 15) Kuwonjezera pamenepa, Satana anamuyesa Yesu kuti agwiritse ntchito njira zachidule n’cholinga choti akhale wolamulira wa dziko lonse. (Mat. 4:​8, 9) Ndipo mtumwi Petulo, yemwe anali mmodzi mwa anzake apamtima a Yesu, anamulimbikitsa kuti achite zinthu zimene zikanachititsa kuti asakumane ndi mavuto, pomuuza kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye.”—Mat. 16:​21, 22.

8. Kodi Yesu anakwanitsa bwanji kulimbana ndi zinthu zimene zikanamusokoneza?

8 Kodi Yesu anatani polimbana ndi zinthu zimene zikanamusokoneza? Anachita zinthu zitatu. Choyamba, ankaona zinthu mmene Yehova amazionera. (Yoh. 8:28; 14:9) Chachiwiri, ankatanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira. (Mat. 9:35) Ndipo chachitatu, ankadziwa bwino zinthu zomwe zinali zofunikadi. (Yoh. 4:34) Iye anakana mwamphamvu mayesero a Satana komanso sanatengeke ndi mawu omveka ngati omufunira zabwino amene Petulo analankhula, omwe anali osemphana ndi zimene Mulungu amafuna. (Mat. 4:10; 16:23) Yesu sankalola kuti zimene ena ankaganiza, kulankhula komanso kuchita zimulepheretse kukwaniritsa cholinga cha Mulungu. N’zoona kuti zomwe zingatisokoneze panopa, zingasiyane ndi zimene zikanasokoneza Yesu. Koma tikhoza kulimbana ndi zinthu zosokoneza potengera zinthu zitatu zimene Yesu anachitazi.

KODI TINGATANI KUTI TILIMBANE NDI ZINTHU ZOSOKONEZA?

9. Kodi ‘kupitiriza kuzindikira chifuniro cha Yehova’ kumatanthauza chiyani? (Aefeso 5:17)

9 Yesetsani kuti muziganiza ngati mmene Yehova amaganizira. Zimenezi zingakuthandizeni kuti ‘mupitirize kuzindikira chifuniro cha Yehova.’ (Werengani Aefeso 5:17.) Tingadziwe zimene Yehova amasangalala nazo tikamawerenga Mawu ake komanso kuwaganizira. Tingachite zimenezi ngakhale kuti Baibulo silinafotokoze mwachindunji zokhudza zimene tikukumana nazo. Zimenezi zingatheke ngati timaphunzira Baibulo kuti tidziwe mmene Yehova amaganizira n’kumagwiritsa ntchito zomwe tikuphunzirazo.

10. Kodi tingatani kuti tidziwe mmene Yehova amaganizira?

10 Tikhoza kudziwa mmene Yehova amaganizira pophunzira Baibulo komanso kuganizira mmene amachitira zinthu ndi anthu. (Yer. 45:5) Tikamawerenga nkhani za m’Baibulo tingadzifunse kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova? Kodi ndikufunika kusintha chiyani kuti ndiziganiza mmene Yehova amaganizira?’ Komabe tisamaiwale kuti maganizo a Yehova ndi apamwamba kwambiri kuposa athu. (Yes. 55:9) Choncho timamupempha kuti atiphunzitse kuchita zimene iye amafuna. (Sal. 143:10) Timamupemphanso kuti atithandize kumvetsa mmene amaganizira kuti ifenso tizichita zomwezo.—1 Yoh. 5:14.

11. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?

11 Tikayamba kuganiza ngati mmene Yehova amaganizira, timamvetsa kuti iye amafuna kuti tizipewa zinthu zimene zingatisokoneze kuti tikhale okonzeka pamene mapeto a dzikoli akuyandikira. (Mat. 24:44) Iye safuna kuti tilemedwe kwambiri ndi nkhawa. (Mat. 6:​31, 32) Choncho ngati tayamba kudera nkhawa kwambiri zokhudza thanzi lathu, ntchito yathu, malo okhala, zinthu zokhudza banja lathu kapenanso zina, Yehova amatipatsa malangizo amene angatithandize. Iye amatiuza kuti tizimudalira kuti azitipatsa nzeru komanso mphamvu zotithandiza polimbana ndi mavuto athu.—Sal. 55:22; Miy. 3:​5-7.

12. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalalabe ngakhale kuti m’dzikoli mukuchitika zinthu zoipa? (Mateyu 5:3)

12 Muzitanganidwa ndi zinthu zauzimu. Tonsefe timada nkhawa ndi zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli, zomwenso sitingathe kuzisintha. Choncho kuti tisasokonezedwe, tizitanganidwa ndi zinthu zauzimu. Tingamasangalale tikamakwaniritsa zosowa zathu zauzimu chifukwa ndi mmene Yehova anatilengera. (Werengani Mateyu 5:3.) Tikhoza kupeza zosowa zathu zauzimu pophunzira zokhudza Yehova m’Mawu ake komanso kuyesetsa kumutumikira m’njira zosiyanasiyana zomwe tingathe. Tikamachita zimenezi, Yehova adzasangalala nafe chifukwa tidzakhala tikugwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru.—Miy. 23:15.

13. Kodi tingatani kuti ‘tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu’?

13 Akhristufe timakhala otsimikiza mtima kuti ‘tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu.’ (Aef. 5:​15, 16) Sikuti lembali likungonena za mmene timagwiritsira ntchito nthawi tsiku lililonse, koma likutilimbikitsa kuti tiziganizira kwambiri mmene tikugwiritsira ntchito nthawi yathu panopa, Yehova asanawononge dziko loipali. Ndiye kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu? Ngati titamangokhalira kuwerenga, kuonera komanso kumvetsera nkhani za zinthu zoipa zomwe zikuchitika, tikhoza kusokonezedwa, kufooka komanso kusiya kuchita khama pa zinthu zokhudza kulambira. Choncho n’zofunika kudziikira malire pa kuchuluka kwa nkhani zomwe timaonera kapenanso kuwerenga. Tikamachita zimenezi timakhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zauzimu. Ndi bwinonso kuganizira zomwe tingachite kuti tiwonjezere zimene timachita mu utumiki, monga kuchita maulendo obwereza ambiri. Timadziwa kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene wapezeka pothandiza anthu kuti “apulumuke nʼkukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Tim. 2:4.

14. Kodi kutanganidwa ndi zinthu zauzimu kumatithandiza bwanji? (Onaninso chithunzi.)

14 Tikamatanganidwa ndi zinthu zauzimu, timaona moyenera zochitika za m’dzikoli. Sitisunthika tikamaona kuti anthu sakugwirizana pa ndale, chuma sichikuyenda bwino komanso kufalikira kwa matenda. Timadziwa kuti zimenezi zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo. M’malo mosokonezeka chifukwa cha mantha, timakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova adzathetsa mavuto onsewa m’tsogolo. Timakhala odekha tikamapitiriza kudalira Yehova kuti azitithandiza kupirira.—Sal. 16:8; 112:​1, 6-8.

Mwamuna ndi mkazi wake akuyenda ndi timashelefu, kwinaku akuyang’ana mtsogolo ndi chikhulupiriro. Zithunzi: Mbali zosiyanasiyana zosonyeza zochitika zosokoneza za m’dzikoli. 1. Gulu la anthu okwiya likuchita zionetsero. 2. Malo oonetsera zotsatira za zisankho. 3. Asilikali ali kunkhondo. 4. Mankhwala akuchipatala. 5. Tchati chosonyeza kusayenda bwino kwa chuma pakampani.

Ngakhale kuti m’dzikoli muli zosokoneza zambiri, tizitanganidwa ndi zinthu zauzimu (Onani ndime 14)b


15. Kodi kukhala “oganiza bwino” kumatithandiza bwanji? (1 Petulo 4:7)

15 Musamaiwale zinthu zomwe ndi zofunikadi. Anthu ambiri m’dzikoli amangoganizira zokhudza kuchita zinthu zosangalatsa m’malo momaganizira zoti mapeto ayandikira. N’zoona kuti kuchita zosangalatsa sikulakwa. Komabe tiyenera kukhala “oganiza bwino” kuti tisatengere maganizo a anthu am’dzikoli pa nkhaniyi. (Werengani 1 Petulo 4:7.) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti kuona zinthu moyenera kumatithandiza kuti tisamangokhalira kuchita zinthu zosangalalatsa, koma tizisankha zinthu mwanzeru. Zimene tingasankhe zingasonyeze ngati tikuyendera maganizo a Yehova komanso timadziwa zinthu zomwe ndi zofunikadi.—2 Tim. 1:7.

16. Kodi Yesu ankaganizira kwambiri chiyani atatsala pang’ono kuphedwa?

16 Nthawi zonse Yesu ankakumbukira zinthu zofunika kwambiri. Ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri, kutatsala maola ochepa kuti aphedwe, maganizo ake onse anali pa kukhalabe wokhulupirika komanso kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu. N’chifukwa chake pa nthawiyi anapemphera kwambiri. Mosiyana ndi Yesu, ophunzira ake ankagona. Iwo anali “atafooka ndi chisoni.”—Luka 22:​39-46; Yoh. 19:30.

17. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, nanga zimenezi zingawasokoneze bwanji? (Onaninso chithunzi.)

17 Mofanana ndi ophunzira a Yesu, ifenso nthawi zina tingakhumudwe komanso kutopa. Zochitika za m’masiku otsirizawa zingatipangitse kuti tizida nkhawa. Pofuna kuiwalako mavuto, anthu ambiri amawononga nthawi yambiri pamalo ochezera a pa intaneti. Iwo amagwiritsa ntchito malowa polumikizana ndi anzawo ndi achibale awo padziko lonse n’kumatumizirana nkhani, zithunzi ndi zinthu zina. Amangokhaliranso kuonerapo mavidiyo komanso kusewera magemu. Komatu anthuwa amawononga nthawi komanso mphamvu zawo zambiri pofuna kuona zinthu zatsopano zomwe zachitika. Kuti tizigwiritsa ntchito moyenera malo ochezera a pa intaneti, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi kugwiritsa ntchito malowa kumandithandizadi kukhala wosangalala kapena kumandilepheretsa kuzindikira zinthu zimene ndi zofunikadi?’

Mlongo ali kunyumba kwake, akuwerenga Baibulo koma akusokonezedwa ndi mauthenga apafoni yake ochokera pamalo ochezera a pa intaneti, pulogalamu yoonetserapo mafilimu komanso pulogalamu yogulitsirapo malonda.

Kukhala oganiza bwino kumatithandiza kuti tisasokonezedwe ndi malo ochezera a pa intaneti komanso zosangalatsa (Onani ndime 17)


18. N’chifukwa chiyani timafunika kukhala oganiza bwino tikamasankha zosangalatsa?

18 Timafunikanso kukhala oganiza bwino pa zimene timaonera komanso magemu amene timasewera kaya ndi pa TV kapena pa intaneti. Zinthu zimenezi zingakhale zosangalatsa komanso zotsitsimula. Koma tiyenera kukhala oganiza bwino kuti tizisankha zosangalatsa zoyenera komanso kuti zisamatidyere nthawi. Nthawi zambiri opanga mavidiyo amakopa anthu kuti aonere mavidiyo atsopano ndipo mavidiyowa amaonetsa zinthu zachiwawa kapena zachiwerewere. Taganizirani zomwe zinachitikira m’bale wina wa ku Asia. Iye anayamba ndi kuonera timavidiyo ting’onoting’ono tosonyeza zimene zili m’mafilimu ena patsamba lina la pa intaneti. Pamene ankapitiriza kuonera, anayamba kuonera tizigawo ta zinthu zachiwerewere m’timavidiyoto. N’kupita kwa nthawi anayamba kuonera zolaula. Koma n’zosangalatsa kuti mothandizidwa ndi akulu komanso anzake apamtima, anachitapo kanthu. Anadilita mapulogalamu oonerapo mavidiyo ndipo anadziikira malire a mmene angamagwiritsire ntchito foni yake. Chitsanzo cha m’baleyu chikutithandiza kumvetsa chifukwa chake timafunika kukhala oganiza bwino tikamasankha zosangalatsa.

19. Kodi chingachitike n’chiyani tikamangoganizira zopeza nthawi yopuma?

19 Tiyeneranso kukhala oganiza bwino pa nkhani yokhudza nthawi yopuma. Tonsefe timafunika nthawi yopuma chifukwa imatithandiza kukhala ndi thanzi labwino. Koma ngati titamangoganizira zopeza nthawi yopuma, tikhoza kuyamba kuchita zinthu mopitirira malire n’kuwononga nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri. (Afil. 1:10) Aliyense amayenera kusankha yekha zimene akufuna kuchita komanso kuchuluka kwa nthawi yochitira zinthuzo. Mukamasankha zochita pa nkhani ngati zimenezi muzidzifunsa kuti: ‘Kodi kuchuluka kwa nthawi imene ndimapuma, kumasonyeza kuti ndine woganiza bwino? Kodi pamenepa ndingakhale kuti ndikusankha zinthu zomwe ndi zofunikadi kwambiri komanso kukonzekera “mapeto a zinthu zonse”?’

20. Kodi kulimbana ndi zinthu zosokoneza kumatithandiza bwanji?

20 Timapeza madalitso ambiri tikamayesetsa kulimbana ndi zinthu zimene zingasokoneze ndandanda yathu yochitira zinthu zauzimu. (Yes. 48:17) Ndi thandizo la Yehova, tikhoza kumapirira mavuto amene timakumana nawo ndipo sitingamade nkhawa kwambiri ndi zochitika za m’dzikoli. Sitingamawonongenso nthawi yambiri pa zinthu zosangalatsa. Choncho tiyeni tikhale otsimikiza mtima kuti tiziganiza ngati Yehova, tizitanganidwa ndi zinthu zauzimu komanso nthawi zonse tizichita zinthu zomwe ndi zofunikadi. Tikamachita zimenezi, tidzapewa zinthu zosokoneza komanso ‘tidzagwira mwamphamvu moyo weniweniwo.’—1 Tim. 6:19.

KODI TINGALIMBANE BWANJI NDI ZOSOKONEZA . . .

  • tikamaganiza ngati mmene Yehova amaganizira?

  • tikamatanganidwa ndi zinthu zauzimu?

  • tikamaonetsetsa kuti tikuchita zinthu zomwe ndi zofunikadi?

NYIMBO NA. 129 Tipitirizebe Kupirira

a TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mawu akuti zinthu zauzimu akutanthauza chilichonse chimene timachita polambira Yehova monga kuphunzira Baibulo, kusonkhana, kulambira kwa pabanja komanso kulalikira. Timalambiranso Yehova tikamasamalira komanso kumanga malo ochitirapo misonkhano, tikamathandizapo pa mavuto osiyanasiyana, tikamagwira ntchito yongodzipereka pamisonkhano ikuluikulu komanso tikamatumikira pa Beteli.

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja latanganidwa ndi ntchito yolalikira m’malo mosokonezedwa ndi zochitika za m’dzikoli

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena