Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 February tsamba 30-tsamba 31 ndime 7
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhala Ogalamuka Molimbana ndi “Mtendere ndi Chisungiko” monga Kwaganiziridwa ndi Mitundu
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Lingaliro Labaibulo la mtendere ndi Chisungiko
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 February tsamba 30-tsamba 31 ndime 7
Atsogoleri a mayiko aimirira pafupi ndi likulu la bungwe la United Nations uku akulengeza kuti “bata ndi mtendere” ku gulu la anthu omwe akusangalala.

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ndi liti pamene mayiko adzalengeze kuti “bata ndi mtendere”?

Monga mmene tinafotokozera munkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” yomwe ili m’magazini ya Nsanja ya Olondaa yaposachedwapa, Yehova adzaika “maganizo ake” m’mitima mwa “nyanga 10,” zomwe ndi maulamuliro onse a padzikoli, kuti adzapereke mphamvu zawo kwa ‘chilombo chofiira kwambiri,’ chomwe ndi bungwe la United Nations. Chilombo chimenechi chimatchulidwanso kuti “chifaniziro cha chilombo.” (Chiv. 13:​14, 15; 17:​3, 16, 17) “Nyanga 10” komanso chilombo chimene chidzapatsidwe mphamvucho, zidzathetsa zipembedzo zabodza padziko lonse. Ndiye kodi mayiko adzalengeza kuti “bata ndi mtendere,”b zipembedzo zabodza zisanawonongedwe kapena zitawonongedwa kale?—1 Ates. 5:3.

Mwachidule, sitikudziwa nthawi yeniyeni imene mayiko adzalengeze kuti “bata ndi mtendere.” Tikanakhala kuti tikudziwa zonse pa nkhaniyi, panalibe chifukwa choti tizikhala maso komanso tcheru. Koma paja Yesu anachenjeza otsatira ake mobwerezabwereza kuti ‘apitirize kukhala maso.’ (Mat. 24:42; 25:13; 26:41) Tsopano tiyeni tione bwinobwino ulosi wouziridwawu womwe mtumwi Paulo analemba m’kalata yake yopita kwa Atesalonika.

Paulo analemba kuti: “Akadzangonena kuti, ‘Bata ndi mtendere!’ nthawi yomweyo adzawonongedwa. Tsoka limeneli lidzawagwera modzidzimutsa.” (1 Ates. 5:​2, 3) Pofotokozera mawu a Paulowa, nthawi zambiri mabuku athu akhala akunena kuti mayiko adzalengeza kuti “bata ndi mtendere” chisautso chachikulu chitangotsala pang’ono kuyamba. Chisautsochi chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zabodza. Takhala tikufotokozanso kuti kulengeza kumeneku, kudzakhala chizindikiro chakuti chisautso chachikulu chatsala pang’ono kuyamba.

Pambuyo pofufuza nkhaniyi mosamala kwambiri, taona kuti tikhoza kuifotokozanso mwa njira ina. N’kutheka kuti kulengezedwa kwa “bata ndi mtendere” kudzachitika pambuyo poti zipembedzo zabodza zawonongedwa. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani mafunso otsatirawa.

Kodi zipembedzo zabodza zakhala zikukhudzidwa bwanji pankhondo za mayiko? Baibulo limafotokoza kuti: “Mwa iye [‘hule lalikulu,’ Babulo Wamkulu] munapezeka magazi a . . . onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chiv. 17:​1, 5; 18:24) Kuyambira kalekale, hule lalikululi lakhala likulimbikitsa nkhondo zamayiko komanso zinthu zauchigawenga. Choncho zipembedzo zabodza zakhala zikuyambitsa nkhondo komanso zachiwawa, osati kulimbikitsa bata ndi mtendere. Zimenezi zikubweretsa funso lakuti: Kodi ndiye kuti basi mayiko adzalengeza kuti “bata ndi mtendere” pambuyo poti Babulo Wamkulu wawonongedwa? N’kutheka kuti adzatero, koma sitinganeneretu.

N’chiyani chimene chidzachitike pambuyo poti mayiko alengeza kuti “bata ndi mtendere”? Paulo anati: “Nthawi yomweyo adzawonongedwa. Tsoka limeneli lidzawagwera modzidzimutsa.” (1 Ates. 5:3) Ngati maboma adzalengeze kuti “bata ndi mtendere” pambuyo poti zipembedzo zabodza zawonongedwa, ndiye kuti kuwonongedwa kwa mabomawo kudzachitika mwadzidzidzi kwambiri.

Kodi anthu a Yehova adzatani zinthu zimenezi zikadzachitika? Paulo anati: “Abale, simuli mumdima kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene akuba amadzidzimukira kunja kukawachera.” (1 Ates. 5:4) Taganizirani izi: Ngati mayiko adzalengeze kuti “bata ndi mtendere” pambuyo poti zipembedzo zabodza zawonongedwa, ndiye kuti anthu a Yehova adzadziwa kuti mayikowo atsala pang’ono kwambiri kuwonongedwa. Mosiyana ndi zimenezi, mayiko akadzangolengeza kuti “bata ndi mtendere,” azidzaona kuti ndi otetezeka ndipo sadzayembekezera kuti awonongedwa. Kuwonongedwa kwawo kudzakhala kodzidzimutsa ngati kubwera kwa wakuba.

Komabe zomwe tikudziwa n’zakuti, mtsogolomu “nyanga 10” komanso chilombo chimene chidzapatsidwe mphamvu, zidzawononga zipembedzo zabodza. Kumeneku kudzakhala kuyambika kwa chisautso chachikulu. Tikudziwanso kuti pa nthawi inayake, mayiko adzalengeza kuti “bata ndi mtendere.” Kodi zimenezi zidzachitika liti? Takambirana zinthu ziwiri. Choyamba: Mayiko akhoza kudzalengeza kuti “bata ndi mtendere,” zipembedzo zabodza zisanawonongedwe. Chachiwiri: Mayiko akhoza kudzalengeza kuti “bata ndi mtendere” pambuyo poti awononga zipembedzo zabodza. Tiyeni tingodikira kuti tidzaone zomwe zidzachitike. Nthawi zambiri timamvetsa bwino maulosi a m’Baibulo pamene akukwaniritsidwa, kapena pambuyo poti akwaniritsidwa kale.—Yerekezerani ndi Yohane 12:16.

Panopa chofunika kwambiri si nthawi imene mayiko adzalengeze kuti “bata ndi mtendere,” koma kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Tiyenera ‘kukhalabe maso ndiponso tikhalebe oganiza bwino’ n’cholinga choti tikhale okonzeka mokwanira, posatengera mmene zinthu zidzachitikire.—1 Ates. 5:6.

a Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya November 2025.

b Mawu amene mtumwi Paulo anawagwiritsa ntchito palembali, akusonyeza kuti akhozanso kudzalengeza zimenezi maulendo angapo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena