Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/13 tsamba 7
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 12/13 tsamba 7

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 30, 2013. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.

1. N’chiyani chingatithandize kukhala ofatsa kwa olamulira? (Tito 3:2) [Nov. 4, w03 4/1 tsa. 25 ndime 18-19]

2. Kodi tingaphunzire chiyani pa mawu amene Paulo anauza Filimoni opezeka pa Filimoni 4, 5 ndi 7? [Nov. 4, w08 10/15 tsa. 31 ndime 2, 3; w92 4/15 tsa. 25 ndime 3]

3. Kodi tingalowe bwanji mu mpumulo wa Mulungu? (Aheb. 4:9-11) [Nov. 11, w11 7/15 tsa. 28 ndime 16, 17]

4. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Samueli ndi oweruza okhulupirika komanso aneneri omwe “anachita chilungamo”? (Aheb. 11:32, 33) [Nov. 18, w11 1/1 tsa. 25 ndime 5, 6]

5. N’chifukwa chiyani Yakobo analemba kuti “nzeru yochokera kumwamba, choyamba ndi yoyera, kenako yamtendere”? (Yak. 3:17) [Nov. 25, w11 8/15 tsa. 30-31 ndime 15]

6. Kodi “uthenga wabwino unalengezedwa” kwa “akufa” ati? (1 Pet. 4:6) [Dec. 2, w08 11/15 tsa. 21 ndime 8]

7. Kodi lamulo “lakale” ndiponso lamulo “latsopano” limene Yohane ankanena pa 1 Yoh. 2:7, 8, n’chiyani? [Dec. 9, w08 12/15 tsa. 27 ndime 6]

8. Kodi dzina lakuti “Alefa ndi Omega” komanso lakuti “Woyamba ndi Wotsiriza” ndi landani? (Chiv. 1:8, 17) [Dec. 16, w09 1/15 tsa. 30 ndime 6]

9. Kodi Akhristu odzozedwa adzaikidwa “chidindo” m’njira ziwiri ziti? (Chiv. 7:3) [Dec. 23, w07 1/1 tsa. 31 ndime 1]

10. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso amene Mulungu anatilonjeza mu Ufumu wake ndipo kodi kudziwa zimenezi kuyenera kutikhudza bwanji? (Chiv. 21:5, 6) [Dec. 30, re tsa. 304 ndime 9]

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena