Ndandanda ya Mlungu wa November 3
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 3
Nyimbo Na. 112 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 3 ndime 19-21, ndi bokosi patsamba 34 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 14-18 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 15:16-23 ndi 16:1-8 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Chifukwa Chake Tiyenera Kuzindikira Kuti Tchimo N’loopsa—rs tsa. 359 ndime 2-tsa. 360 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndi Zifukwa Ziti za M’Malemba Zimene Zimachititsa Anthu Kusudzulana?*—lv tsa. 219-220 ndime 1 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Thandizani Ana Anu Kuti Azikonzekera Utumiki. Nkhani yokambirana yochokera pa Mateyu 21:15, 16. Funsani ana mafunso awiri awa: Kodi ndi angati amene ali ndi chikwama cha mu utumiki? Ndi zinthu ziti zimene ayenera kutenga m’chikwama chawocho akamapita mu utumiki? Kenako funsani makolo kuti, Kodi angathandize bwanji ana awo kukonzekera asanalowe mu utumiki? Pomaliza chitani chitsanzo chosonyeza mwana akugawira magazini.
Mph. 10: Zimene Ena Achita Kuti Azilalikira Modzipereka. Mkulu afunse ofalitsa awiri kapena atatu omwe asintha zinthu zina n’cholinga choti achite upainiya kapena awonjezere nthawi imene amathera mu utumiki. Pomaliza, fotokozani zimene mpingo wakonza zokhudza misonkhano yokonzekera utumiki. Kenako alimbikitseni kuti achite zonse zimene angathe kuti azilowa mu utumiki nthawi zonse.
Mph. 10: Kodi Zakuthandizani Bwanji? Nkhani yokambirana yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene nkhani zakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki” zawathandizira. Pomaliza limbikitsani ofalitsa kuti apitirize kulalikira modzipereka potsatira malangizo amene ali m’nkhanizi.
Nyimbo Na. 100 ndi Pemphero