Baibulo ndi Makhalidwe Abwino a Achichepere
“Achichepere akuwoneka kukhala akulowa m’dziko lothekera loipa koposa ponena za kudzivumbula kwawo ku uthenga wonena za kugonana: Makanema, nyimbo, mawailesi, ndi TV zimawawuza iwo kuti kugonana kuli kwa chikondi, kosangalatsa, kokondweretsa . . . Komabe, pa nthaŵi imodzimodziyo, anthu achichepere amalandira uthenga wakuti atsikana abwino ayenera kunena kuti ayi.”—The Alan Guttmacher Institute.
ACHICHEPERE amasiku ano akula mu mbadwo wa makhalidwe abwino okaikiritsa. Baibulo, ngakhale kuli tero, limapereka chitsogozo chomvekera, chosakaikirika pa mkhalidwe wabwino wa kugonana. Pamene kuli kwakuti maprogramu a maphunziro a zakugonana alunjikitsa pa kupewa kukhala ndi pakati, Baibulo limasonyeza kuti kugonana kwa otomerana iko kokha kuli chinthu choyenera kupewedwa. “Mungakhale otsimikizira ndithu kuti palibe wina aliyense amene m’chenicheni amadzilowetsa mu dama [limene limaphatikizapo kugonana kwa osakwatirana] kapena kupanda chiyero kapena chisembwere . . . angalowe m’malo china chirichonse cha Ufumu wa Mulungu,” limatero Baibulo. (Aefeso 5:5, The Jerusalem Bible) Mwachimvekere, mayanjano akugonana ali olekezera mu ukwati.
Yankho ku vuto la mimba za achichepere chotero liri, osati kuwaphunzitsa achichepere kumwa mankhwala oletsa kukhala ndi pakati, koma kuwapatsa iwo chitsogozo cha makhalidwe abwino ndi chauzimu. Baibulo limachimveketsa bwino kuti ndi thayo la ndani la kupereka chitsogozo chimenechi: “Atate inu, musakwiitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova NW].”—Aefeso 6:4.
M’kufufuza kumodzi, ngakhale kuli tero, achichepere anafunsidwa “kundandalika makolo awo pa mlingo wochokera ku osakhutiritsa kufika ku okhutira kwambiri monga magwero a chidziŵitso cha kugonana. Kundandalika kwa anamwali ndi kwa amayi awo kunali mokulira mwa ndandanda ya osakwaniritsa kwenikweni. Kundandalika kwa atate kunali kosakhutiritsa kwenikweni.” Kodi chiri chotsimikizirika, chotero, kuyembekezera makolo kupereka kwa ana awo chitsogozo mu nkhani za kugonana?
Kupatsa Achichepere Chitsogozo cha Makhalidwe Abwino
Pa Miyambo 4:1-4, Mfumu Solomo akufulumiza achichepere kuti: “Ananu, mverani mwambo wa atate, . . . Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga, wokondedwa ndi mayi, ndine ndekha, sanabala wina. Atate nandiphunzitsa nati kwa ine: ‘Mtima wako uwumirire mawu anga.’” Chiri chachidziŵikire kuti Solomo anali wokhoza kukambitsirana ngakhale zinthu zathithithi ndi atate wake; Solomo iyemwini anapitiriza kukambitsirana mkhalidwe woipa wa chisembwere mu mkhalidwe wowona mtima koposa.—Miyambo 5:1-19.
Pakati pa Mboni za Yehova, mabanja ambiri akusungirira kalankhulidwe komasuka kofananako ndi ana awo—ndi chipambano chachikulu! Iwo amachita zoposa kungowawuza kokha ana awo kuti “Ayi!” ponena za maunansi a kugonana. Baibulo limathandiza iwo kupereka kwa ana awo zifukwa zomveka za kupeŵera chisembwere. Lingalirani, kachiŵirinso, mawu a Solomo. Pa Miyambo 5:3, 4, iye akulimbikitsa amuna achichepere kupewa kukhala ndi mayanjano a kugonana ndi mkazi wadama. “Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere [mkazi wa dama] ikukha uchi, mkamwa mwake muti see koposa mafuta.” Inde, ziyembekezo za mkhalidwe woipa zingawoneke kukhala zosangalatsa. Komabe, akuchenjeza Solomo: “Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo, ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthwa konse konse.”
Mofanana ndi Solomo, makolo angalingalire ndi ana awo pa zotulukapo za pambuyo pa unansi wa kugonana. Monga chikumbumtima chovutitsidwa, mimba zosafunidwa, matenda opatsirana mwa kugonana monga ngati AIDS—izi ziri zotulukapo zowawa za mphindi zowerengeka za chisangalalo chokondweretsa. Solomo mowonjezereka akuchenjeza achichepere kuti asapereke “ulemu [wawo] kwa ena.” (Miyambo 5:9) Kodi icho sichimasonyeza kusoweka kwa kudzilemekeza kwa achichepere kudzipereka iwo eni kwa wina wake amene sali wokondweretsedwa mu ukwati? Kodi icho sichiri chochititsa manyazi kutumikira kokha monga njira ya kukhutiritsa zisonkhezero zadyera za inumwini kapena za wina? Makolo angathandize ana awo kuyamikira nsonga zimenezo.
Solomo anapereka uphungu wowonjezereka ponena za kuchita ndi munthu wa makhalidwe oipa: “Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo, osayandikira ku khomo la nyumba yake.” (Miyambo 5:8) Mofananamo, makolo angapereke uphungu wogwira ntchito kwa ana wa kupewa mikhalidwe yogonjeretsa. Iwo angafulumize iwo kusapita ku kucheza ndi anthu opanda maprinsipulo abwino. Ndipo pamene iwo afika pa nsonga ya kukhala okwaniritsidwa kulondola kupalana ubwenzi, iwo angalimbikitsidwe kutenga masitepi okhoza kugwirirapo ntchito kuti apewe mkhalidwe wochimwa. Mwachitsanzo, aŵiri omwe ali pa ubwenzi angakonze kaamba ka winawake nthaŵi zonse kukhala nawo pamene apita kukacheza. Zachikale? Mwinamwake. Koma chiri chabwino kutenga kuchinjiriza koyenerera koposa ndi “kulira pa chimaliziro chako, pothera nyama yako ndi thupi lako; ndi kuti: ‘Bwanji ndinada mwambo, . . . ndipo sindinamvera mawu a aphunzitsi anga.’”—Miyambo 5:11-13.
Kuthandiza Achichepere Kuwopa Yehova
Mogwirizana ndi ziyerekezo zina, pali achichepere oposa mamiliyoni 12 omwe ali okangalika mwa kugonana mu United States mokha. Ngakhale mliri wa AIDS wachita zochepa kuletsa funde la khalidwe loipa limeneli. Komabe, Mboni za Yehova zimayesera kuika mwa ana awo chinachake chosonkhezera kwambiri kuposa kuwopa AIDS kapena mimba: kuwopa Yehova Mulungu kwa umoyo. Solomo akukumbutsa achichepere pa Miyambo 5:21 kuti: “Pakuti njira za munthu ziri pamaso pa Yehova, asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.” John, mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo atate wa ana anayi, akupereka uphungu uwu: ‘Chomwe chimathandiza chiri chakuti ana akhale ndi kuwopa Yehova kwa chikondi. Musawope kulola mwana wanu kudziŵa kuti Yehova angakwiitsidwe ndi njira yathu ya kagwiritsidwe kadyera.’—Yerekezani ndi Miyambo 27:11.
Ndithudi, kuti kuwopa Mulungu kukhale choletsa chokhutiritsa cha mkhalidwe woipa, Mulungu ayenera kukhala weniweni kwa munthu wachichepere. (Yerekezani ndi Ahebri 11:27.) Makolo angathandize ana awo kukulitsa unansi weniweni ndi Mulungu kupyolera mu phunziro lokhazikika la Baibulo, pemphero la tsiku ndi tsiku, ndi chokumana nacho cha moyo weniweni. Pamene wachichepere afikira ku kuyamikira kuti Mulungu amamsamalira iye, iye adzasonkhezeredwa kupewa mkhalidwe womwe sungamkondweretse iye.—1 Petro 5:7.
Mosangalatsa, unansi wa achichepere ndi Mulungu ungakhalenso wa thandizo m’kukwaniritsa zofunika zina zimene kaŵirikaŵiri zimangopita popanda kukwaniritsidwa mwa achichepere ena ambiri. Akatswiri amanena kuti, mwachitsanzo, chisembwere chiri njira yofala ya achichepere ya kuthetsera malingaliro a kupanda mphamvu kapena kusoweka kwa kudzilemekeza. Malingaliro oterowo, ngakhale kuli tero, samafunikira kukantha mmodzi amene ali pa ubwenzi ndi Yehova! Wachichepere woteroyo anganene kuti: “Mulungu ndiye mthandizi wanga; [Yehova NW] ndiye wachirikiza moyo wanga.”—Masalmo 54:4.
Kawonedwe Kolinganizika ka Kugonana ndi Ukwati
Ndithudi, makolo safuna kuti ana awo akulitse kawonedwe ka manyazi kapena koipa ka kugonana. Pamene kuli kwakuti Baibulo limatsutsa dama, limasonyezanso kuti mayanjano a kugonana angakhale okongola—mkati mwa chomangira cha ukwati, kunena kwake titero. Akugwiritsira ntchito mawu a ndakatulo, Solomo akuwonjezera: “Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula naye. . . . Maere ake akukwanire nthaŵi zonse. Ukondwe ndi chikondi chake chosaleka.”—Miyambo 5:18, 19.
Kulingalira kawonedwe kapamwamba kameneka ka maunansi a mu ukwati, palibe chifukwa kwa makolo cha kumvera moipidwa mu kukambitsirana nkhani za mwathithithi. Akutero John (yemwe walozedwako poyambirirapo): “Nthaŵi zonse timalankhula mowona mtima ndi iwo, chotero nkhani ya kugonana siiri ya chinsinsi. Timawunikira kuti ndi mphatso yochokera kwa Mlengi, Yehova, yoyenera kusangalalidwa ndi mwamuna ndi mkazi pa nthaŵi yoyenera.” Akutero tate wina wa anyamata achichepere aŵiri: “Kuyambira ku zaka zawo za kumayambiriro, takambitsirana nkhani ya kugonana mowona mtima ndi iwo. Tayesera kuwaphunzitsa iwo kawonedwe kolemekezeka, kokonzeka ka chikondi ndi kugonana. Timasunga kukambitsirana kopitirizabe.” Motsimikizirika, ana awo anakhaladi oyera.
Kupanga Achichepere Kukhala “Anzeru Kaamba ka Chipulumutso”
“Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire,” analosera tero mtumwi Paulo. (2 Timoteo 3:13) Miyezo ya makhalidwe abwino mwakutero idzapitirizabe kutsika. Chisembwere cha achichepere ndi mimba zidzapitirizabe kukantha chitaganya.
Makolo aumulungu adzatembenukira ku Baibulo kotero kuti apange ana awo “anzeru kaamba ka chipulumutso.” (2 Timoteo 3:15) Ngati muzindikira kuti inu mwaumwini mufunikira langizo m’Baibulo, dzimveni aufulu kufunsa Mboni za Yehova mwa kulembera ofalitsa a magaziniyi. Iwo adzakhala achimwemwe kukonzekeretsa kaamba ka inu kulandira malangizo oterowo popanda malipiro. Mboni za Yehova zingakupatseninso zofalitsidwa monga ngati bukhu la Your Youth—Getting the Best out of It.a Iri liri ndi chidziŵitso cha m’Malemba chomwe chathandiza zikwi za achichepere kuthaŵa misampha ya makhalidwe oipa a dziko.
Bwanji, ngakhale kuli tero, ponena za atsikana omwe akumana kale ndi tsoka la mimba yopanda lamulo? Mikhalidwe yoteroyo iri kutalitali ndi kukhala yopanda chiyembekezo. Mulungu ‘amakhululukira m’njira yaikulu’ mmodzi amene mowonadi ali wachisoni kaamba ka njira yake ya mkhalidwe. (Yesaya 55:7) Pamene kuli kwakuti kukhala kholo limodzi sikuli kopepuka, wina angapange chipambano cha icho mwa kugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo. Mkazi wachichepere amene anali ndi ana atatu a kunja kwa ukwati asanakhale Mkristu wachita kokha chimenecho. Iye amakalamira kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu m’banja lake. Mwakuyanjana mwathithithi ndi mpingo wa Mboni za Yehova, iye wapeza chitonthozo ndi chirikizo lalikulu. Iye akunena kuti: “Icho ndithudi chiri chokondweretsa kutumikira Mulungu yemwe ali wokhululukira, ndi kukhala ndi abale ndi alongo omwe ali omvetsetsa. Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndimadzimva woyera ndi wathunthu, mwauzimu ndi mwakuthupi.”
Ndithudi, chikakhala chabwino kwambiri kupewa mavuto a kugonana kwa otomerana pa malo oyamba. Mwachimwemwe, zikwi za achichepere lerolino zikuchita chimenecho chifukwa zimatsatira uphungu wa pa nthaŵi yake wa Baibulo.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Mboni za Yehoba zimayesera kuika mwa ana awo chinachake cha chisonkhezero kwambiri kuposa kuwopa AIDS kapena mimba: kuwopa Yehova Mulungu kwa umoyo
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Mogwirizana ndi ziyerekezo zina, pali achichepere oposa mamiliyoni 12 okangalika mwa kugonana mu United States mokha
[Zithunzi patsamba 5]
Makolo angasunge kukambitsirana kopitirizabe ndi ana awo pamene chibwera ku nkhani za kugonana
[Zithunzi patsamba 7]
Achichepere Achikristu adzapewa mkhalidwe womwe ungasakaze unansi wawo ndi Yehova Mulungu