Ndandanda ya Mlungu wa July 21
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 21
Nyimbo Na. 62 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 14 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 25-27 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 26:1-17 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Anthu Onse Potsirizira Pake Adzapulumutsidwa?—rs tsa. 95 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Mmene Malemba Amasiyanitsira Ngozi Yeniyeni Ndi Zinthu Zadala—lv tsa. 84 ndime 23-25 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Amatilemekeza Chifukwa cha Khalidwe Lathu Labwino Komanso Chifukwa Chosalowerera Ndale. Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2014, tsamba 120 ndi 149. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Mph. 10: Kodi Mungadzachite Upainiya Wothandiza mu August? Nkhani. Funsani ofalitsa awiri kapena atatu amene akonza zodzachita upainiya m’mwezi wa August ngakhale kuti amadwaladwala kapena amatanganidwa. Kodi adzatani kuti akwanitse kuchita upainiya? Funsani woyang’anira utumiki kuti anene zokhudza misonkhano yokonzekera utumiki m’mwezi wa August.
Mph. 10: “Kodi Yehova Amandiona Kuti Ndine Munthu Wotani?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 65 ndi Pemphero