Ndandanda ya Mlungu wa May 12
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 12
Nyimbo Na. 69 ndi Pemphero
jr mutu 11 ndime 9-14 (Mph. 30)
Kuwerenga Baibulo: Ekisodo 27-29 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 29:19-30 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Yesu Sanagawe Chilamulo cha Mose Kukhala ndi Mbali ya “Mwambo” ndi ya “Makhalidwe Abwino”—rs tsa. 347 ndime 3–tsa. 348 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingatani Kuti Tisiye Kugwirizana ndi Mizimu Yoipa?—bh tsa. 103-104 ndime 14-16 (Mph. 5)
Mph. 15: Mitundu Yonse Idzakhamukira Kumeneko. (Yes. 2:2) Funsani ofalitsa awiri. Mmodzi akhale woti wakhala m’choonadi kwa zaka zambiri ndipo wina akhale woti wangobatizidwa chakumene. Kodi n’chiyani chinawapangitsa kuti aphunzire choonadi? Ndi mavuto ati amene anakumana nawo? Nanga n’chiyani chinawachititsa chidwi pa nthawi yoyamba imene anafika pamisonkhano ya mpingo? Ndi zinthu ziti zimene amakumbukirabe zomwe zinachitika pa tsiku loyamba limene analowa mu utumiki? Kodi abale ndi alongo anawathandiza bwanji kuti apitirizebe kukula mwauzimu?
Mph. 15: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzikonzekera Mawu Oyamba.” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo cha mbali ziwiri. Mbali yoyamba isonyeze munthu akunena mawu oyamba osonyeza kuti sanakonzekere. Mbali yachiwiri ikhale ndi mawu oyamba osonyeza kuti anakonzekera. Ngati nthawi ilipo, fotokozani mfundo zothandiza pa nkhaniyi zimene zili m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 215 mpaka 219.
Nyimbo Na. 117 ndi Pemphero