Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/14 tsamba 3
  • Ndandanda ya Mlungu wa November 24

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Mlungu wa November 24
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Timitu
  • MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 24
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 11/14 tsamba 3

Ndandanda ya Mlungu wa November 24

MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 24

Nyimbo Na. 104 ndi Pemphero

Phunziro la Baibulo la Mpingo:

cl mutu 4 ndime 19-23 ndi tsamba 45 (Mph. 30)

Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:

Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 28–31 (Mph. 10)

Na. 1: Deuteronomo 30:15–20 ndi 31:1–8 (Osapitirira mph. 4)

Na. 2: Nyama Zili Ndi Moyo—rs tsa. 295 ndime 6–tsa. 296 ndime 5 (Mph. 5)

Na. 3: Kodi Mkhristu Ayenera Kulandira Mankhwala Opangidwa Kuchokera ku Tizigawo Tamagazi?—lv tsa. 215-217 (Mph. 5)

Msonkhano wa Utumiki:

Nyimbo Na. 47

Mph. 10: “Muzigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu mu Utumiki​—‘Kuyankha Mafunso a M’Baibulo.’” Nkhani yokambirana. Tchulani mafunso ena omwe ayankhidwa pa mbali imeneyi ya webusaiti yathu. (Pitani pa jw.org/ny ndipo yang’anani pomwe palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA › KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.) Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akugwiritsa ntchito njira imodzi pa njira zomwe zili m’nkhaniyi. Kenako pemphani omvera kuti afotokoze njira zina zomwe angagwiritsire ntchito mbali yakuti, “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” mu utumiki. Ngati kudera lanulo anthu alibe mwayi wogwiritsa ntchito Intaneti, kambiranani mmene tingalalikirire mogwira mtima pogwiritsa ntchito mfundo zomwe zafotokozedwa m’buku la Kukambitsirana, patsamba 9 mpaka 15.

Mph. 10: “Ndikapita Sindiwapeza.” Nkhani yokambirana. Kambiranani chifukwa chake tiyenera kuyesetsabe kuthandiza munthu wachidwi yemwe sapezeka pakhomo.—Mat. 28:19, 20; Maliko 4:14, 15; 1 Akor. 3:6.

Mph. 10: “Buku Lothandiza Kufufuza Nkhani.” Nkhani. Fotokozaninso malangizo omwe ali pansi pa kamutu kakuti, “Mmene Mungagwiritsire Ntchito Bukuli Pofufuza” pa mawu oyamba mu Buku Lofufuzira Nkhani. Tchulani zinthu zosiyanasiyana zomwe zili m’buku limeneli. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akulankhula yekha, akugwiritsa ntchito bukuli.

Nyimbo Na. 69 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena