Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu December: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mungagawirenso timapepala iti: Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?, Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?, Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi? ndi kakuti Kodi Baibulo Mumalikhulupirira? January ndi February 2014: Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, Mverani Mulungu ndi Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. March: Magazini a Nsanja ya Olonda komanso Galamukani!
Tikupempha akulu onse kuti azitumiza mwamsanga malipoti a utumiki wakumunda ku ofesi ya nthambi akangolandira uthenga wapafoni kapena kalata yowakumbutsa zimenezi. Tikuyamikira ntchito imene mumachita posonkhanitsa malipoti komanso kuwatumiza mwachangu ku ofesi ya nthambi.