Ndandanda ya Mlungu wa May 26
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 26
Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 12 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ekisodo 34-37 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 34:1-16 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Chifukwa Chimene Malamulo Onse Amakhalidwe Abwino Sanachotsedwe Pamene Malamulo Khumi Anachotsedwa—rs tsa. 349 ndime 1-2 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzitsa Chikumbumtima Chathu?—lv tsa. 17-19 ndime 8-11 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pamene ankayambitsa maphunziro a Baibulo Loweruka loyambirira la mwezi uno. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 4, chitani chitsanzo chachidule cha mmene tingayambitsire maphunziro. Limbikitsani onse kuti adzayambitse nawo maphunziro a Baibulo.
Mph. 10: Kupirira Pozunzidwa Kumakhala Ndi Zotsatira Zabwino. (Luka 21:12, 13) Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2013 tsamba 124 ndime 1 komanso tsamba 128 ndime 1-2. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu. Pemphani ofalitsa, koma osati ana, kuti afotokoze mmene anapindulira chifukwa chophunzitsidwa mfundo zozama za m’Baibulo ndi makolo awo.
Nyimbo Na. 88 ndi Pemphero