Ndandanda ya Mlungu wa May 18
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 18
Nyimbo Na. 105 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 13 ndime 1-10 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 9-12 (8 min.)
Na. 1: 2 Samueli 10:13–11:4 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Tizilemekeza Akulu Mumpingo—bt tsa. 98-99 ndime 17-20 (5 min.)
Na. 3: Kodi Akufa Adzakhalanso ndi Moyo?—igw tsa. 19 ndime 1-3 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Muzithandiza anthu onse kudziwa choonadi molondola.—1 Tim. 2:3, 4.
10 min: Kodi Paulo Anathandiza Bwanji Agiriki Kudziwa Choonadi Molondola? Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 17:22-31. Kenako kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki.
20 min: Yehova Akuthandiza Kuti Ukhale Wolimba Mtima. Nkhani yokambirana. Ikani vidiyo yakuti, Yehova Akuthandiza Kuti Ukhale Wolimba Mtima. (Vidiyoyi ikupezeka pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA.) Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzira m’vidiyoyi. Pemphaninso ana omwe amapita kusukulu kuti afotokoze mmene vidiyoyi ingawathandizire kuti azikhala olimba mtima akamalalikira anzawo a kusukulu komanso aphunzitsi. Konzani zoti mwana mmodzi achite chitsanzo chosonyeza zosangalatsa zomwe zinachitika pamene ankalalikira kusukulu. Ngati n’zosatheka kuonera vidiyoyi, kambiranani nkhaniyi pogwiritsa ntchito lemba la 2 Mafumu 5:1-19. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzira pamavesi amenewa. Pemphaninso ana omwe amapita kusukulu kuti afotokoze mmene nkhaniyi ingawathandizire kuti azilalikira anzawo a kusukulu komanso aphunzitsi molimba mtima. Konzani zoti mwana mmodzi achite chitsanzo chosonyeza zosangalatsa zomwe zinachitika pamene ankalalikira kusukulu.
Nyimbo Na. 60 ndi Pemphero