APRIL 27–MAY 3, 2026
NYIMBO NA. 99 Abale Ambirimbiri
Kodi Mwakonzekera Mavuto Amene Mungakumane Nawo Mukabatizidwa?
“Ndithandizeni kuti ndipitirize kuyenda mʼnjira zanu.”—SAL. 17:5.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tikambirana zimene anthu omwe angobatizidwa kumene angachite kuti akonzekere mavuto amene angakumane nawo.
1-2. Kodi tingatani kuti tikonzekere mavuto amene tingakumane nawo? Perekani chitsanzo.
TIMADZIWA kuti tizikumana ndi mavuto m’dziko la Satanali. M’pake Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Zopunthwitsazo ziyenera kubwera ndithu.” (Mat. 18:7) Poganizira zimenezi, tiyenera kukhala okonzeka kuti tizikumana ndi mavuto, kuphatikizaponso kukhumudwitsidwa ndi Akhristu anzathu.
2 Taganizirani chitsanzo ichi: Nthawi zonse anthu a Yehova amalimbikitsidwa kuti azikonzekera ngozi zam’chilengedwe. Ndiye kodi timakonzekera bwanji? Choyamba, timaganizira ngozi zimene zingachitike m’dera lathu. Izi n’zofunika kwambiri makamaka ngati tangobwera kumene m’deralo. Tikadziwa ngozi zimene zingachitike, timafunika kukhala ndi pulani ya zimene tingadzachite pangozi iliyonse. (Miy. 21:5) Mofanana ndi zimenezi, timafunika kudziwiratu mavuto amene tingakumane nawo pambuyo pobatizidwa n’kuona zomwe tingadzachite kuti tithane nawo. Zimenezi zingadzatithandize kuti tisadzakhumudwe kwambiri ndiponso kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova. (Sal. 17:5) Choncho tiyeni tikambirane mavuto atatu omwe tingadzakumane nawo komanso zimene tingadzachite pa vuto lililonse.a
M’BALE KAPENA MLONGO AKAKUKHUMUDWITSANI
3. Kodi mungakumane ndi vuto liti mukabatizidwa?
3 Kodi munamva bwanji mutafika pamisonkhano kwa nthawi yoyamba n’kuona chikondi cha anthu a Yehova? N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinakuthandizani kutsimikizira kuti mwapeza choonadi. (Yoh. 13:35; Akol. 3:12) Ndi mmenenso Blancab anamvera. Koma atabatizidwa anakumana ndi zinthu zimene sankayembekezera. Iye anati: “Mlongo wina sanandichitire zinthu mokoma mtima. Ndinamumvanso akulankhula zinthu zoipa zokhudza anthu ena. Sindinkayembekezera zimenezi chifukwa ndinaphunzira kuti a Mboni amayesetsa kukhala mwamtendere komanso amakondana.” N’zoona kuti abale ndi alongo anu amayesetsa kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Komabe anthu a Yehova si angwiro. (Aef. 4:23, 24; 1 Yoh. 1:8) Choncho muziyembekezera kuti nthawi ina, munthu wina adzalankhula kapena kuchita zinthu zokukhumudwitsani. (Yak. 3:8) N’zomvetsa chisoni kuti mavuto ngati amenewa achititsa ena kusiya kutumikira Yehova.
4. Kodi mungatani kuti mukonzekere zimene mungachite ngati m’bale kapena mlongo atakukhumudwitsani? (Aefeso 4:32)
4 Kodi mungatani kuti panopa mukonzekere zomwe mungachite, ngati m’bale kapena mlongo atakukhumudwitsani? Mukhale ndi chizolowezi choti muzitsatira malangizo opezeka pa Aefeso 4:32. (Werengani.) Mukamayesetsa kukhala wachifundo komanso wokoma mtima, zidzakuthandizani kuti mupewe kumangokangana ndi anthu ena. Muzikhala ndi cholinga choti muzikhululuka ndi mtima wonse anthu ena akakukhumudwitsani. N’chiyani chingakuthandizeni kuchita zimenezi? Taganizirani kuchuluka kwa nthawi zimene mumapempha Yehova kuti akukhululukireni komanso mmene amachitira zimenezi ndi mtima wonse. (Mat. 6:12) Mukamaganizira maulendo ochuluka amene Yehova wakhala akukukhululukirani, zimakhalanso zosavuta kuti muzikhululukira ena.
5. Kodi ndi mfundo iti ya m’Baibulo imene ingatithandize ngati munthu wina watikhumudwitsa? (Miyambo 19:11) (Onaninso zithunzi.)
5 Werengani Miyambo 19:11. Baibulo limanena kuti munthu akatikhumudwitsa, kuzindikirac kungatichititse kuti tibweze mkwiyo. Mfundo imeneyi inathandiza Rima, yemwe anabatizidwa zaka zingapo zapitazo. Iye anati: “Abale ndi alongo akachita zinthu zondikhumudwitsa, choyamba ndimakumbukira lemba la Miyambo 19:11. Ndimaganizira mmene zinthu zilili pa moyo wawo, zimene anakumana nazo komanso zimene zawapangitsa kuchita zinthu mwa njira imeneyo. Ndimayesetsanso kulowa nawo mu utumiki. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndiwadziwe bwino.” Amenewatu ndi malangizo abwino chifukwa angakuthandizeni kuti muwadziwe bwino abale ndi alongo anu. Mukatero, m’pamenenso zimakhala zosavuta kuti muwakhululukire.
Ngati mwasemphana maganizo ndi m’bale kapena mlongo, mungamupemphe kuti muyendere limodzi mu utumiki (Onani ndime 5)
6. N’chiyani chingatithandize kuti tizigwirizana ndi Akhristu anzathu mumpingo?
6 Kodi mungatani kuti muzigwirizana ndi Akhristu anzanu mumpingo? Pamene mukuyesetsa kuwadziwa bwino abale ndi alongo anu, muziganizira kwambiri makhalidwe awo abwino. (Yerekezerani ndi Miyambo 10:12; Aroma 12:10; Afil. 2:2, 3) Onani mmene kuchita zimenezi kunathandizira m’bale wina dzina lake Mark atangobatizidwa kumene. Atayamba kucheza kwambiri ndi abale ndi alongo mumpingo mwake, anayambanso kudziwa kwambiri zimene anzakewo amalakwitsa. N’chiyani chinathandiza Mark kuti asakhumudwe ndi zimenezo? Iye anati: “Ndinazindikira kuti zimene abale ndi alongo amalakwitsazo ndi zazing’ono kwambiri poyerekeza ndi zoipa zimene anthu m’dzikoli amachita. Ndiye ndinaona kuti ndisamangoganizira zimene Akhristu anzanga amalakwitsa. Choncho ndinayamba kuganizira makhalidwe awo abwino.” Ngati inunso mutamachita zimenezi, mukhoza kumagwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo anu mumpingo.
MUKAYAMBA KULAKALAKA ZINTHU ZOMWE MUNAZISIYA
7. Kodi n’chiyani chingachititse kuti muyambe kulakalaka zinthu zomwe munazisiya?
7 N’zosakayikitsa kuti mutaphunzira choonadi, munasangalala kwambiri chifukwa choti munasiya kukhala kumbali ya dziko la Satanali. Ndiye mwina mungadabwe kuti, ‘Zingatheke bwanji kuti munthu ayambirenso kulakalaka zinthu zomwe anasiya?’ Mukamakumana ndi mavuto, mukhoza kuyamba kukumbukira komanso kulakalaka zina mwa zinthu zomwe munasiya pamene munayamba kutumikira Yehova. (Yerekezerani ndi Numeri 11:4-6.) Mwachitsanzo, abale ena anasankha kusiya ntchito yapamwamba yomwe inkawadyera nthawi. N’kuthekanso kuti ena, anzawo apamtima anasiya kucheza nawo chifukwa choti anayamba kuphunzira Baibulo. Pamene ena ankafunika kusiya chizolowezi chochita khalidwe linalake lodetsa ngakhale kuti ankasangalala nalo. Zingakhaletu zomvetsa chisoni kwambiri ngati Mkhristu atalola kuti zinthu zomwe anazisiya m’mbuyo zimusiyitse kutumikira Yehova. Ndiye kodi mungatani panopa kuti mavuto alionse amene mungadzakumane nawo asadzakuchititseni kubwerera ku zinthu zakale?
8. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara?
8 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu okhulupirika omwe akanatha kuyamba kulakalaka zinthu zomwe anazisiya m’mbuyo. Mwachitsanzo, pomvera lamulo la Yehova, Abulahamu ndi Sara anachoka mumzinda wotetezeka wa Uri n’kumakakhala m’matenti. (Aheb. 11:8, 9) N’zosakayikitsa kuti nthawi zina ankakumbukira moyo wofewa womwe ankakhala ku Uri. Koma “akanakhala kuti ankangoganizira” kapena kulakalaka zinthu zomwe anazisiya m’mbuyo, akanayesedwa kuti abwerere ku moyo wofewawu. M’malomwake ankaganizira za madalitso a m’tsogolo.—Aheb. 11:15, 16.
9. Kodi mtumwi Paulo ankaziona bwanji zinthu zomwe anazisiya m’mbuyo? (Afilipi 3:7, 8, 13)
9 Mtumwi Paulo anasintha zinthu pa moyo wake kuti azitumikira Yehova. Asanakhale Mkhristu, iye anaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli, mphunzitsi wa Chilamulo wolemekezeka. (Mac. 22:3) Apatu Paulo akanakhala ndi udindo wapamwamba m’chipembedzo cha Chiyuda. (Agal. 1:13, 14) Koma ataphunzira choonadi anasiya zonsezo. Ndiye kodi moyo unali wophweka pambuyo poti wakhala Mkhristu? Ayi. Iye ankamenyedwa, kuikidwa m’ndende komanso anthu amtundu wake ankadana naye. (2 Akor. 11:23-26) Akanakhala kuti ankaganizira kwambiri mavuto amene ankakumana nawo, n’kumawayerekezera ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wake m’mbuyomo, akanayamba kuona kuti zinthu zinali bwino asanakhale Mkhristu. Koma Paulo ankaganizira kwambiri mwayi wamtengo wapatali umene anali nawo wotumikira Khristu Yesu komanso madalitso amene adzalandire m’tsogolo. Iye sankakayikira kuti madalitsowo anali oposa zinthu zonse zomwe anasiya.—Werengani Afilipi 3:7, 8, 13.
10. Kodi nthawi zonse tiyenera kumaganizira za chiyani? (Maliko 10:29, 30) (Onaninso zithunzi.)
10 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mukayamba kuganizira zinthu zomwe munasiya kuti mukhale Mkhristu, muzikumbukiranso chifukwa chake munazisiya. (Mlal. 7:10) Muziyerekezera zomwe munasiya ndi madalitso omwe mwapeza chifukwa chodziwa choonadi. Panopa muli pa ubwenzi wabwino ndi Wolamulira Wamkulu wachilengedwe chonse. (Miy. 3:32) Muli ndi abale ndi alongo anu padziko lonse omwe amakukondani kwambiri. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Mukuyembekezeranso zinthu zabwino kwambiri m’tsogolomu. (Yes. 65:21-23) Nthawi zonse mukamaganizira madalitso amene mumapeza chifukwa chotumikira Yehova, simungamalakelake zinthu zimene munazisiya.
M’malo momalakalaka zinthu zimene tinazisiya, tizisangalala ndi utumiki umene Yehova anatipatsa (Onani ndime 10)e
11. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Rosemary?
11 Mlongo wina dzina lake Rosemary anabatizidwa ali ndi zaka za m’ma 50. Taonani zimene anachita kuti asamalakelake zinthu zimene anazisiya. Iye anati: “Poyamba ndinkaisowa Khirisimasi chifukwa choti inali nthawi imene ndinkasangalala ndi anthu a m’banja lathu. Ndinkamva bwino ndikamapereka mphatso kwa anthu omwe ndimawakonda. Zinkandisangalatsa kuona ana atazungulira maluwa a Khirisimasi nkhope zawo zili zachimwemwe akamatsegula mphatso zomwe ndawapatsa.” Ndiye kodi n’chiyani chimamuthandiza? Rosemary anati: “Ndimachita zinthu zina m’malo mwa Khirisimasi. Chaka chilichonse ndimasankha tsiku limene ndingaitane anthu a m’banja lathu, kuwapatsa mphatso komanso kuwafotokozera chifukwa chake ndimawayamikira.” Rosemary anakumananso ndi vuto lina. Iye anati: “Nditaphunzira choonadi, anzanga anasiya kucheza nane. Nthawi zina ndinkawasowa n’kumadziona kuti ndili ndekhandekha.”d Ndiye n’chiyani chinamuthandiza? Anakonza zoti azilowa mu utumiki ndi alongo osiyanasiyana. Iye anati: “Zimenezi zandithandiza kupeza anzanga atsopano omwe ndimawakonda komanso kuwaona kuti ndi amtengo wapatali.” Kodi mungaphunzire chiyani kwa mlongoyu? N’zoona kuti nthawi zina mungamalakelake zinthu zomwe munkasangalala nazo musanaphunzire choonadi. Komabe mukhoza kuchita zinthu zinanso zabwino zomwe zingakuthandizeni kuti muzisangalala. (Afil. 4:8, 9) Muzikumbukiranso kuti Yehova amakupatsani zinthu zambiri kuposa zimene munasiya.
ENA AKASIYA KUTUMIKIRA YEHOVA
12. Kodi mumpingo mungachitike chiyani chomwe chingakhale chovuta kwambiri?
12 Pamene munakhala wa Mboni, n’zosakayikitsa kuti munasangalala kuchoka m’dziko loipali n’kulowa m’gulu la anthu omwe amaphunzitsa choonadi komanso kuyesetsa kuchita zabwino. (Yes. 65:14) Komabe nthawi zina mukhoza kumva kuti wina mumpingo wachita tchimo. Enanso angafike pochotsedwa kumene. (1 Akor. 5:13) Taonani mmene zinthu ngati zimenezi zinakhudzira mlongo wina dzina lake Samar. Iye anati: “Pasanapite nthawi yaitali nditabatizidwa, mkulu wina anachita tchimo lalikulu ndipo anachotsedwa. Ndinakhumudwa kwambiri chifukwa sindinkaganiza n’komwe kuti mkulu angachimwire Yehova komanso mpingo.” N’zoona kuti nthawi zonse tiyenera kukhulupirira kuti abale ndi alongo athu amakonda Yehova ndipo amafunitsitsa kuti asamusiye. (1 Akor. 13:4, 7) Komabe n’zomvetsa chisoni kuti chaka chilichonse anthu ena amachotsedwa mumpingo. Ndipotu zimakhala zopweteka kwambiri ngati munthu amene timamukonda komanso kumulemekeza wasankha kusiya Yehova.
13. Kodi tingatani kuti tilimbitse chikhulupiro chathu panopa kuti ngati munthu wina amene timamukonda atasiya kutumikira Yehova tisadzakhumudwe?
13 Kodi mungachite chiyani panopa kuti mukhale wokonzeka, kuti ngati munthu amene mumamukonda atasiya kutumikira Yehova musadzakhumudwe? Pitirizani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. (Yak. 4:8) Musamalole kuti ubwenzi wanu ndi Mulungu uzidalira pa kukhulupirika kwa munthu wina. Mwachitsanzo, ngakhale kuti timalambira Mulungu limodzi ndi banja lathu komanso mpingo, patokha timafunikanso kumapemphera ndiponso kuwerenga Baibulo nthawi zonse.—Sal. 1:2; 62:8.
14. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha mtumwi Petulo? (Yoh. 6:66-68)
14 Tingaphunzireponso mfundo yofunika pa zimene mtumwi Petulo anachita ophunzira ambiri atasiya kutsatira Yesu. Mtumwiyu ayenera kuti nayenso sanamvetse zimene Yesu ananena pa nthawiyi. Koma taonani zimene Petulo ananena pa Yohane 6:66-68. (Werengani.) M’malo moganizira zimene ena anachita, iye ankaganizira kwambiri mfundo za choonadi zimene Yesu anamuphunzitsa. Zotsatira zake, Petulo sanakhumudwe. Ifenso tizikumbukira kuti ngakhale anthu ena atasiya kutumikira Mulungu, choonadi chimene gulu la Yehova linatiphunzitsa sichisintha ndipo sitiyenera kuchisiya. Samar yemwe tamutchula kale uja anati: “Nthawi zonse ndimadzikumbutsa kuti zoipa zimene munthu mmodzi wachita, sizitanthauza kuti ndi zimene mpingo wonse kapena gulu lonse la Yehova limachita. Ndipo sizisonyezanso kuti ndi mmene Yehova alili.”
15. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Emily?
15 Taganizirani chitsanzo cha Emily. Patangotha wiki atabatizidwa, mayi ake anasiya banja lawo komanso anachotsedwa mumpingo. Emily anati: “Sindinkaganiza n’komwe kuti zimenezi zingachitike. Limeneli ndi vuto lalikulu kwambiri lomwe ndakumana nalo pa moyo wanga ndipo ndimawasowa kwambiri mayi anga.” Ndiye kodi n’chiyani chimene chimamuthandiza? Iye anati: “Sindili ndekha. Bambo anga komanso abale ndi alongo amumpingo, omwe ali ngati anthu a m’banja langa, amandithandiza. Aliyense akukumana ndi mavuto. N’chifukwa chake timafunika kumakondana komanso kumalimbikitsana.” (1 Pet. 5:9) Musamadikire kuti mukumane kaye ndi mavuto kuti muyambe kugwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo anu. Yesetsani kuwadziwa bwino panopa. Mukamachita zimenezi, simudzadzimva kuti muli nokhanokha ngati mutakumana ndi vuto linalake.
16. Kodi tizikumbukira chiyani? (Onaninso chithunzi.)
16 Tizikumbukiranso kuti Yehova amalanga anthu amene amawakonda. (Aheb. 12:6) Iye akufuna kuti onse amene anachotsedwa mumpingo abwerere. (2 Pet. 3:9) Choncho ngati munthu amene mumamukonda wachotsedwa mumpingo, musamakayikire kuti akulu achita zonse zomwe angathe pomuthandiza kuti abwerere kwa Yehova.—2 Tim. 2:24, 25.
Ngati munthu amene timamukonda wachotsedwa mumpingo, tizikumbukira kuti akulu amafunitsitsa kumuthandiza kuti abwerere kwa Yehova (Onani ndime 16)f
17. Kodi tikhale otsimikiza za chiyani?
17 Tangokambirana mavuto ochepa omwe mungakumane nawo mukabatizidwa. N’zoona kuti mungamade nkhawa mukaganizira mavuto ena. Koma simuyenera kuchita mantha. Pali zambiri zomwe mungachite kuti mukonzekere. Musamaiwale kuti Yehova adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika. Iye wakhala akukuthandizani ndipo akufuna kuti azikuthandizani mpaka kalekale. (1 Pet. 5:10) Nthawi zonse adzakupatsani mphamvu komanso kukuthandizani kuti mupirire mavuto alionse amene mukukumana nawo. Ngati mungalole kuti Yehova apitirize kukuthandizani, palibe vuto lomwe lingakuchititseni kuti musiye kumutumikira.—Sal. 119:165; Aroma 8:38, 39.
NYIMBO NA. 154 Chikondi Sichitha
a Ngakhale kuti cholinga cha nkhaniyi ndi kuthandiza anthu omwe angobatizidwa kumene, mfundo zake zingathandizenso tonsefe.
b Mayina asinthidwa.
c Kuzindikira kumaphatikizapo kukhala ndi luso lodziwa zinthu zosaonekera. Khalidweli lingatithandize kudziwa chifukwa chake munthu walankhula kapena kuchita zinthu m’njira inayake.
d Tonse mumpingo tiyenera kuthandiza amene akuphunzira Baibulo komanso omwe angobatizidwa kumene kumva kuti amakondedwa. Onani ndime 15 ndi 16 munkhani yakuti, “Aliyense Mumpingo Angathandize Ophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe” mu Nsanja ya Olonda ya March 2021.
e MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI : Ali mu utumiki, mlongo waona timu ikusewera mpira ndipo wakumbukira nthawi imene nayenso anali katswiri wa masewerawa. Kenako mlongoyo akulalikira mayi wachitsikana yemwe n’kutheka kuti poyamba anali timu imodzi.
f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Akulu awiri apita kwa munthu yemwe anachotsedwa mumpingo ndipo akumulimbikitsa kuti abwerere kwa Yehova.