Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 February tsamba 32
  • Obadiya​—⁠Phunzirani Kuopa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Obadiya​—⁠Phunzirani Kuopa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Nkhani Yofanana
  • Kulimba Mtima Chifukwa cha Chikhulupiriro ndi Kuopa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Obadiya, Yona, ndi Mika
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Machenjezo Aumulungu Amene Amakuyambukirani
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 February tsamba 32

MUNTHU WOTCHULIDWA M’BAIBULO

Obadiya—Phunzirani Kuopa Mulungu

Obadiya anali woyang’anira nyumba ya mfumu yoipa Ahabu, yomwe inalola kuti kulambira Baala kufalikire mu Isiraeli. Komabe Obadiya anaphunzira kuopa Yehova ‘kuyambira ali mwana.’ (1 Maf. 18:​1-13) Ndiye Mfumukazi Yezebeli italamula kuti aneneri onse a Yehova aphedwe, Obadiya anadziwa kuti ayenera kuchita zinthu molimba mtima kuti zimenezi zisachitike. Zinali zoopsa kungobisa ngakhale mneneri mmodzi, koma Obadiya anabisa aneneri 100 n’kumawapatsa chakudya pa nthawi imenenso kunali njala yaikulu. Sizinalitu zophweka kuti aneneri abodza mahandiredi omwe ankatumikira mfumu ndi mfumukazi asadziwe zimenezi.—1 Maf. 18:19.

Kodi tingaphunzire chiyani kwa munthu yemwe anali woopa Mulunguyu? Ngakhale kuti Obadiya ankachita mantha ndi Ahabu, iye ankaopa kwambiri Mulungu. Zimenezi zinamuthandiza kuti alimbe mtima n’kuika moyo wake pangozi kuti ateteze abale ake. Ngati ntchito yathu ndi yoletsedwa m’dziko limene tikukhala, ifenso tiyenera kuyesetsa kuti tiziopa Mulungu. Mantha amenewo adzatithandiza kukhala olimba mtima kuti tizithandiza abale ndi alongo athu amene akukumana ndi mavuto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena