Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwhf nkhani 31
  • Kodi Mungatani Kuti Musamachitirane Nsanje M’banja?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Kuti Musamachitirane Nsanje M’banja?
  • Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi nsanje ndi chiyani?
  • N’chiyani chimachititsa kuti anthu azikayikirana popanda zifukwa zenizeni?
  • Mungatani ngati mukuchita nsanje?
  • Chikondi Chimagonjetsa Nsanje Yoipa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Yosefe Anachitiridwa Nsanje
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Kodi Akristu Ayenera Kukhala Ansanje?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Nsanje ya pa Kulambira Yehova Koyera
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Mfundo Zothandiza Mabanja
ijwhf nkhani 31
Banja lili kuphwando, ndipo mkazi akuyang’ana mwamuna wake mokwiya atamuona akulankhula ndi mkazi wina.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MABANJA

Kodi Mungatani Kuti Musamachitirane Nsanje M’banja?

Banja silingayende bwino ngati mwamuna ndi mkazi wake amakayikirana. Ndiye kodi mungatani kuti musamachitirane nsanje pa zifukwa zosamveka?

Zimene zili munkhaniyi

  • Kodi nsanje ndi chiyani?

  • N’chiyani chimachititsa kuti anthu azikayikirana popanda zifukwa zenizeni?

  • Mungatani ngati mukuchita nsanje?

  • Zomwe mungachite ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wansanje

  • Zomwe mungagwiritse ntchito pokambirana

Kodi nsanje ndi chiyani?

Mawu akuti “nsanje,” ali ndi matanthauzo ambiri. Koma munkhaniyi, tikambirana mmene munthu amamvera mumtima chifukwa choganiza kuti munthu wina akufuna mwamuna kapena mkazi wake, kapenanso ngati akuganiza kuti mwamuna kapena mkazi wake akudyerera maso munthu wina. Zimenezi zikayamba kuchitika, timaona kuti banja lathu lili pangozi. Ngati zimenezi ndi zomwe zikuchitikadi, ndi pomveka kuchita nsanje ndipo si zolakwika kumva choncho. Paja banja ndi anthu awiri. Choncho mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuchita chilichonse chotheka kuti ateteze banja lawo.

Mfundo ya m’Baibulo: “Moti sakhalanso kuti ndi awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:6.

“Nsanje ili ngati chipangizo chokuchenjezani ngati pali chinachake chomwe chingasokoneze banja lanu, n’cholinga choti muchitepo kanthu zisanafike poipa.”—Benjamin.

Ngati munthu wina atamakayikira mwamuna kapena mkazi wake popanda zifukwa zenizeni, imeneyi ingakhale nsanje yosathandiza. Mukakhala ndi chikondi chenicheni mumapewa nsanje ya mtundu umenewu. (1 Akorinto 13:4, 7) Dr. Robert L. Leahy analemba kuti: “Zinthu zomwe anthu amachita chifukwa cha nsanje pomwe alibe umboni uliwonse wogwirika, ndi zimene zingasokoneze mgwirizano womwe akufuna kutetezawo.”a

N’chiyani chimachititsa kuti anthu azikayikirana popanda zifukwa zenizeni?

Munthu akhoza kukhala ndi nsanjeyi ngati mwamuna kapena mkazi wake wakale, ankamuzembera ndi munthu wina. Apo ayi, ngati banja la makolo ake linasokonekera chifukwa choti wina anali wosakhulupirika, ndipo nayenso akuopa kuti zikhoza kuchitikira banja lake.

“Ndili mwana, bambo anga ankawazembera mayi anga. Choncho kuyambira kale zimandivuta kukhulupirira munthu. Zinandisokoneza kwambiri maganizo moti nthawi zina zimafika posokoneza banja lathu.”—Melissa.

Chinanso chomwe chimayambitsa vutoli: Ngati umaopa kuti mwamuna kapena mkazi wako akhoza kukopekanso ndi anthu ena, n’zosavuta kuyamba kukayikira aliyense kuti akhoza kukusokonezera banja. Moti nthawi zina utha kumaganiza kuti ngati atapeza mpata, akhoza kukusiya n’kutengana ndi munthu wina.

“Mwamuna wanga anapemphedwa ndi mnzake kuti akagwirizire ukwati wake monga mnzake wamkwati. Kusonyeza kuti nthawi zina ankafunika kumakavina ndi mnzake wa mkwatibwi. Sizinandisangalatse, mpaka ndinamuletsa.”—Naomi.

Maukwati amachitika m’njira zosiyanasiyana potengera madera. Koma Akhristu amafunika kuyendera mfundo za m’Baibulo. Koma kodi zinalidi zomveka kuti Naomi akanize mwamuna wake kukagwirizira ukwati wa mnzake? Panopa amaona kuti anangochita nsanje pa zifukwa zosamveka. Iye anafotokoza kuti, “Ndinkangoopa. Ndinkaganiza kuti mwamuna wanga amandiyerekezera ndi akazi ena. Koma ndinalibe nazo umboni, zinali za m’mutu mwanga basi.”

Kaya nsanjeyi ibwere pa zifukwa zotani, koma ngati munthu akuchitira nsanje mwamuna kapena mkazi wake popanda zifukwa zomveka, amayamba kukayikira mnzakeyo kapenanso kumuimba mlandu kuti akumuzembera. Pamapeto pake zimatha kusokoneza banja lawo komanso thanzi lawo.

Mfundo ya m’Baibulo: “Nsanje ili ngati khansa.”—Miyambo 14:30, Baibulo la Easy-to-Read Version.

Mungatani ngati mukuchita nsanje?

Muzikhulupirira kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu. M’malo mokhalira kufufuza kuti mupeze ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wosakhulupirika, muziganizira kwambiri zimene amachita kuti muzimukhulupirira.

“Ndimaganizira makhalidwe abwino a mwamuna wanga. Akamamvetsera pomwe anthu akulankhula naye, chimakhala chifukwa choti amawadera nkhawa, osati chifukwa choti ali ndi maganizo olakwika. Ndimafunika kudzikumbutsa kuti ngati banja la makolo anga linali la mavuto, sizikutanthauza kuti banja langanso lizikumana ndi zomwezo.”—Melissa.

Mkazi yemwe uja akumwetulira akuyang’ana chithunzi cha ukwati wake. Patsogolo pake pali Baibulo lotsegula.

Mfundo ya m’Baibulo: “Chikondi . . . chimakhulupirira zinthu zonse.”—1 Akorinto 13:4, 7.

Muzisamala ndi zimene mumaganiza. Dr. Leahy yemwe tamutchula poyamba paja analembanso kuti: “Nthawi zambiri timaona kuti zomwe tikuganiza ndi zoona. Chifukwa choti tikukhulupirira zomwe tikuganizazo, timangoona ngati ndi umboni wa nkhaniyo. Koma kungokhulupirira kuti zinazake ndi zoona sikuchititsa kuti nkhaniyo ikhaledi yoona. Mmene tikumvera mumtima si umboni wokwanira wotsimikizira kuti nkhaniyo ndi yoona.”b

“Kuthamangira kuganiza kuti pakuchitika zinazake zolakwika tikangoona zinthu zimene zatikayikitsa, kutha kuyambitsa mavuto m’banja lathu.”—Nadine

Mfundo ya m’Baibulo: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.”—Afilipi 4:5

Kambiranani zimene zikukudetsani nkhawa. Kaya mukuchita nsanje pa zifukwa zotani, fotokozerani mwamuna kapena mkazi wanu nkhawa imene muli nayo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mukambirane mmene muzichitira zinthu, kuti aliyense azikhala womasuka komanso kuti asamadere nkhawa chilichonse. Ndiponso onetsetsani kuti zimene mwagwirizanazo zisakuchititseni kuti muzichita zinthu mopanikizika.

“Muzikambirana nkhanizi muli ndi maganizo akuti mnzanuyo alibe cholinga chilichonse chofuna kukupweteketsani mtima ndiponso kuti nayenso akufuna kuchita zoyenera. Muziona kuti mnzanuyo ali ndi zolinga zabwino. Mwina inuyo mumakhumudwa msanga kapenanso kuyembekezera kuti azichita zinazake zomwe sangakwanitse. Mwinanso n’kutheka kuti mwamuna kapena mkazi wanuyo sadziwa n’komwe kuti mumayembekezera kuti azikuchitirani zinazake.”—Ciara

Mwamuna ndi mkazi wake akucheza panja. Mkazi akufotokozera mwamuna wake zomwe zikumudetsa nkhawa.

Mfundo ya m’Baibulo: “Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.”—1 Akorinto 10:24.

a b Kuchokera m’buku lakuti The Jealousy Cure.

Ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wansanje

Musathamangire kuganiza kuti mnzanuyo alibe zifukwa zomveka zokuchitirani nsanje. M’malomwake, yesani kuona zomwe zikumuchititsa kumva choncho. Baibulo limalangiza amuna kuti azikhala ndi akazi awo “mowamvetsa.” (1 Petro 3:7, Baibulo la The Word—New Century Version). Mfundoyi ikukhudzanso akazi. Ndipo kuona zinthu mwanjira imeneyi kungakhale kothandiza kwambiri makamaka ngati mnzanuyo anakhumudwitsidwapo ndi mwamuna kapena mkazi wake wakale, ndipo nthawi zina amaopa kuti mukhoza kumuthawa.

Inunso muyenera kukhala osamala ndi mmene mumachitira zinthu. Kodi machezedwe anu sakhala okayikitsa mukamacheza pamasom’pamaso kapena pa zipangizo zamakono ndi amuna kapena akazi ena? Kapena kodi mumalankhula kapena kuchita zinthu zokopana nawo? Kodi mwamuna kapena mkazi wanu angamve bwanji ataona mmene mumachitira? Muzionetsetsa kuti simukuchita chilichonse chomwe chikhoza kuchititsa mnzanuyo kuti azikukayikirani.

Zomwe mungagwiritse ntchito pokambirana

Ngati mwayamba kuchitirana nsanje m’banja mwanu popanda zifukwa zenizeni, mwina panokha mungadzifunse mafunso ali m’munsiwa. Kenako pa nthawi ina yabwino, mungakambirane mayankho ake ndi mwamuna kapena mkazi wanuyo. Komabe kumbukirani kukhala ‘wokonzeka kumvetsera komanso kuganiza kaye musanalankhule.’—Yakobo 1:19.

  • Ndi zinthu zotani zomwe zimakuchititsani nsanje?

  • Kodi mumaona kuti zochita za mnzanuyo ndi zomwe zimakuchititsani kukhala ndi nsanje? Ngati ndi choncho, amatani?

  • Kodi pali zinthu zinanso, mwachitsanzo zomwe mwamuna kapena mkazi wanu wakale anakuchitirani, zomwe zikukuchititsani nsanje?

  • Kodi vuto ndi zomwe mnzanuyo amachita akakhala pa foni, pa kompyuta kapenanso mmene amachezera ndi anthu ena pa intaneti?

  • Kodi mungakonde kuti mwamuna kapena mkazi wanu asinthe zinthu ziti?

  • Mungasonyeze bwanji kuti mumakonda mwamuna kapena mkazi wanu komanso kuti ndinu wokhulupirika?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena